DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
BWAILA SECONDARY SCHOOL
2024/2025 END OF TERM I FORM 2 EXAMINATIONS
CHICHEWA
PEPALA LACHIWIRI (Malikisi 50)
December, 2024 NTHAWI: 1 hours 30
minutes
MALANGIZO
1) Lembani dzina, kalasi ndi shifiti Nambala Chongani funso Osalemba
chanu pamwamba pa pepalali ya funso lomwe mu danga ili
mwayankha
2) Pepalali lili ndi magawo atatu
1
(A, B ndi C). Yankhani
2
mafunso onse omwe 3
aperekedwa m’magawowa 4
3) Onetsetsani kuti pepalali lili ndi TOTAL
masamba oyenera.
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
GAWO A (MALIKISI 20)
KUMVETSA NKHANI
1) Werengani nkhani ili m’musiyi ndipo muyankhe mafunso otsatirawo
KUSAMALIRA NSOMBA
Ndikoyenera kusamalira zinthu zachilengedwe. Chitsanzo chimodzi cha
zachilengdwe ndi nsomba. Izo zimathandiza m’njira zosiyanasiyana m’moyo
wathu wa tsiku ndi tsiku.
Tiyenera kusamalira nsomba potsatira malamulo omwe boma lidakhazikitsa. Ilo
lidakhazikitsa malamulo poona kuti anthu ena amawononga nsomba chifukwa cha
umphawi. Iwowa amapha nsomba mosatsatira malamulo kuti akagulitsa apeze
ndalama zowathandizira pa zosowa zawo. Palinso ena omwe amapha nsomba
mosatsatira malamulo kuti apeze ndiwo. Boma lidawonanso kuti mchitidwe opha
nsomba motero ndiwosasamala ndipo ndioononga nsombazoi.
Nkofunika kusamalira nsomba makamaka zazing’onozing’ono. Anthu amene
amapha nsomba zazing’onozing’ono sazindikira kuti kuteroko ndikuwonponga
mtundu wa nsombazo. Pofuna kuthetsa mchitidwe wa umbuliwu boma limakhala
ndi njira zosiyanasiyana zothetsera pa miyezi ina.
Thawi zina boma limalamula kuti pasawoneke nsodzi wopha nsomba m’nyanja
pogwiritsa ntchito maukonde a maso ang’onoang’ono. Boma limachita izi
chifukwa chakuti maukonde a maso ang’onoang’ono amapangitsa kuti nsomba
zazing’onozing’ono zisatuluke m’maukondewo. Pofuna kuteteze moyo wa
nsombazi boma limakakamiza asodzi kuti azigwiritsa ntchito maukonde a maso
aakulu. Boma likalamula motere limapereka mwayi kwa nsomba zing’onozing’ono
kuti zikule ndiponso zidzaswane pofuna kuti mtundu wa nsomba usathe.
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
Mafunso
1) Tchulani chitsanzo chimodzi cha zinthu za chilengedwe.
________________________________________________________ (Malaikisi
1)
1) Perekani chifukwa chimene boma limakhazikitsira malamulo ophera nsomba.
__________________________________________________________________
_________________________________________________________ (malikisi 2)
2) Tchulani zifukwa ziwiri zomwe anthu amaphera nsomba mosatsatira
malamulo?
__________________________________________________________________
_________________________________________________________ (malikisi 2)
3) Fotokozani ubwino woteteza nsomba zazing’onozing’ono.
__________________________________________________________________
_________________________________________________________ (malikisi 2)
4) Kupha nsomba motsatira malamulo kuli ndi ubwino wake. Tsimikizani yankho
lanu pa mfundoyi.
__________________________________________________________________
__________________________________________________________________
_________________________________________________________ (malikisi 2)
5) Pezani mawu ofanana m’matanthauzo ndi mawu awa kuchokera mu’nkhaniyi.
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
a) Umiriza: ____________________________________________ (malikisi 2)
b) Zidzaberekane: _______________________________________ (malikisi 2)
c) Tchinjiriza: __________________________________________ (malikisi 2)
6) Fotokozani zinthu ziwiri zomwe anthu amachita pofuna kupeza ndalama
pamoyo watsiku ndi tsiku.
________________________________________________________________
________________________________________________________________
________________________________________________________________
______________________________________________________ (malikisi 4)
7) Pezani mutu woyenera wankhaniyi.
__________________________________________________________________
________________________________________________________ (malikisi 1)
GAWO B (MALIKISI 20)
NKHANI ZAMCHEZO NDI ZOLEMBEDWA
2) Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala kwambiri ndipo muyankhe
mafunso otsatirawo.
Bulu m’chikopa cha Nkhalamu
Kalekale padali munthu yemwe ntchito yake idali yochapa zovala za anthu ndi
kumamulipira. Iyeyu adali ndi bulu wake wofooka ndi wosoana bwino chifukwa
mbuye wakeiyo samamusamala ndi kumupatsa chakudya chokwanira.
Tsiku lina mkuluyu akudziyendera mu nkhalango adapeza nkhalamu yakufa. Iye
powona adati mwayi wake woti atenge chikopacho kuti akaveke bulu wake kuti
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
anthu akamuona azithawa udali womwewo. Iye adaganiza kuti anthu akawona bulu
wakeyo m’chikopa cha nkhalamu azikaganiza kuti ndi chilombo cholusa cha
m’thengo. Pachifukwachi usiku uliwonse buluyo azitha kumakadya zakudya za
m’minda uku anthuwo akuchita mantha kuchipirikitsa kuopa kujiwa.
Ganizo la anthulo lidali loti athamangitse bulu kuti amuphe ndi mipaliro, nthungo
ndi zibonga. Ganizo limeneli lidatheka: Bulu uja adamuveka chikumba cha
nkhalamu ndi kumakadya m’minda kufikira buluyo adayamba kunenepa
ndikukhala wamphamvu. Mwini buluyo m’mawa uliwonse amapita kukamutenga
buluyo ndikukamutsekera mu balani yake. Iye amachita izi anthu asanadzuke.
Koma tsiku lina buluyo atafikapo poti ndi chibulu cha mphamvu, buluyo adamva
kulira kwa bulu wamkazi ndipo iye adatengeka ndi kuyankhira kulirako. Alimi
onse adadzidzimuka kuti siidali nkhalamu koma kuti adangomuzimbayitsa kuti
aziwoneka ngati nkhalamu ali bulu. Nthawi yomweyo anthu onse adatenga
nthungo, mikondo, zikwanje ndi mipaliro ndi kuthamanga kukapha buluyo.
Mafunso
i. Ndimalo awiri ati pomwe nthanoyi inachitikira?
__________________________________________________________________
________________________________________________________ (malikisi 2)
ii. Tchulani ampanga nkhani awiri omwe akupezeka munkhaniyi.
__________________________________________________________________
________________________________________________________ (malikisi 2)
iii. Nchifukwa chiyani bulu wamunthuyu anali ofooka?
__________________________________________________________________
________________________________________________________ (malikisi 2)
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
iv. Kodi nkhaniyi ili mu mphendero yanji?
__________________________________________________________________
________________________________________________________ (malikisi 2)
v. Perekani mfundo ziwiri zopezeka munkhayi.
__________________________________________________________________
________________________________________________________ (malikisi 2)
3) Werengani ndakatulo ili m’musimu ndipo muyankhe mafunso otsatirawo.
Tcherani Khutu ana inu
kuti anga malangizo abwino mumve
Malangizo aphindu olimbikira Sukulu
Kuti pabwino m’tsogolo mudzakhale
Dziwani kuti wakutsina khutu ndi mnasi.
Musakhalekhale ku sukulu ana inu
Kuti mukonze tsogolo labwino
Musamati lero kwazizila sitipita ku sukulu
Mukalimbikira sukulu chuma mudzakhala nacho.
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
Dziwani kuti kwazizira alibe mpani.
Khalani akhama pa ntchito ana inu
Olemera alero mukuwaonawa si chabe ayi
Iwo ankagona mutu uli ku khomo
Ndipo chambiri adachipezadi
Dziwani kuti kutora khobwe ndi m’mawa.
Adalipo anzanu m’mbuyomu ana inu
Pomva kuti khama lipindura ankayesa nkhambakamwa
Sukulu adaithawa, ntchito sadaipezenso
Lero ndi awo akunong’oneza bondo
Ali mbuu kutuwa kuli kusowa sopo
Dziwani kuti mawu aakulu akoma akagonera.
Tsopano yankhani mafunso otsatirawa
a) Kodi nkhaniyi ikuchitikira kuti?
______________________________________________________ (malikisi 1)
b) Kodi akuyankhula m’ndakatuloyi ndi ndani?
___________________________________________________ (malikisi 1)
c) Perekani zipangizo zitatu zimene mlembi wagwiritsa ntchito m’ndakatuloyi.
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
_____________________________________________________________
_____________________________________________________________
___________________________________________________ (malikisi 3)
d) Chamuchititsa woyankhulayu kupereka malangizo n’chiyani?
_____________________________________________________________
____________________________________________________________
(malikisi2)
e) Lembani kamvekedwe kandakatuloyi.
_____________________________________________________________
_____________________________________________________________
(malikisi 2)
f) Perekani phunziro limodzi lopezeka m’ndakatuloyi.
_____________________________________________________________
_____________________________________________________________
(malikisi 1)
GAWO B (MALIKISI 10)
4) Masulirani kandime kankhani kali m’munsika m’chichewa chomveka
bwino.
Every citizen has a right to participate in development of the country.We are
supposed to be patriotic for the country to develop.
__________________________________________________________________
__________________________________________________________________
__________________________________________________________________
__________________________________________________________________
________________________________________________________ (malikisi 5)
DZINA: __________________________________________ KALASI: _________ SHIFT:
_______
5) Fupikitsani kankhani kali m’munsika kuti kakhale ndi mawu osachepera 10
komanso asapitirire 15.
Tiyenera kuwonetsetsa kuti pamalo ozungulira mijigo pazikhala popanda maenje.
Maenje amatha kumasunga madzi, nasanduka zithaphwi. Sikoyenera kuti pamalo
ozungulira mijigo pazikhara zithaphwi popeza m’menemo ndi momwe
mumaswanirana udzudzu womwe umayambitsa matenda a malungo.