0% found this document useful (0 votes)
184 views99 pages

Nyimbo Za Mulungu

The document is a collection of hymns and praises directed towards God, emphasizing His holiness, power, and mercy. It includes expressions of worship, requests for forgiveness, and a call for divine assistance. The lyrics reflect a deep reverence for the Trinity and a commitment to faith and worship in daily life.

Uploaded by

hildahntamb
Copyright
© © All Rights Reserved
We take content rights seriously. If you suspect this is your content, claim it here.
Available Formats
Download as PDF, TXT or read online on Scribd
0% found this document useful (0 votes)
184 views99 pages

Nyimbo Za Mulungu

The document is a collection of hymns and praises directed towards God, emphasizing His holiness, power, and mercy. It includes expressions of worship, requests for forgiveness, and a call for divine assistance. The lyrics reflect a deep reverence for the Trinity and a commitment to faith and worship in daily life.

Uploaded by

hildahntamb
Copyright
© © All Rights Reserved
We take content rights seriously. If you suspect this is your content, claim it here.
Available Formats
Download as PDF, TXT or read online on Scribd
You are on page 1/ 99

1 Mzimu Nkhoswe yemwe.

1. NDINU wakuyera! Wamphamvu


6. Khristu Mfumuyo yaulemerero!
zonse.
Mwana wosatha wa Atate ndinu!
Nthaŵi ya m’mamaŵayi tiimba
Simunanyoza mimba ya Namwali
nyimboyi.
Potipulumutsa.
Mlengi wachifundo, tikuyamikani,
E! Mlungu Mmodzi mwa Atatuwo.
7. Imfa mutagonjetsa ndi zoŵaŵa.
Njira munatsegula tikaloŵe
2. Ndinu Wakuyera! Anthu ochuluka
Momwe mukhala Inu ndi Atate
Akuimbirani, nakupempharanibe;
Mwaulemerero
Akumwamba omwe nagwadira Inu,
Wachikhalire ndi wosafa ’yi.
8. Kumva milandu yathu mudzabwera
Mutithandize, atumiki anu;
3. Ndinu wakuyera! Ife akuchimwa
Mwatiwombola nawo mwazi wanu:
Zaulemerero zanu sitiona’yi;
Mutipulumutse.
Mwayera nokha, wina saoneka
Wangwiro m’mphamvu ndi
9. Mtiŵerengere m’Mwamba ndi oyera;
m’kuyeramo.
Mutidalitse, ndife anthu anu;
Moyo wosatha, mutipatse tonse,
4. Ndinu wakuyera! Zakumwamba zonse
Mutilamule.
Ndi zapansi zitamabe dzina lanulo;
Mlengi wachifundo, Mphambi,
10. Tsiku ndi Tsiku timalemekeza:
Ambuyathu,
Nanu tikukuzani osaleka;
E! Mlungu Mmodzi mwa Atatuwo.
Mbuye, mtisunge tingachimwe lero;
Mtichitire nsisi.
2
1. INU Mulungu, tikuyamikani; 11. Mbuye, chifundo chanu chitigwere
Tivomereza ndinu Ambuyathu; Monga tikhulupira inu nokha:
Ponse, atate, akugwadirani, Ndakhulupira zedi mwanu, Mbuye
Ndinu wamuyaya! Ndisagome konse!

2. Nanu akukuzani amithenga,


Nanu zam’mwamba ndi zamphamvu
3
1. ATATE wa Kumwambako,
zake,
Munawombola ife ndi
Nanu angelo a mitundu yonse
Chikondi chanu chijacho;
Akuimbirani:
Tiyamikira Inutu.
3. Mbuye Woyera! E, Woyera nokha!
2. Ambuye Yesu Inutu
Mbuye Woyera! Mbuye wa makamu!
Munabadwira anthu ’fe;
Ponse ulemu wanu ndi wodzaza
Munatifera tonsefe;
Pansi ndi Kumwamba.”
Tiyamikira Inutu.
4. Nanu Atumwi akumveka aja,
3. Mzimu Woyera, m’mtimamo
Ndi Aneneri oyanjana omwe,
Tiyeretsedwe ndinutu;
Ndi aunyinji anakuferani
Munatisunga bwinoli;
Akuyamikani.
Tiyamikira Inutu.
5. Mpingo woyera wa kwa anthu onse
4. Atate, Mwana, Mzimunso,
Ukumverani Mfumu ndi Atate,
Ndinu Atatu Mmodzitu,
Mwana woona wa ulemu wonse,

1
Ochimwa tikupemphani:
Mutikhululukire ’fe 6 Zamoyo zili m’thengo zonsezo,
Zodzuma, zina zobangulazo,
4 Zimene ndi kulira konseko:
Aleluya.
1. LEMEKEZA Mulungu ’Tate,
Lemekeza Mulungu Mwana,
7 Inu mumvere anyamatawo,
Lemekeza Mulungu Mzimu,
Okondedwa kuseŵerako,
Mulungu Mmodzi ndi wamkulu,
Mumtima mubvomere monsemo:
Lemekeza, lemekeza
Aleluya.
Mulungu wathu yemweyo.
8 Ndi anamwali obvekedwa mbuu!
2. Mlemekeze, anakonda
Ndi ana osakula msinkhu ’nu
Natitsuka m’mtima mwathu;
Ana a Mulungu mubvomeretu:
Anatiwombola ife
Aleluya.
Tikakhale ndi chifumu.
Lemekeza, lemekeza
9 Akulu nonse ndi mafumu ’nu
Yesu Mbuye Nsembeyo.
Magulu nonse apadzikopa,
Mumlemekeze Mbuye yemweyo:
3. Lemekeza Mfumu yathu,
Aleluya.
Mfumu ya mipingo yonse,
Ipambana anthu onse
10 Ndi amithenga akumwambako,
Akumwamba ndi apansi.
Ndi anthu ndi zamoyo zonsezo,
Lemekeza, lemekeza
Bvomerezani mau omwewo:
Mfumu ya mafumuyo.
Aleluya.

6 7
1 MITAMBO inu yakumwambako
1. TAMANI Ambuye,
Yogunda mvula m’mlengalengamo,
Wamphamvu ndi Iye
Mawu akulu muzinenadi:
Akhala m’ulemu
Aleluya.
Kumwamba komweko:
Chikopa cholimba
2 Paphiri paja papakulupo,
Ndi kothaŵiranso
Pamwala ponse pakuŵala mbuu!
Kwa anthu akewo,
Mumvomereze mawu omwewo:
Kotero ndi Mlungu.
Aleluya.
2. Uzani zamphamvu,
3 Mphepo yay’kulu yakuwombayo,
Imbani chisomo,
Chisanu chija chozizirachi,
Za Mwini ulemu,
Ndi kabvumbulu muzinenadi;
Ambuye wathuyo;
Aleluya.
Powomba chimphepo
Mvulanso ndi bingu
4 Mitengo yaitalitali ’nu
Padziko, pathambo,
Yachiimire mumaimabe,
Akhala ponsepo.
Mubvomereze ndi kunenabe:
Aleluya.
3. Zozizwa za m’dziko,
Za m’mwamba zonsezi,
5 Zam’madzi zonse zakuopsyazo,
Mulungu wamphamvu,
Nyanja, matiti ndi mitsinjeyo,
Munalenga zonse;
Chigumula chakulindimacho,
Muyendetsa mwezi
Aleluya.

2
Nyenyezi ndi dzuŵa: 9
Zolengedwa zonse
1. NDI mitima yokondwera
Zimvera Ambuye.
Mbuye wathu tiyamika.
4. Sitiha ifedi
E, chifundo chake chonse
Kukamba zokoma
Ndi chosatha nthaŵi zonse.
Za Inu Mulungu
Wolera anthuwa;
2. Dzina lake tibukitsa,
Zifika ndi mphepo
Mlungu ndiye yekhayekha.
Ndi mvula ndi dzuŵa,
Zigwera ponsepo
3. Mphamvu yake inalenga
Pa anthu onsewa.
Dziko lonse ndi kumwamba.
5. Wamphamvu yosatha,
4. Anatsogolera kale
Chikondi changwiro,
M’chipululu anthu ake.
Angelo akonda
Kutama Mulungu;
5. Ndi chifundo atipenya
Ndiponso ifetu
Ife anthu osauka.
Ananu tonsefe
Tiyimba nyimboyi
6. Amaŵeta nyama zonse.
Yotama Ambuye.
Zingasoŵe kanthu konse.

8 7. Tiimbire Mlungu wathu


1. TSOPANO linoli Waulemu ndi wamkulu.
Tiimbe nyimbo zathu;
Tiimbe nyimbozi, 8. Tithaŵire kwa Mulungu,
Titame Mlungu wathu; Ndiko tikapeze moyo.
Masiku onsewo
Anatisungadi, 10
Anatipatsanso
1. NDITAMATU Ambuyangayu,
Zabwino zonsezi.
Moyo wanga wonse ndidzamtamatu,
Ndiponso dziko lakumwambako;
2. Mulungu yemweyo
Masiku anga onse ndidzamlemekeza
Akhale m’fupi mwathu;
Iye;
Mtendere wakewo
Sindizaleka konsekonse m’mene ndili
Ukhale m’mtima mwathu;
m’moyotu,
Titsate Iyedi
Padziko pano pena m’Mwambamo.
Ndi nsoni zakezo,
Panjira yakeyi
2. Ndiye wokondwa, E, munthuyo
Masiku onsewo.
Wokhulupirira Mlungu yekhadi,
Wolenga dziko, nyanja, zonsezi;
3. Tilemekezetu
Choona chake chonse chingokhalatu
Atate wakumwamba,
chosatha;
Ndi Yesu Mbuyathu,
Apulumutsa onse namadyetsa anthu
Ndi Mzimu Wakuyera;
akewo,
Mulungu Mmodziyu
Wokonda ndiye Mbuye wathuyo.
Wanthaŵi zonsezo,
Timlemekezetu
3. Mlungu kuona athiratu
Masiku onsewo.
Inde m’maso awo osapenyawo.
Natuma akumvera mpumulo;

3
Amathandiza inde aulendo awo
ofokatu, 4. Nditama mphamvu yake
Akazi amasiye maka ndi anawo Ya Mlungu yondizinga;
onsewo, N’kafoka an’limbitsa,
Olira otonthoza mtimadi. N’kadwala andichiza

4. Nditama Ambuyangayu, Pakundisiya bwenzi


Moyo wanga wonse ndidzamtamatu Mulungu ali paja;
Ndiponso m’dziko lakumwambako; N’kaloŵa imfa ine
Masiku anga onse ndidzamlemekeza Alipo Mlungu wanga.
Iye:
Sindidzaleka konsekonse m’mene 12
ndili m’moyotu,
1. Mtima wanga uyamike
Padziko pano pena m’Mwambamo.
MfumuYakumwambako;
Anandiwombola ine
11 Nanditsuka m’mtimamo
1. Paphiri ndi padambo
Ponsepo pali Mlungu, Ife tonse, ife tonse,
Poyenda ife m’njira Tiyamike Mlunguyo.
Mpoima pali Mlungu;
2. Tiyamike Mulungu wathu,
Kokwera Maganizo, Kaamba ka chifundocho;
Komwe kuli Mlungu, Nthaŵi zonse sasanduka
Kumwamba ndi pansipo Mlungu wathu yemweyo
Ponsepo pali Mlungu.
3. Nthaŵi zonse monga ‘Tate
(Mulungu ali nane!) Atisamaliratu,
(Ali nane, ali nane, ali nane Atisunga m’manja mwake,
Ali nane, Aa! Atipulumutsatu.
Mulungu ali nane!)
4. Anthu a mitundu yonse,
2. Ndi maso Ambuyathu Ndipo a Kumwambako,
Apenyetsetsa ife; Yamikani Mungu wathu,
Amadalitsa onse Ndiye wakukomatu.
Okhulupira Iye;
Anthu onse, anthu onse,
Amamva timbalame, Yamikani Mlunguyo.
Nabveka dziko lonse;
Sataya tizirombo, 13
Asunga zina zonse.
1. YEHOVA ndiye Mbusa wanga,
sin’ngasoŵe konse:
3. Okwaŵa pansi inu,
Andigonetsa pali busa
Oyenda m’madzi inu,
la misipu yonse.
Oyesa dziko nkwanu,
Am’mlengalenga inu,
(Ndiye Mbusa wanga,
Ndiye Mbusa wanga!
Nonsenu ntchito zake
Yehova ndiye Mbusa wanga,
Muona tsiku n’tsiku,
Sin’ngasoŵe konse.)
Saleka kusamala
Ndikudalitsa inu.
2. Kumadzi kuli njiratu

4
andiyendetsa bwino, Aleluya! Kondwerani!
Nalimbikitsa moyo wanga Mlungu wathu yamikani!
ndi chifundo chino.
15
3. Pabande lolunjika
1. MULUNGU ndiye Mbusa wanga,
andilondolera njira;
sindisoŵa konse;
Chifukwacho cha dzina lake
Amandiŵeta nandidyetsa
anandisungira.
nandipatsa zonse.
4. Chigwa choopsacho cha imfa
(Ndiye Mbusa wanga,
ndikachiloŵera,
Ndiye Mbusa wanga!
Ndilibe mantha, muli ndine,
Mulungu ndiye Mbusa wanga,
ndodo ndiigwira.
Sindisoŵa konse)
5. Pamaso pa adaniwo
2. M’mitsinje yamtendere mtima
mwayala gome langa;
wanga aumwetsa;
E, mutu mwaudzoza,
Mapazi omwe m’njira
chisefuka chikho changa.
Yolungama nayendetsa.
6. Zabwino ndi zokoma
3. Za m’mdima, imfa, nkhondo ndi zoipa
zinditsata chitsatire;
sindiopa;
E, m’nyumba ya Yehova
Ndikakhumudwa ndi kutopa,
ndidzakhala chikhalire.
Andipulumutsa.

14 4. Podwala ine pobvutidwa


1. MTIMA wanga lemekeza Andisamalira;
Mlungu wako ndi Chimwemwe. Pondisauts’ adani anga
Nthaŵi zonse ndimtamanda; nandithangatira.
Ndimwimbira nyimbo zanga.
Moyo, mphamvu, nzeru zonse, 5. Chisomo ndi zokoma zake
Zidzamlekeza konse. sizileka konse;
Ndi m’nyumba ya Mulungu
2. Ndi wamwayi munthu uja Ndidzakhala nsiku zonse.
Amthandiza Mbuye wake
Akachita mantha iye 16
Amchotsera nkhaŵa yake,
1. ZOBVUTA zoopsya ndi zosaukazi
Ndipo likamgwera tsoka
Sitingathe ife kuzithaŵa tokha.
Amakhulupira kokha.
Koma Ambuyathu timtamande Iye,
Uthenga Wabwino timveretu kokha.
3. Mbuye ndiye wachifundo,
Achiritsa akudwala;
2. Amadyetsa iye mbalame
Anyamula akufoka
zam’mwamba,
Naŵadyetsatu anjala.
Timtamande ndithu potisunga ife;
Wakusunga mlendo ndiye,
Timvere malembo a m’kalata mwake,
Nathandiza amasiye.
Ambuye yemweyo atisungirabe.
4. Ndiye Mbuye wa ambuye;
3. Abramu kalelo anamvera bwino;
Mphamvu yake ndi yokwana.
Timverenso ngatitu yemwe wakale.
Adzakhala chikhalire,
Pokhala alendo atsogoza iwo,
Mfumu yathu yopambana,
Timkhulupirire Ambuye tonsefe.

5
Lochimwa kalelo,
4. Timtamande Iye ndi moyo wathunso Labweranso ku nkhondoyi,
Pakutsatatsata malembedwe awo. Laposa monsemo.
Tipezamo malembedwe awo.
Tipezamo malo okwanira ife 4. Choposa nalo thupilo
Ambuye wathu atipatsa kwawo. Chikhale momwemu,
Chiyeretsetsa m’katimo,
17 Ndi Mulungu Iyeyu.
1. POKONDWA ndi poona bvuto
5. Anatikondakonda ’Ye,
Ndi tsoka pena mwayi,
Ndi Mlungu Iyeyo,
Ndikumbukira, ndiimbira
Anatifera anthu ’fe
Mulungu wangayo.
Ndi Mulungu Iyenso.
2. Kwezani nane Ambuyathu,
6. Ndi m’munda muja chete, phee!
Timlemekeze yekha;
Pamtanda pati njo!
Popsinja mtima ndinamtchula,
Anaphunzitsa ’bale ’fe
Nandithangata ’ne
Titero ifenso.
3. ANGELO amazinga nyumba
7. Kuuzani Mlungu m’Mwambamo
Za anthu olungama;
Mtamande m’kuyanso;
Mulungu ateteza omwe
Nzozizwa nkhani zakezo,
Amkhulupirira.
Njolimba ntchito njo!
4. Laŵani chikondano chake;
Mudzadziŵitsa msanga 19
Kudala kwawo kwa anake 1. KALELO anthu onse
Omkonda Mbuyeyo. Nachimwa kwa Mulungu
Mulungu anaona
5. Opani iye, nimuleke Naona tchimo lawo,
Kuopa kanthu kena; Nafuna kwawononga,
Mumtumikire mokondwera, Nafuna kwawononga.
Akusungani ’nu.
2. Mulungu anatuma,
6. Mulungu wathu Mmodzi yekha Natuma mvula ija,
Atate, Mwana, Mzimu, Nadzaza dziko lonse
Akhale ndi ulemerero Anafa anthu onse,
Wachikhalirewo! Anafa m’mvula muja,
Anafa m’mvula muja.
18 3. Mulungu anatuma,
1. KUZANI Mlungu m’Mwambamo,
Natuma Nowa uja,
Mtamande m’kuyanso;
Wamanga chombo chake,
Nzozizwa nkhani zakezo,
Ndi chachitalitali,
Njolimba ntchito njo!
Nowayo nayendamo,
Nowayo nayendamo.
2. Pochimwa anthu onsewo
Nja Mlungu nzeruyi;
4. Nowayo anatuma,
Adamu wachiŵiriyo
Natuma chikwangwala,
Wathetsa tchimoli.
Chatsika pansi pansi,
Chosabwerera konse,
3. Thupi la mwazi wathu ’li

6
Chithaŵa m’talitali, Mulungu wathu wabwino,
Chithaŵa m’talitali. Pakuti akondana nawo
Anthu okhala padziko;
5. Kutuma wabwereza, Tero natuma Mwana wake,
Natuma nkhunda ija, Wakukondedwa kalelo,
Yatsika pamadzipo, Kutiphunzitsa ife tonse
Yathyolatu mayani, Za chikondano chakecho.
Yampatsa Nowa yemwe,
Yampatsa Nowa yemwe. 2. Mulungu ndiye wachifundo,
Nadzalandira onsewa
6. Kalelo Mbuye Yesu Akuulula mphulupulu
’Nafera anthu onse, Ndi kukondana ndi Yesu
Ndiyeyo chombo chathu, Tilondelonde njira yake
Tikabisala mommo Yopapatiza yaing’ono;
Tipulumuka mommo, Adzatilondolera ndiye
Tipulumuka mommo. Kutifikitsa m’Mwambamo.

20 3. Pakuwoloka mtsinje wa imfa


Dzanja Mbuyathu agwira;
1. MULUNGU aŵakonda anthu
Tikadagwira ntchito zake
Ali pansi pano;
Atipatsatu korona;
Afuna kuŵapulumutsa
Komwe kulibe masauko,
Kumilandu yawo.
Pena misozi maliro;
Mulungu tidzamtamandira,
A! Chikondi chachikulu
Inde kosalekezanso.
Mulungu ali nacho,
Chimam’tengera Mpulumutsi,
Andifere pano 22
1. NDIKONDA Mlungu pomva
2. Ndikhulupira mwa Ambuye, Mbuye wanga
Mulungu namukitsa, Amva pemphero ndi kulira kwanga,
Imfayo indipulumutsa, Namachereza khutu nditapfuula,
Mwazi und’yeretsa. Andithandiza, nandipulumutsa.

3. Chikondi chake chindidzera 2. Mulungu wanga ndiye wachifundo


M’mtima mwanga muno, Ndi wolungama mtima ndi wabwino;
Chipulumutsa nditalema Apulumutsa anthu akufoka,
Ndi machimo anga. Akathandiza nkhaŵa imachoka.

4. Mukondwe anthu a Mulungu, 3. Mtimanga, bwera kuti upumule,


Tere mulandira Wakuchitiranso zokoma Mbuye,
Chimwemwe chija chakumwamba, Wakuchotsera imfa ndi misozi,
Chidzaloŵa m’mtima. Ndingakhumudwe asungira phazi.

5. Mulungu atipatsa mphamvu 4. Nditani ine kubwezera Mbuye


Yoletsetsa tchimo; Zokoma zonse anandichitira?
Pofika tsikulo la imfa, Chipulumutso chake ndidzatama,
Tidzakhala bwino. Ndinalumbira zija ndidzapatsa.

21 5. Imfa ya anthu ake imkomera,


Aŵalandira m’nyumba zokonzeka.
1. TIIMBE nyimbo zotamanda

7
Mbuye, kapolo wanu ndipereka 3. Angelo kwezani
Nsembeyi yonga yanu, ndine ndekha. Nyimbo zanu zonse,
M’wambamo mumveke zoyamikazo;
23 Lemekezani
Mulungu Wakumwamba.
1. TITAME Mlungu Wakumwamba,
Timwimbire nyimbo,
4. M’dzikomo Ambuye
Kukoma kwake kwatipatsa
Mnabadwira ife,
Zonse tili nazo.
Ulemu wosatha muyeneradi.
Mawu a ’Tate,
(Timwimbire nyimbo,
Munaloŵa m’thupi.
Timwimbire nyimbo!
Kukoma kwake kwatipatsa
Zonse tili nazo) 25
1. NDIKULEMEKEZA
2. Poyamba paja analenga Ambuye Mpulumutsi wanga;
Zonse dziko muno, Moyo ndi mtima wanga
Tsopano lomwe azisunga ndilikukondwa mwa Mulungu.
Zonse zili moyo.
2. Ndiye anayang’ana
3. Tinasokera ngati nkhosa, umphaŵi wa mdzakazi wake;
Moyo tinataya, Onse adzandiyesa
Tinakondwera ndi zoipa ine wodala nsiku zonse.
Zonse tinatsata.
3. Ndiye wamphamvu zonse
4. Komweko titasaukira, anandichitira zazikulu;
Titafuna kufa, Dzina la Ambuyanga
Atate anatilondola lili loyera kopambana.
Naitana ife.
4. Ndiye amachitira
5. Tiyeni tizipita kwathu, chifundo anthu a mibadwo,
Tisasokerenso, E! a mibadwo yonse
Tilape m’mtima kuti yakumuopa ndi kummvera.
tikakhale ndi Mulungu.
5. Iye amazichita
24 zamphamvu nawo mkono wake;
Iye nabalalitsa
1. OONADI mtima,
omwe anyada nadzitama
’Dzani mokondwera,
Tiyeni, tiyeni ku Betlehemu;
6. Iye natsitsa kunsi
Modyera ng’ombe
mafumu ku mipando yawo.
Muli Mfumu yathu.
Iye nakweza konko
omwe afatsa nasauka.
Tiyeni timgwadire
Khristuyo.
7. Ife amakhutitsa
anjala ndi zabwino zake,
2. Mulungu wamkulu
Ndi olemera onse
Wakuyerayera
naŵaingits’ opanda kanthu.
Kubadwa mwamkazi sanakana ’yi;
Mwana wa ’Tate,
8. Monga anapangana
Sanalengedwadi.
ponena kwa makolo athu,

8
Ali kuthandizadi Monga analankhula
lero anake a Yakobo, mwa aneneri ake, kuti

9. Poti akumbukira 3. Adzatipulumutsa


atate wathu Abrahamu; kudzanja la onse akutida,
Inde chifundo chokha Ndipo adzachitira
akuchitira ana ake. akulu chifundo ndi chisoni.

26 4. Ndiye akumbukira
pangani loyera lake lija,
1. AMITHENGA a Mulungu
Ndi chilumbiro chake
Anaimba nyimbo yomwe,
cha kwa atate Abrahamu,
Posonkhana m’mlengalenga,
Natitu usiku womwe;
5. Choti timtumikire
“Onse azilemekeza
osaŵaopa ’dani athu,
Mlungu Wakumwambamwamba;
Ndi kuyeranso mtima
Akhalebe ndi mtendere
mwa chilungamo nsiku zonse.
Anthu ali ponseponse.”
Amithenga anaimba
6. Mwana, adzakuyesa
Ndi usiku m’mlengalenga.
mneneritu wa Wamkulukulu,
Ndiwe udzakonzera
2. Anamva abusa omwe
njira ya Mbuye Wakumwamba.
Anaŵeta nkhosa zawo.
Mthenga nati: “Musaope;
7. Udzadziŵitsa anthu
Mumve ndikufotokoza:
za Mpulumutsi wawo yemwe
Wabadwa usiku uno
Aŵakhululukira
Yesu Kristu Ambuyathu
Nafafaniza tchimo lawo,
Ndiye Mpulumutsi wathu;
Anabadwa m’Betlehemu.”
8. Poti Mulungu wathu
Amithenga anaimba
ali ndi mtima wachifundo.
Ndi usiku m’mlengalenga.
Ndiye kumwamba komwe
Ationetsa mbanda kucha,
3. Yesu ndinu Mbuye wathu,
Munasiya za Kumwamba;
9. Poŵalitsira omwe
Munakhala mwana kuno;
ali mumdima ndi muimfa,
Mnatifera mwaufulu.
Ndi potilunjikitsa
Inu nonse amithenga,
tonse munjira yamtendere.
Inu mumtamande Iye;
Anthu onse ali pansi
Adza akondane naye. 28
Zoonazi amithenga 1. AMBUYE tsopano lino,
Anaimba m’mlengalenga. monga mwa mawu anu aja,
Lolani kapolo wanu
27 ndikachokere mumtendere;
1. AMBUYE ngwodalitsika,
2. Chifukwa chipulumutso
Mulungu wa Israyeli ndiye,
chanu mwandionetsa zedi,
Poti anayang’ana
Chimene munachikonza
naŵawombola anthu ake,
akachione anthu onse;
2. Napulumutsa tonse
3. Ndi nyali yakuŵalitsa
mwapfuko la Davide mwana wake;

9
omwe sadziŵa mawu anu; Ndi zonyoza munafoka,
Ndiwo ulemerero Mnasenzera anthu mkwiyo
wa Israyeli mpingo wanu. Wa Atate, Inu nokha.
Chikho chija ndi choopsa
29 Munamwacho m’phiri lija
M’mene munalola mtanda,
1. M’KATI mwa zobvuta zathu
E! chifundo chanu chinja.
Yesu aitana ife,
Tsiku lonse amanena:
4. Yesu ndinu moyo wathu,
“Tsata Ine mkristu iwe.”
Chuma chathu choposetsa.
E! tikondwerera mtanda,
2. Kale ophunzira ake
Apo moyo munapatsa.
Namvanso kunyanja kwawo,
Mbuye tikondana nanu,
Zinthu zonse anasiya
Yesu Mbuye Mwini zonse;
Kukatsata Mbuye wawo.
Ndi mitima ndi milomo,
Tikuyamikani tonse.
3. Yesu aitana ife;
Tikakonda chuma chokha,
Ati Yesu; “Mwana wanga, 31
Undikondetu koposa.”
1. “SENZANI mtanda wanuwu.”
4. Mwachimwemwe, mwachisoni, Atero Yesu Mbuyathu;
Pogwiritsa ntchito zonse, “Mukanditsata Inetu,
Aitana Mpulumutsi Mudzikanize nokhanu.”
Kuti tizimkonda tonse.
2. “Senzani mtanda wanuwu.”
5. Yesu aitana ife; Musaopsedwe nawotu;
Mbuye, mutimvetse ndithu, Mphamvu za Yesu nzanunso;
Tipereke mtima wathu, Limba mtima wanuwo.
Tikondane lero ndithu.
3. “Senzani mtanda wanuwu.”
30 Bwanji manyazi mumva ’nu?
1. IFE timakufunani Yesu anapiriratu,
Inu wotonthoza mtima. Kuti mupulumuketu.
Yesu, nyimbo zathu zonse
Ziyamika Inu nokha. 4. “Senzani mtanda wanuwu.”
Munasiya zonse m’Mwamba,
Nawo muyende chetetu,
Kudzakhala pansi pano
Kuwombola akapolo, Mutsogoledwe nawonso
Kumasula anthu anu. Kwanu Kumwamba komweko.

2. Yesu, ndi chifundo chanu 5. “Senzani mtanda wanuwu.”


Chachikulu munadzera Tsatani Yesu m’njiramu;
Ife anthu osauka, Iye wakusalemayo
Tsoka lathu mnachotsera. Ndiye alandiridwadi.
Mwazi ndi misozi yanu
Munakhetsa m’munda muja,
Kukonzera ife njira 34
Yonkako Kumwamba kuja. 1. KU Mzinda wakuyerawo
Wapachikidwa Mbuyeyo,
3. Yesu munalaswa m’mtima, Nasautsidwa Mbuyeyo,

10
Akatipulumutsa ’fe. Ambuye wanga ’nafatu;
Pamtandapo, pamtandapo
2. Padzanja lachifundolo Anandiwombolerapo.
Linapenyetsetsa ’khunguwo,
Lachiza nalo nthendazo, 2. Kwa munthu wosokerayo
Papyolatu msomaliwo. Kudziko lakutaliko,
Atero Yesu: “Bweratu
3. Mapazi ake namvatu Ukhale nawo moyowo.”
Zoŵaŵa zopambanazo,
Napachikidwa kaamba ka 3. E! Yesu Mbuye wangadi,
Zoipa zathu zonsezi. Ndipatsa Inu mtimawu;
Ndithandizeni inedi
4. Ambuye, tikondweratu Ndisalekane nanu ’yi.
Kupulumutsa kwanuko;
Satana tisammvere ’yi 4. Zochimwa zanga zonsezo
Komabe Mpulumutsiyo. Wandichotsera mwaziwo;
Mumtima mwanga muli mbee!
35 Mwayeretsedwa indetu.
1. TIYENI, dzalireni nane,
Tidze ku mtanda wa Ambuye, 37
Tionse tichitetu maliro; 1. ZATHEDWA zonsetu
Wapachikidwa Ambuyathu. Za moyo wakewo,
Ambuye anatsikayo
2. Kodi misozi itisoŵa, Nafika pansipa.
Poona anthu amanyoza?
Onani umo apirira; 2. Zintchito zakezi
Wapachikidwa Ambuyathu. Zofuna ’Tatewo
Anatsiriza zonsedi,
3. Anena mawu m’mtanda momwe Sanazisiya ’yi.
Mawu ochepa achifundo,
Apempherera ’dani ake; 3. Pa Iye padzapo
Wapachikidwa Ambuyathu. Chisoni m’mtimamo,
Mpweteko wonse wathuwo
4. Mtima wangawe, uyenera Wa dziko lonseli.
Kuduka ndi manyazi lero,
Zamlasa ndi zoipa zako; 4. Pamutu minga kwe!
Wapachikidwa Ambuyathu. Pamoyo wakewo
Zoipa zathu zonsezo,
5. Ona chikondi cha Mulungu, Zinaikidwapo.
Ona zoipazo za anthu,
Koma chakula ndi chikondi; 5. Anandiferatu ’Ye,
Wapachikidwa Ambuyathu. Afera inedi;
Athetsa nsembe zonsezi
36 Ambuye Nsembeyi.
1. PAMTANDAPO Ambuyeyo
6. Pakugomedwapo
Anatifera ifetu,
Pa mlandu wangawo,
Nakhetsa mwazi wakewo
Ndidzaitana Mbuyeyo
Kutiwombola tonsefe.
Andilanditsepo.
Pamtandapo, pamtandapo

11
38 A! panalibe kalelo
Wondibvalira mingayo.
1. A! MUTU wakuyera,
Wolaswa wachisoni,
4. Chinkana dziko lonselo
Abveka Inu anthu
Lichepa ndithu mtulowo,
Ndi minga ya udani;
Chikondicho chagwirabe
Ambuye mwafokatu
Mtimanga, moyo, ndense ’ne.
Ndi masauko aja,
Mwatuŵa m’maso mwanu
Mumayerera kale. 40
1. LERO Kristu anauka, Aleluya.
2. Ambuye Mwini moyo, Ndilo tsiku lokondwera. Aleluya.
Kokoma mnafumako; Iye kale anafera, Aleluya.
Ndizizwa pomva mawu Nawombola otaika Aleluya.
Umo mwachitiramo.
Chisoni chija chanu 2. Timwimbire zomtamanda Aleluya.
Ncha pamachimo anga, Ndiye Kristu wa Kumwamba
Mwasaukira Inu Aleluya.
Kupalamula kwanga. Natsikira kumanda, Aleluya.
Nalanditsa akuipa. Aleluya
3. Nditani! Bwezi langa
Kulemekeza Inu 3. Koma masauko ake Aleluya.
Chifukwa cha chifundo Anatiwombola ife. Aleluya.
Ndi imfa ija yanu? Ndiye Mfumu ya mafumu Aleluya.
Mundikhalitse wanu, Mwana ndithu wa Mulungu.
Wokhulupira inu; Aleluya.
Musandilole konse 4. Timwimbire Mulungu wathu,
Kufulatira Inu. Aleluya.
Kuti atikonda ndithu: Aleluya.
4. Pakufa ine Mbuye Mtamenso angelo inu, Aleluya.
Mukhaletu pafupi, Ndiye ‘Tate, Mwana, Mzimu
Mundithandize ine, Aleluya.
E, mudzandimasula;
Ndipenyetsetsa Yesu,
Ambuye Mfumu yanga, 41
Ndikafa ndine wanu, 1. NLA Mlungu dzuŵali:
Ndikhale nanu m’Mwamba. Pa mbanda kuchapo
Angelo ‘nadzatu
Nachotsa mwalawo.
39
1. POKUMBUKIRA mtandawo
Ndi mtima wonse mwimbedi,
Ambuye ’nandiferapo,
Wauka Mbuye leroli.
Ndiyesa zingochepazo
Ndinazitama kalelo.
2. Akonda onsewo
‘Nagwidwa manthadi
2. Mndiletse ndisatame’yi
Poona zo’psyazo
Zachabe, koma imfayi;
Zoonekerazi.
Zijazo ndinakondazo
Ndazilekera mwaziwo.
3. Mulibe m’mandamu,
Wadzuka Mbuyetu;
3. Onani m’mutu, m’manjawo
Woposa imfayo
Mudzera nsoni m’mwazimo.

12
Ndi Mwini moyowu. Mfumu yathu yaulemu. Aleluya.

4. Dzukani nayetu, 3. Yesu nkana saoneka, Aleluya


Oyera inunso, Atipempherera komwe: Aleluya.
Lekani m’mandamo M’nyumba yake yokonzeka Aleluya.
Zakufa zanuzo. Atilinda ife tomwe Aleluya.

5. Titama Yesuyo, 4. Tiyamike Dzina lake, Aleluya.


Ambuye m’Mwambamo, Mfumu ya ulemu wonse. Aleluya.
Wofera anthu ’Ye, Tibukitse mbiri yake Aleluya.
Timkondakondako. Pansipa padziko lonse. Aleluya.

42 44
ALELUYA, Aleluya, Aleluya! 1. LAMBIRA, Mfumuyo,
1. Nkhondoyo yatha, imfa yagonja, Ndi Yesu Mbuyathu,
Yesu wamoyo anaiposa, Tamvani nyimbo za ‘mithenga a
Msampha woipa wonse nawonja, Kumwambako;
Aleluya! Nafenso pansipa
Timyamikire ’Yo,
2. Mphamvu za imfa ndi za Satana Ndi Mpulumutsi wathu wotifera
Naye Ambuye zinalimbana, kalelo.
Komatu Yesu anapambana.
Aleluya! 2. Lambira Yesuyo
Wokonda tonsefe;
3. Atha masiku aja ansoni, Mabala ake achikondi aonekabe;
Mbuye wauka, ali ndi mboni; Tisaiwale ’yi
Lero chimwemwe, chatha chisoni, Zoŵaŵa zakezo,
Aleluya! Tileke kumchimwira, kumsautsa
Yesuyo.
4. Nsinga za imfa Iye ’nadula,
Khomo la m’Mwamba, nalitsegula; 3. Lambira Yesuyo,
Yesu timtama tonse tipfuula, Uthenga wakewu
Aleluya! Uyanjanitsa anthu onse m’dziko munomo:
Amaiŵala za
5. Mbuye mabala anu olimba Kudana kwawoko,
Atichotsera mantha a imfa; Nayamikira Mfumu yamtendere
Tsono ndi mtima wonse tiiimba: monsemo.
Aleluya!
4. Lambira Mfumuyo
43 Wolenga zonsezi:
Nyenyezi, dziko, dzuŵa, mwezi ndi
1. KONDWERANI dzuŵa lino,
mitamboyi;
Aleluya.
Tikweze dzinalo
Yesu wanka m’Mwamba momwe:
La Mbuye Yesuyo,
Aleluya.
Timyamikire pansi pano ndi Ku-
Wachokera m’dziko lino, Aleluya.
mwambako.
Wabwerera kwawo komwe. Aleluya.

2. Zomkwezetsa zili m’Mwamba, Aleluya. 45


Zodikira Mbuye wathu; Aleluya. 1. YESU wakukoma mtima,
Mloŵetseni n’kumlambira, Aleluya. Akondadi!

13
Wakuposa mbale ndiye, Mundiperekeze inetu;
Akondadi! Ndine mlendo, Mbuye ‘Nu,
Wina asautsa iwe, Mutsagane nanetu
Pena adzasiya iwe,
Yesu sadzanyenga iwe, 2. Inu mundibisadi
Akondadi! M’mene ndabvutidwamo,
Ngati muli ndinedi
2. Kumdziŵitsa ndiko moyo, Bwino ndidzakhalamo.
Akondadi!
Akhumbira mtima wako, 3. Mbuye, mutsaganebe
Akondadi Mpaka moyo watha zi!
Mwazi wake ngwowombola, Kwanu mundifitseko,
M’chipululu akufuna, Kwanu nsoni zathadi.
M’khola mwake akusunga,
Akondadi! 49
1. E, MOYO wanga’we
3. Akufuna kumdziŵitsa,
Utsitsimuketu;
Akondadi!
Ambuye Yesuyo
Udzimpatsa moyo wako,
Akhala m’Mwambamo.
Akondadi!
Pampandopo
Kodi umachita mantha?
Akhalabe, natchula dzina langali.
Pena umadera nkhaŵa?
Yesu amasangalatsa,
2. Kwa Mlungu m’Mwambamo
Akondadi!
Amapempherako;
Chikondi chakenso
4. Bwenzi ndiye wakufera,
Chikhala chosatha;
Akondadi!
Ndi mwaziwo
Nthaŵi zonse sakusiya,
Akhalatu Wansembe wanga Yesuyo.
Akondadi!
Anthu ena akunyenga,
3. Mabala ajawo
Yesu sadzanyenga iwe,
A m’thupi mwakemo
Zakubvuta adzachotsa,
Amukumbutsanso
Akondadi!
Za ine pansipa;
Zoipazo
5. Akhululukira iwe,
Achotsadi kotero sindingafe ’yi
Akondadi!
Nadzainga mdani wako,
4. Mulungu ali wo-
Akondadi!
khulula mtimatu,
Adzakudalitsa iwe,
Ndilibe mantha ’yi,
Nadzaletsa tsoka lonse,
Andisungiradi;
Nadzakutsogoza kwawo,
Ndibwera kwa
Akondadi!
Atatewo, titayanjana leroli.

48 50
1. MBUYE , mutsaganetu
1. M’KHOLA mwa ng’ombe ku Betlehemu
Nane ndingachimwenso;
Anabadwamo Ambuyangayo;
Nanu ndisungidwedi,
Etu, ndizizwa! natsikirako,
Mwa chikondi chanucho.
Kufuna inetu.
Mbuye Yesu,
Kufuna inetu, kufuna inetu,

14
Etu ndizizwa! Natsikirako 3. Tisaleke kugwirabe
Kufuna inetu. Ntchito ya Mulunguyo,
Tibukitse mbiri yake m’dzikoli,
2. Popachikidwa pa Golgotapo Ndi podzatha moyo wathu
Yesu anandiwombola ine, Ndi zintchito zathuzo,
Etu, ndidziŵa! Nakondetsadi Tidzakondwerera naye komweko.
Nafera inetu.

Nafera inetu, nafera inetu,


53
1. MBUYE Yesu adzabwera,
Etu ndizizwa! Nakondetsadi
Asekere anthu onse;
Nafera inetu.
Mawu awa achimwemwe
Azimveka m’dziko lonse.
3. Mbusa wokoma ndi Mbuyangayo,
Adzabwera, adzabwera;
Nandiitana posokerapo,
E! bwerani Mbuye wathu.
Konse koipa nalondolako
Kubweza inetu.
2. Dziko lino linaona
Masauko a Mbuyathu,
Kubweza inetu, kubweza inetu,
Lidzaonanso ulemu,
Konse koipa nalondolako
M’mene adzabwera Iye.
Kubweza inetu.
Adzabwera, adzabwera;
Timvomera, E! mubwere
4. Uko kumwambako Mbuyangayo
Andikonzera mokhaliramo;
3. Anthu anu amafoka,
Tsiku linalo adzabweranso
Pa ulendo nasokera;
Kutenga inetu.
Ha! Adzaonana nanu
Atabvalanso zoyera.
Kutenga inetu, kutenga inetu,
Mudzabwera, mudzabwera;
Tsiku linalo adzabweranso
Inde Mbuyetu mubwere.
Kutenga inetu.
4. Ndi chiyembekezo ichi
52 Sitikhala chete ife:
1. PAKWITANA Mbuye wanga Tiimbitsa nyimbo zathu
Potsiriza dzikoli, Zakulemekeza Mlungu.
Pakufika tsiku la kuŵalalo, Adzabwera, adzabwera
Posonkhana akumvera, E!! mubwere msanga YESU.
Pakuona Yesuyo,
Ndidzakondwerera naye komweko. 54
1. YANG’ANANI, anthu onse,
Pakwitana Mbuye wanga,
Yesu Mbuye wathuyo:
Pakwitana Mbuye wanga,
Alinkudza ndi ulemu,
Pakwitana Mbuye wanga,
Kuoneka m’Mwambamo.
Ndidzakondwerera naye komweko.
Anthu onse amlambire
2. Potuluka m’manda mwawo
Yesu Mwana wa Mulungu
Anthu ake onsewo,
Alinkudza ndi ulemu
Tidzasanganatu nawo nthaŵiyo.
Wopambana, indetu.
Pakuuka osankhidwa,
Kunka naye Yesuyo,
2. Adzatenga anthu ake
Ndidzakondwerera naye komweko.
Akumvera pansipo
Iwo adzakhala naye

15
M’dziko la Kumwambako. Uzani onse m’Mwambamo,
Uzani onse pansipa,
3. Koma anthu onse omwe Wafera Iye anthuwo.
Anamnyoza pansipo,
Nthaŵi Yesu alinkudza 2. Waleka kronayo,
Adzaopa m’mtimamo. Nasiya ’Tatewo,
Natsika m’Mwambamo,
4. Ife tonse tikumbuke Nalira, nafatu.
Mawu ake onsewo; Zoŵaŵa zake zonsezo
Timuyang’anire Iye, Nazimva, zinaposatu
Yesu Mbuye wathuyo. Kuti tipulumukedi.

55 3. Nadzuka m’mandamo
1. A MULUNGU, Moopsya m’mdimamo,
Munatuma Yesuyo, Nigonja imfayo
Mwana wanu Yekhayo. Ndi mdani waketu;
Nakweradi Kumwambako,
2. Anabadwa, Nakhala Mfumu monsemo,
Anabadwa motere, Ambuye wathu Mlunguyo.
Monga mmphaŵi m’kholamo.
4. Adzadza indetu
3. Anakonda Kudziko linoli;
Anakonda anthuwo, Tidzanka nayeyu
Naŵapulumutsanso. M’ufumu wakedi.
Momwemo tidzampenya ’Ye,
4. Anafera, Momwemo tidzakhala ‘fe
Anafera m’mtandamo, M’kuŵala kwake koti mbee!
Anafera ifenso.
57
5. Anadzuka 1. Yesu, dzina lakukonda,
Anadzuka m’mandamo, Lopambana onse ena,
Anatenga moyowo. Tonse tidzaligwadira
Ndi mitima yochepetsa.
6. Anakwera,
Anakwera m’Mwambamo 2. Yesu, dzina lokondwetsa
Kwa Mulungu ’Tatewo. Akuipa a padziko,
Kale linatidziŵitsa
7. Adzabwera, Mpulumutsi ndiye Yesu.
Adzabwera Iyeyo
Tsiku lomalizalo. 3. Yesu dzina lakufatsa,
Anamutcha ’kali Mwana,
8. Aleluya, M’mene analoŵa kale
Aleluya Yesuyo, M’dziko lino lakudana.
Tizitama dzinalo.
4. Yesu, dzina ndi lomweli
56 La pa dziko lino lonse,
1. IDZANI nonse ’nu Ndi lamphamvu yolanditsa
Okonda Yesuyo; Anthu mu masoka onse.
Libuke Dzinali,
Timtame konseko. 5. Yesu, dzina lakukonda

16
La Mwanayo wa Mulungu,
Ife anthu osauka 3. Akhala mafumu
Tithaŵira nalo kwanu. Kwa Mbuyathuyo,
Anawombola onse
60 Ndi mwaziwo pyu!
1. NDITAME Mlungu m’mtimamo,
4. Akadakhalabe
Wakundifera pansipo,
Osaukako
Nafafaniza tchimolo,
Ngati Yesu sakana-
Nanditengera dipolo
Wombolatuwo.
Wandiwombola inetu
5. Ndi nyimbo yabwino
Pokhetsa nwazi wakewo;
Tidzamtamako,
Timlemekeza Iyetu
Kuti ena pakumva
Wotilipira dipolo.
Amwimbirenso:
2. Ndinasokera kalelo,
“Kwa Iye atikonda
Ndamkana Iye Yesuyo,
Natsuka ’fe mbuu!
Koma ndiimba leroli:
E! kukhale ulemu
Wandiwombola inedi.
Kwa Mbuyathuyu.”
3. M’mtima ndimakondweramo
Popenyetsetsa Yesuyo 63
Pamtanda pake pomwepo, 1. TAMANI mphamvu ya Yesu,
Pakundifera inenso. Angelo agwade;
Tulutsanitu korona,
4. Sizitha ntchito zangazo Mumbveke, mbveke, mbveke,
Kundiyeretsa m’mtimamo; Mbveke Mbuyeyo!
Anandiyesa inetu
Wakulungama Yesuyo. 2. Inu osankhidwa ake,
Owomboledwa ’nu,
5. Tsono mubwere inunso; Tamani Mpulumutsiyo,
Mtetezi wanu ndiyedi. Mumbveke, Mbveke, Mbveke,
Apulumusa onsewo Mbveke Mbuyeyo!
Akumkhulupiriradi.
3. Anthu onse ndi mitundu
62 Pa dziko linotu,
Amlemekeze Mfumuyo.
1. KHAMULO liliko
Mumbveke, mbveke, mbveke,
Kumwambako mbuu!
Mbveke Mbuyeyo!
Pakukhala ndi Yesu
Aimbirako:
4. Tifuna kuti komweko
Tikamgwadire ’Ye;
“Kwa Iye atikonda
Tidzaimba kosaleka:
Natsuka ’fe mbuu!
Mumbveke, mbveke, mbveke,
E! kukhale ulemu
Mbveke Mbuyeyo!
Kwa Mbuyathuyu.”

2. Onsewa ’nachimwa 64
Nadetsedwa bii, 1. MUBWERE Mzimu Wakuyera,
Nthaŵi yino ayera Kuyatsa moto m’mtima mwathu;
Naimbiradi: Ntchito ndi yanu kudzozera

17
Ndi kutininkha mphatsozo. Mundigoneke pachifuwa chake
Cha Yesu kuti ndikakondwepo.
2. Kudzodza kwanu kutipatsa
Chimwemwe, moyo ndi mtendere; 4. Wotsogolera, munditsogolere
Kuŵala kwanu kupenyetsa Kuti n’kafike kwawo kwa Atate,
A m’mdima ndi a m’ndendemo. Nditsate Yesu ndikuyendayenda
M’njira yomweyo anapondamo.
3. Mtima wodetsa mukonzere,
Chisomo chanu chakwanira; 5. Mthandizi ndinu, mndithangate ine
Adani athu muthaŵitse Kupempha bwino izo zindisoŵa.
Kupempha monga Mlungu amafuna
4. Mutidziŵitse ‘Tate wathu, Kulingalira zake zokhazo.
Ndi mwana wake ndinu Mmodzi.
Mnafuma kwa aŵiri onse, 6. Mzimu Woyera, n’dzipereke ndense,
Koma Mulungu Mmodziyo. Mundichitire ntchito yaikulu;
Mtima woyera ndi womvera mpatse,
65 Wodzala ndi chikondi chanucho.
1. MZIMU Woyera, mudze mumitima
mwathumo, 67
Mufike nazo mphamvu zanu zazikuluzo. 1. MPUME pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
Ndi kundidzaza moyo wanuwo,
2. Mufike monga nyali younika m’mti- Kuti ndikonde zomwe mukondanso,
mamo. Ndichite chomwe mumachitanso.
Mutidziŵitse zakuipa zakukhalamo.
2. Mpume pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
3. Mufike monga moto wakuotcha zomwezo. Mpaka mtimanga ukayeretu,
Mutiyeretse ifetu m’mitima mwathumo. Ndipo zokhumba zanga zilingane
Nazo zanuzo zakuyera mbuu!
4. Mufike monga ngati njiŵa yamtenderewo.
Kutitu anthu anu onse akondanetu. 3. Mpume pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
Mpaka ndikhale wanu nokhatu;
5. Mufike monga ngati mphepo Ayeretsedwe makhalidwe anga
yokokomayo, Ndi mphamvu yanu yondisunga nji!
Tikhale tonse nazo mphamvu zanu
zonsezo. 4. Mpume pa inetu, Mpweya wa Mulungu,
Kuti inedi ndisafe ’yitu,
Koma ndikhale nanu m’moyo womwe
66 Wangwiro ndi wa nthaŵi zonsetu.
1. MZIMU Woyera, mudzetu kwa ine
E, ngati mvula m’dziko lakuuma,
Ndikhale munda wanu wakupatsa
68
1. MUBWERE Mzimu Inu
Zipatso zoyenera Mbuyeyo.
Woyera wakufatsa,
Muchotse mdima m’mtima mwathu
2. Mphunzitsi, ndinu mudziŵitse ine
Tikapenye m’maso.
Chikondi chanu chija chachikulu;
Lembani mawu anu pamtimanga,
2. Mtisangalatse m’zonse,
Kuti ndikhumbukire zanuzo.
Ndi wachifundo Inu,
Tiyembekeze kumapazi
3. Wosangalatsa, ine ndikalira
A Mbuyathu Yesu.
Muchotse nsoni, m’mtimamo mudikhe;

18
3. Mtitsitsimutse ife Tiyeretsedwe m’mtimamu;
Kuchotsa nkhaŵa zathu, Mupatse anthu anuwa
Muyatse moto wachikondi Mitulo yanu yonseyo.
Mu mitima yathu.
2. Kudzoza kwa Kumwambako
4. Mtitsutse titachimwa Kutitonthoza m’mtimamo,
kutilapitsa m’mtima, Ndi kutidzutsa m’moyomu,
Mwonetsenso chikondi chokhululukira Tikhale okondanatu.
tchimo.
3. Pankhope pathu mthirepo
5. Kutiyeretsa m’mtima Chisomo chanu chijacho;
Ndi ntchito yanu yokha, Mtendere mutininkhebe,
Kupatsa moyo watsopano Mutiyendetse ponse phee!
M’mene timafoka.
4. Tionetseni tonsetu
6. Mukhale m’kati mwathu, Umodzi wanu wonsemo,
Mutichotsere mantha, Atate, Mwana, Mzimu ’Nu
Tidzayamika ’Tate wathu, Tiimbe Nthaŵi zonsezo:
Mwana wawo ndi ’Nu.
Titamire Nthaŵi zonse
69 ’Tate, Mwana, Mzimu, Nonse.
Amen.
1. IDZANI, Mzimu Inu,
Mundidalitse kuno;
Ndafoka mtima ine 71
Polendo wanga uno; 1. MUBWERE kuno Mzimu ’Nu
Kwambiri ndakhumudwa Chitsime cha chikondicho;
Panjirayo ya moyo; Mudziŵa ndimaliratu,
Mkaleka kutsogola Mukhale m’mtima mwangamo;
Ndiwonongeka pompo. Ndipatsa inu mtimawu,
Masiku onse mkhalemu.
2. Wakunga mwana ine,
Sindidziŵitsa konse; 2. Mukonze mtima wangawu,
Mundilangize Mzimu Muyere ndithu m’katimo;
Panjira yanga yonse; Ndilinda tere, Mzimu ’Nu,
Mundiyendetse bwino Mupatsetu chikondicho;
Ndifike ine ndemwe Lichepa dontho lokhali,
Panjira yolungama, Ndipempha mundidzazedi.
Kudziko lachimwemwe.
3. Ndilira Mzimu leroli,
3. Mundilimbitse m’mtima Mutsimikize Mawuwo;
Pogwira ntchito izi; Ya Mbuye Yesu mphamvuyi,
Ndikapumula pena Ikhale yathu, yanganso;
Mukhale ndithu ndine; Muloŵe m’mtima, mdzazetu
Zolingirira zanga Ndi mphamvu, nzeru, moyowu.
Ziyere zonse m’mtima
Zoipa muzichotse, 73
Sindidzazichitanso. 1. MBUYE, Mawu anu
Atikondweretsa,
70 Atitsogolera,
1. MZIMU Woyera, mudzetu, Salephera konse.

19
Ndikhale mfuludi,
2. Poyesedwa ife Wosamangika,
Atipambanitsa, Mukhale moyo wanga wonsewo.
Natonthoza mtima
Natipulumutsa. 76
1. MBIRI yakalelomwe
3. Tikaona bvuto
Mundisimbiretu
Tikaloŵa m’dima,
Ya Yesu Mbuye yemwe
Kuunika kwake
Anandiferatu.
Kusonyeza njira.
2. Simbani bwinobwino –
Ndilibe nzeru ’yi –
4. Atisangalatsa,
Ndimve tsopano lino
Atilemeretsa
Mbiri ya moyowo.
Poŵerenga mommo
Nawo mtima wonse.
Mbiri yakalelomwe,
Mbiri yakalelomwe,
5. Ndiwo alimbitsa
Mbiri yakalelomwe
Omwe akufooka,
Mundisimbiretu.
Naŵapatsa moyo
Akufuna kufa.
3. Mawu amveke bwino,
Aloŵe m’mtimamo,
6. Mbuye, mtiphunzitse
Ndizindikire tsono
Nzeru zake zonse,
Chipulumutsocho.
Tikayenderane
4. Simbani mobwereza,
N’tiyanjane nanu.
Ndisaiŵale ‘yi
Koma ndisunge bwino
75 Mumtima Mbiriyi.
1. MUNDINYEMERE ’ne
Mkate wamoyo 5. Simbani Mbiri yonse
Monga kunyanja kuja kalelo; Ya Mbuye wangayo;
Ndipyola Mawuwo, Zochimwa zanga ndizo
Ndifuna Inu, Zinapha Yesuyo.
Ndikhumba Inu mwini moyowo. 6. Simbanitu mwachete
Mbiri ya Yesuyi,
2. Mkate wamoyowo Pakubvutidwa ine
Ndinu Ambuye; Inditonthozepo.
Mawu oyera anu n’khumbanso,
Mun’dyetse onsewo 7. Simbani Mbiri yomwe,
Ndikhale moyo, Ndikhulupiredi,
Ndikonde zakuona zanuzo. Kuti pakuyesedwa
Ndipulumukepo.
3. Mtume tsopanoli 8. Inde, pakufa panga
Mzimu Woyera, M’maso mukhale mbee!
Kuti andikonzere m’masomo; Mbiri ya Mbuye wanga
Abvumbulutse zinsinsi za m’Mawu, Mundisimbirebe.
Kuti ndionemo Ambuyeyo.

4. Mndidalitsire ’ne
77
1. Kodi ulikulemedwa
Mawu amoyo,
Ndi zoipazo?
Monga munadalitsa mkatewo;
Idza kuno, ati Yesu,

20
Pumako. Lolani kuti Mzimuyo
Agwire ntchito zakezo.
2. Ndikamzindikira ninji
Mbuye wangayo? 79
Ali ndi mabala m’manja
1. PAKUPEMPHA ife pano,
Mwakemo.
Pakwitana ’Tatewo,
Pakudziŵa tsoka lako,
3. Kodi ali ndi chilemba
Bweratu kwa Mbuyeyo.
M’phumi mwakemo?
E, chilembacho chaminga
Idzatu, idzatu
Chilimo.
Kwa Mbuyathu Yesudi
Idzatu, idzatu,
4. Ndikampeza, ndikamtsata
Iwe bwera leroli.
Ninji pansipa?
Masauko ndi misozi
2. Unachimwachimwa ndithu,
Zilipo.
Wasokera m’talimo
Unachedweranji kudza
5. Ndikamfunafuna Iye,
Pakulinda Yesuyo?
Ndipezenjiko?
Kumaliza kwa chisoni
3. M’dziko lino pansi pano
Chonsecho.
Sungapeze kanthumo
Kokwanitsa mtima wako;
6. Ndikampempha anditenge,
Bweratu kwa Mbuyeyo.
Akataniko?
Ati Yesu, “Idza msanga,
4. Bvumbulutsa zonse zako
Idzatu.”
Zobisika m’mtimamo;
Ayeretse moyo wako
78 Nawo mwazi wakewo.
1. MUSAŴALOLE mawuwo
Apite ngati mphepozi, 80
Musaumitse mtimatu,
1. MIPINGO iyo idzatu,
Polira Yesu Mbuyedi.
Yoyenda mangu pajapo,
Afuma kuti anthuwo?
Idzanitu, idzanitu,
Afika bwanji komweko?
Idzani kwa Ambuyeyo.
Idzanitu, idzanitu
Anena anthu onsewo,
Apulumutse inunso.
“Yesu Sing’anga apitapo.”
Anena anthu onsewo,
2. Musachitenso nthantha ’yi,
“Yesu Sing’anga apitapo”
Mufulumire inutu;
Tsiku labwino nleroli,
2. Azizwa anthu ajawo,
Mulandirenso moyowu.
Nafunsa, “Ndani mlendoyo?
Wanzeru monga Iyeyo
3. Zokondweretsa m’dzikomu
Kulibe wina konseko.”
Nzosakhutitsa m’mtimamu,
Koma za Yesu zonsezo
3. Ndi Yesu yemwe kalelo
Zikwaniritsa inudi.
’Nakhala munthu pansipa;
Anthenda onse nthaŵiyo
4. Sakukanani Yesudi,
Nachira yake mphamvuyo.
E, mukalapa m’mtimamo;

21
4. Afika Yesu leroli, Mupulumuketu.
Chifundo m’mtima mwakemo,
Timfitse msanga kwathuko 5. Chikondi cha Mbuyathu
Akhale nafe ponsepo. Chiposa zonsetu;
Chisomo chake chomwe
5. Timsankhe Yesu Mbuyeyo, Chikondweretsabe;
Timyese Mfumu yathuyo, Ulemu wake wonse
Chifukwa tikamkanatu Umapambanadi;
Tikhala otayikawo. Tiyeni, tikondwere
Popita m’Mwambamo.
Tsopano inu ’dzanitu,
Asanapitirirepo. 84
Tsopano inu ’dzanitu,
1. UTHENGA wa Mulungu
Asanapitirirepo.
Waloŵa m’mtimamu,
Wochotsa zakuipa
82 Zakundidetsazo.
1. AMBUYE wathu Yesu
Akhala Mfumunso; Pakuti anthu akumvera
Zoipa zazikulu Yesu aŵapulumutsa,
Azigonjetsa ’Ye; Ine, aŵapulumutsa, indetu.
Anena mawu ake
Ochotsa zonsezo, 2. Ndidziŵa kuti Yesu
Kalelo nalamula: Anafa kalelo,
Pakhala bata duu! Nafafaniza zonse
Tinazichimwazo.
2. M’ulemerero mwake
Anenanenabe: 3. Satana ndi unyolo
Munkhondo apambana Anandimanga nji!
Ndi mawu akewo. Ambuye Yesu yekha
Akristu akondwera Nandimasuladi.
Poona mphamvuyo
Ya Mbuye wathu Yesu 4. Ambuye muloŵetse
Wotiwombolayo. Mtendere m’mtimamo,
Ndimvetse mawu anu
3. Zobvala zake zonse Masiku onsewo.
Nza mwazi woti pyu!
Pamphumi pake pomwe Akuti anthu akumvera
Korona waketu. Yesu aŵapulumutsa,
Unyolo wa Satana Inde, aŵapulumutsa, indetu.
Umasulidwako;
Kumwamba amithenga 85
Atama Mbuyeyo.
1. OKOMA ndiwo mawu
A Yesu Mbuyeyo,
4. M’kufatsa kwake komwe
Wopatsa ife anthu
Anena nafenso,
Mtendere wakewo.
Tonsefe omangidwa
Kwa ife akumvera
Ndi zakuipazi;
Kulibe mantha ’yi;
Ambuye amanena
Timamva liu lake
Zotichenjezazi:
Lingoti, “Mudze ’nu.”
Ananu, msiye zonse,

22
Inu akutopawo Ndi chimwemwenso
Yesu aitana ’nu; Ndi mikono yake
Mudze kwa Ambuyeyo, Yachikondiyo;
Mudze msangatu. Sankha Iwe msangatu;
Wachedwatu.
2. Mukana Iye bwanji,
Wokoma Bwezilo? 90
Mutsate Yesu yekha,
1. PENYETSETSA Yesu,
E, mpaka imfayo.
Mtima wosauka;
Mwafoka osokera,
Anafera iwe,
Mwadetswa nazozi
Idza, nupumule.
Zoipa mwazichita;
Iye anachotsa
Mumvere Mbuyedi.
Nsoni ndi zoipa;
Penyetsetsa Yesu,
3. Ambuye, musendeze
Ndi kukhulupira.
Pafupi nafedi,
Timvetse Inu msanga,
2. Penyetsetsa Yesu
Poyenda m’dzikoli.
Likatentha dzuŵa;
M’ulendo m’moyo uno
Yachuluka ntchito,
Titsate Inutu;
Mphamvu idzakula.
Kumwamba mutifitse,
Akonzera kwawo
Tidzamve: “Idzani.”
Nyumba zokhalamo;
Penyetsetsa Yesu,
88 Mtsatetu tsopano.
1. YESU ndi wokonda;
Ati “Idzatu, 3. Penyetsetsa Yesu
Yense wakufuna, Pogwirana nawo;
Bwera msangatu.” Nkhondo ikabvuta
Ali wachifundo Tamva Mbuye wako.
Ndi wamphamvunso Achuluka ’dani,
Nthaŵi zonse Yesuyo Iwe ungofoka;
Alindatu. Penyetsetsa Yesu,
Mantha adzachoka.
Yesu akukonda,
Idza msanga ’we, 4. Ndipo pakuloŵa
Adikira iwenso; M’dziko la Kumwamba,
Wachedwatu. Udzapeza komwe
Onse adzatama.
2. Iwe afuna, Mwa zoŵala zija
Inde, kalelo; Za Kumwamba kwawo,
Leronso adika Udzapenya maso
Mbuye wathuyo. Yesu Mbuye wako.
Uza Iye zonse
Za uchimowo; 91
Yesu ati leroli:
1. MALO anachepa,
“Wachedwa ’we.”
Nyumba anammana,
Agona m’modyera,
3. Yesu alindira,
Mutu paudzuwo.
Inde, iwetu;
Anthu sanamtama,
Idza ndi kukhala
Nyimbo panalibe,

23
M’nyumba ya alendo Mawu ake omwewo.
Malo munalibe.
2. Iye anatsika m’Mwamba,
Apempha malo Ambuye; Anachoka kwawo,
E, mlandiretu m’mtimamo, Anafera anthu, nati:
Ungamvetu Kumwambako, “Ndatha zonse zawo.”
“Akusowanso malo.”
3. Mbuye wanga ndilikumva,
2. Wina panalibe Ndikondana nanu;
Kumlandira Iye, Umapuma mzimu wanga,
Wakumsangalatsa, Kwathu ndiko kwanu.
Wamkonda nasowa.
Anthu sanafuna 94
Chuma chosatha,
1. KODI mwalandira Yesu?
Sanamkondweresa,
Iye anakuferani.
Malo unalibe.
Afunitsa inu nonse;
Kodi mumufunanso?
92
1. ATATE,’nu, atate ’nu, Kodi mufunatu Yesu?
Mverani Ambuye. Bvomerani msangatu:
“Inde Yesu ndifunadi,
Khulupirani kuti mukaloŵe Ndinu Mbuye wangatu.”
m’Mwambamo,
Khulupirani kuti mukaloŵe 2. Nthaŵi zonse mufunabe
M’Mwambamo. Zinthuzo za pansi pano;
Koma munyozabe Yesu
2. Amayi ’nu, amayi ’nu Wopachikidwa kalelo.
Tsatani Ambuye.
3. Yesu akuitanani
3. Abale ’nu, abale ’nu, Kwanja kwake kwakukulu;
Kondani Ambuye. ‘Mvani mawu ake lero,
Musachite nthantha ’yi
4. Alongo ’nu, alongo ’nu
Kondani Ambuye. 4. Imfa idzafika msanga;
Ndipo mdzaikidwa m’manda;
5. Abwezi ’nu, abwenzi ’nu, Nthaŵi yomwe simudzamva
Tamani Ambuye. Kutitana kwakeko.

6. Oipa inu nonsetu, 95


Mverani Ambuye.
1. ’MVANI liu lomwe
M’khutu mwakomo,
93 Alikuitana
1. NDICHITENJI kukapeza Mpulumutsiyo:
Moyo? thandizeni!
Ndili wakutopa; Mzimu, “Undipatsetu
Muthandize ine. Mtima wakowo;
Ndinakuferau
Zonse zinathedwadi; Kalekalelo.”
Yesu watha zonsezo;
Sutha ntchito, ungomvera 2. Ati: “Undiuze

24
Nsoni zakozo; 3. Akupeza, akupeza,
Ine ndidzachotsa Tiye tsopanoli;
Zonse zomwezo.” Pano akupeza iwe,
Tiye tsopanoli.
3. Kodi ukafuna
Kupumulatu? 4. Salephera, salephera,
Yesu aitana: Tiye tsopanoli;
“Udze kunoku.” Pano salephera Iye,
Tiye tsopanoli.
4. Tula mtolo wako
Pali mtandapo, 5. Mvera Yesu, mvera Yesu,
Akaunyamula Tiye tsopanoli;
Mpulumutsiyo. Pano mvera Yesu iwe,
Tiye tsopanoli.
96 6. Aleluya, aleluya,
1. YESU ponong’oneza, idzanitu;
Aleluya, Amen;
Mupempherera ife, idzanitu;
Aleluya, Aleluya,
Njabwino nthaŵi yino, idzanitu,
Aleluya, Amen.
Yodziŵa Mpulumutsi, idzanitu.

2. Tulani zoipazo, idzanitu; 98


Yesu adzatha zonse idzanitu; 1. Tadza kukudyaku,
Olema ndi ochimwa, idzanitu; Kwakonzedwatu;
Sakambukira izo, idzanitu. Mkate wamoyodi, idyatu ’we;
Bwera wochimwanso,
3. Imvani mawu ake, idzanitu; Yesu adikatu,
Mudzalandira dalo, idzanitu; Akuitanaku; mvetsatu ’we
Nacho chisomo chake, idzanitu,
Yesu alinda inu, idzanitu. 2. Tadza kumtsinjeku
Wa moyo weni,
4. Mverani Iye ati: Idzanitu Chiza zoŵaŵazo za m’mtimamo;
Tiyeni mudzamwone, idzanitu; Mtsinje wodzalawo,
E! akuitanani, idzanitu; Wokwaniratuwo
Ife tibvomereza, Tibweratu. Yesa sakana ’yi; idzatu ’we.

97 3. M’dzina la Yesuyo
Pemphatu iwe,
1. IWE tiye, iwe tiye,
Iye adzamvatu, dikirapo.
Tiye tsopanoli;
Wamphamvu Mlunguyo,
Pano tiye kuti Yesu,
Ndiye apatsatu,
Tiye tsopanoli.
Dalo labwinolo; idzatu ’we
(Ndaima pano, ndaima pakhomo!
4. Yamba ulendowo
Loŵa, loŵa, loŵa, loŵa!
Wonka Kumwamba;
Ndaima pano, ndaima pakhomo!)
Pano mpoipatu padzikoli;
Komwe tikondwako,
2. Akukonda, akukonda,
Tidzasekeranso;
Tiye tsopanoli:
Tinke Kumwambako; idzatu ’we.
Pano akukonda iwe,
Tiye tsopanoli.
99

25
1. MWAMVA Mawu a Mulungu;
Mukabvomeranjiko? 101
Kodi musandula mtima
1. A! MBUSA wathu amvatu
Ndi kumvera Yesuyo?
Uko kuchipululuko
Zilira nkhosa zakezo,
Bvomerani, Bvomerani
Zili kuthengo kunjako.
Bvomerani msangatu,
Musazengereze ayi,
Bwezatu, bwezatu,
Landirani Yesuyo.
Bwezatu zonse m’moopsyamo;
Bwezatu, bwezatu
2. Munachita nthantha kale,
Bweza zakezo kwa Yesu
Musazengereze ’yi;
Yesu akulindirani,
2. Ndani afuna kunkako
Sadzakana inu ’yi.
Kukazipeza nkhosazo?
Ndani adzathandizako
3. Musaope pokumbuka
Kuti zifunde m’kholamo?
Zakuipa anuzo;
Khulupilirani Yesu,
3. M’tali mutali m’phirimo
Adzachotsa zonsezo
Mvetsa, zilira nkhosazo;
A! Mbusa wathu atitu;
4. Perekani mtima wanu
“Bweza zothodwa m’kholamo.”
Kwa Mulungu wathuyo;
Khulupirirani Yesu,
4. Etu, zilira konseko
Wotifera kalelo.
Zili m’phiri moopsyamo.
Imva, anena Mwiniyo:
100 “Kweye, upeze nkhosazo.”
1. YESU wathu Mbuyeyo
Alandira onsewo 103
Akuipa omwewo,
1. AMBUYE ’naitan ’ne;
Osokera m’talimo.
“Dzapumulire kuno,
Tsamira mutu, mwana ’we
Imba kaŵiri ndi kaŵirinso,
M’chifuwa mwanga muno.”
Yesu Ambuye sakanatu,
Mvetsa Uthenga Wabwinowo,
2. Ndabwera kwa Ambuyeyo;
Wakukchimwa adzatu.
Wolema, wachisoni;
Anandipulumutsako,
2. Idzatu kwa Yesuyo,
Nakondweretsa ine.
Apumitsa inunso,
Inde m’mtima mwanumo
3. Ambuye naitana ’ne;
Ndi mtendere wakewo.
“Ndipatsa anthu madzi,
Wotopa ndi waludzu ’we
3. Walandira inetu
Dzamwere moyo kuno.”
Tsiku lija kalelo,
Wanditsuka ine mbuu
4. Ndabwera kwa Ambuyeyo.
M’mtima mwanga momwemo.
Ndamwera madzi awa;
Laleka ndithu ludzulo,
4. Wandifera Yesuyo
Tsopano moyo wadza
Pansi pano kalelo,
Sindiopa mlanduwo
5. Ambuye naitana ’ne;
Pakubwera Iyeyo.
“La dziko ndine Dzuŵa,

26
Yang’ana Ine, kwacha ’we, (Ali nane, ali nane, ali nane, ali nane,
Wachoka mdima uja.” Aa!
Mulungu ali nane!)
6. Ndayang’anira Mbuyeyo
Ndzapeza Dzuŵa langa 105
Londiyendetsa bwinoli
1. NDI inetu sinditha ’yi
Pa njira yonse yanga.
Kunenako milanduyi
Kupempha zachisonizi;
104 Ndagonjatu Mbuyanga ’Nu.
1. YESU wondikondadi,
Ndithaŵire mwanumo (Aa! Mulungu wanga,
Pakugunda mvulazi. Mundilembe pamphumipo:
Pakubvuta madziwo, Chidzakhala chizindikiro
Cha mpumulo ulinkudza ndi Yesu.)
Yesu mundibise ’ne!
Ikaleka mphepoyo 2. Ndi ine sizitheka ’yi
Tsidya lija chete phee! Kuchoka zakuipazi;
Mundilandire momwemo Ndisambe m’mwazi wanuwo;
Ndagonjatu Mbuyanga ’Nu.
2. Pothaŵira pena ’yi
Ndikhulupirira ’Nu; 3. Ndi ine pondibvutapo
Musasiye inedi, Kugwira nazo m’mtimamo,
Mundigwirizizetu. Mundithandize monsemo;
Ndagonjatu Mbuyanga ’Nu.
Ndinu wothandiza ‘ne
Wolimbitsa mtimawu; 4. Ndi ine ndasaukadi,
Pansi pamapiko phee! Zabwino m’mtima zonsezi
Mundifungatiretu. Mwa Inu ndingapezezi;
Ndagonjatu Mbuyanga ’Nu.
3. Wina sindifuna ’yi,
Zokhutitsa nzanuzo; 5. Ndi ine simufuna ’yi
M’utsetu akugwawo, Ndingatayike m’mdima bii,
Mchizetu odwalawo. Ndimvere mwandiuzazi
Ndagonjatu Mbuyanga ’Nu
Ndine wakuipa bii,
Ndinu wakuyera mbuu! 6. Ndi ine, m’mtima Mwanu mbee!
Ndimadzala tchimoli Mokoma ndingakhalebe,
Wolungama ndinutu. Ndikhale wanu wanudi;
Ndagonjatu Mbuyanga ’Nu.
4. Zindichulukirazi
Nsoni zanu m’mtimamu; 7. Ndi inetu ndidziŵedi
Zindichiza nthendazo, Chikondi chodabwitsachi
Zindiyeretsetsa mbuu! Pansipa ndi Kumwambako;
Ndagonjatu Mbuyanga ’Nu
Pachitsime panupo
Moyo ndimwe ndimwebe; 106
Mubukatu m’mtimamo,
1. NDIKHULUPIRA ’Nu,
Mundilanditsetu ’ne
Mwana wa Mlungutu,
Mbuyangayo;
(Mulungu ali nane!)
Mumve popempha ’ne,

27
Tchimo muchotsebe, Mpulumutsi wanga,
Lero ndikhale ’ne Chifukwa ayeneratu,
Wa Mlunguyo. Wakonza m’mtima mwanga.

2. Mzimu mndipatseko, 110


Wondilimbitsayo
1. NDIKHULUPIRIRA, Yesu,
Mumtimamu.
Inu nokhadi
Munandiferadi;
Mundipulumutsa konse
Ndiyambe leroli
Leroli.
Kukonda Inu ndi
Mtimangawu.
2. Kuti mukhululukira
Tchimo langalo
3. Poyenda m’mdima bii,
Ndi chifundo chachikulu
M’mtimamo nsonizi
Chanucho
Mndigwirepo;
Mdima uchoke zi,
3. Kuti muyeretsa mtima
Msozi ulekedi,
Ndibvomeratu;
Ndisasokere ’yi
Mwazi wanu unditsuka
Kwa Inuko.
M’mtimamu.
4. Moyo ukatha zi,
4. Kuti munditsogolera
Pofika imfadi,
Paulendopo;
Mndisungepo:
Mukwanitsadi zosoŵa
Yesu Mbuyanga ’Nu
Zangazo.
Mantha mthaŵitsetu
Ndifike m’Mwambamo,
5. Kuti mundipatsa mphamvu
E, wanuyu.
Yopambanayo;
Mau mundilonga m’kamwa
107 Mwangamo.
1. CHITSIMECHO cha mwaziwo
Udzera mwa Mbuyanga; 6. Ndikhulupira, Yesu,
Wochimwa ndikasambamo, Mndibvomereko;
Nditaya tchimo langa. Ndine wanu lero, maŵa,
Konseko.
2. Wakuba uja nachiona,
Nangokhulupira, 111
Ambuye namva pempholo,
1. NDASIYA zonse ndi Yesu kalelo,
M’Mwambamo namlandira.
Inde zakuipa zangazo;
Anafera ine m’phirimo:
3. Ambuye, mwazi wanuwo
Pomva Mawu ake n’kondwako;
Siitha mphamvu yake,
Mumachoka m’mtima
E, Mpingo wonsewo
Mwangamo nsonizo,
Wayera m’kati mwake.
Mumachoka m’tima
Mwangamo nsonizo.
4. Chionerere mwaziwo
Wofuma m’bala lanu,
2. Chisoni andichotsera Mbuyeyu,
Sindinaleke ineyo
An’thandiza ine teretu;
Kutama mtima wanu.
Ndikhulupirira Iyeyu
Andisunga m’manja mwakemu;
5. Kumwamba komwe n’dzaimbira
Alimbitsa mtima

28
Wangawu teretu, 2. Kale ndinakana Inu,
Alimbitsa mtima Ndinathaŵatu:
Wangawu teretu. Ndinazengereza, ndati:
“Maŵatu.”
3. Mtima ’we siya ndi Yesu nsonizi,
Usabisa tchimo lakoli 3. Lero mtima ungolema,
Zichuluka mphamvu zakezi, Usaukadi;
Likusunga dzanja lakeli; Wina wakundimasula
Bwera kwa Mbuyathu Ndilibe.
leroli mwana ’we,
Bwera kwa Mbuyathu 4. Mbuye, ndingogonja tere,
leroli mwana’we. Ndibvomerapo;
Mundithyole, mundikonze
112 M’mtimamo.
1. KWA Inu Yesu ndilira,
5. Chifuniro changa, Mbuye,
Wopanda Inu ndidzafa;
Ndiperekachi;
Mupulumutse ined,
Mutsogole, ndidzatsata
Mundilandiretu.
Inudi.
Mundilandiretu,
6. Tere moyo wanga wonse,
Ndiipa m’mtimamo
Mawu, ntchitonso
Kotero mnandiferatu
Zidzakondweretsa Inu
Mundilandiretu.
Zonsezo.
2. Ndifoka ndi zoipazo,
7. E, chimwemwe chachikulu,
Ndidzalatu ndi machimo,
N’taperekadi
Sinditha kuzitayazo;
Mtima wanga, ndimapeza
Mundilandiretu.
Mtendere.
3. Ndayesa kudzikonzadi,
Ndapeza mphamvu ndilibe, 115
Zoipa zakanikadi; 1. MNDILANDIRE ine Mbuye
Mundilandiretu. Yesu wondifera ‘ne;
M’mtima mwanga muzikhala
4. Onani Mbuye ndigonja, Mawu anu okhawa.
Kuyesa kwanga ndaleka;
Chitani Inu mumtima; 2. Ndasokera m’tali ndithu
Mundilandiretu. M’njira zopwetekazo;
Wolemedwa ndingopempha,
5. Muyambe ntchito yanuyi, Mndilandire inetu.
Musalekenso, chitani
Ndidzipereka leroli; 3. Pakukumbukira zanga
Mundilandiretu. Ndili ndi manyazitu;
Ndingogwera pansi, ’Tate,
113 Mlapo wandigwiratu.
1. YESU, mulikundipempha
4. Ndingopatsa Inu Mbuye
Munaterodi;
M’manja mwanu mtimawu,
“Mwana, gonja, ndikupatsa
Moyo, mzimu, zonse zanga,
Chimwemwe.”
Mzilandire Mbuyetu.

29
4. “Kodi mayi wobereka
5. Mukhululukire ine, Mwana wake adzamleka
’Tate mundikondadi; Pena adzamwiŵalira,
Mundisunge nthaŵi zonse Koma ndikukumbukira.
Ndi chikondi chomwechi.
5. “Nthaŵi ilikudza yonse
116 Sindisinthanika konse;
Imfa sindiletsa Ine
1. A CHIKONDI chopambana,
Ndisakondekonde iwe.
E, chinadza ndi Mbuye;
Chinasangalatsa m’Mwamba,
6. “Ine ndidzakuonetsa
Chinaloŵanso mwa ’fe
Zonse zakukondweretsa
Yesu ndinu wachifundo,
Za Kumwamba zanga izo,
Wa chikondi changwiro,
Mwana, sundikonda ine?”
Ee, muloŵetu m’mtimanga,
Mumuyese mwanutu.
7. Ambuyanga, ndalephera,
Mwachisoni ndipemphera
2. ’Dzanitu Wamphamvuyonse,
Mundipatse ine ndithu
Mtilanditse konseko;
Mtima wakukonda Inu.
Musachedwe, thandizeni
Musachoke mwangamu;
Inu nokha timakuza 118
Nditumikirabe; 1. ATI Yesu Mbuyeyo:
Tinyadira chikondicho, “Ofoka ndinutu,
Tichitame konseko. Mudikire, m’pemphedi,
Ndidzapatsa mphamvutu.”
3. Tsirizani ntchito yanu
Yakulenganso ife; Yesu wathadi
Idzakhalatu yangwiro, Za mangaŵatu,
Ndiyo yoyenera ’Nu Inde ndinaipa bii!
Usinthika ’lemu wathu, Watsuka ine mbuu!
Udzakhala momwemo,
Mpakatu Kumwamba komwe 2. Mbuye ndimva leroli
Tidzalemekeza ’Nu. Za mphamvu zanuzi
Zomwe zisandutsadi
117 Mtima wanga woti bii!
1. NDILIKUMVA m’mtima mwanga
3. Ine kanthu ndilibe
Mau ake a MbuyAnga,
Kogula moyowu;
Ati, “Ndakukonda iwe,
Ndingotsuka m’mtimamo
Kodi undikonda Ine?”
M’mwazi wa Ambuye ’Nu
2. Ati; “Mwana, kumbukira
4. M’mene ndifa inedi,
Zonse ndinakuchitira;
Kumwamba mzimuwu
Ndakukonda, ndakufera,
Udzakwera komweko
Ndakufuna posokera.
Kuonana Mbuyeyo.
3. “Ku zoipa zonse zako,
5. Ndipo pakuima phe!
Goli la pakhosi pako,
Pokhala Yesuyo,
Ndi kunthenda zosautsa
Ndidzamama Mlunguyo
Ndine ndakupulumutsa
Kosaleka konseko.

30
119 3. Bwenzi ndinamkomanayo,
Ndapeza mphamvu zanga,
1. LINDIKOMERA dzina la Ambuye
Zakundisunga inemo,
Yesu wanga,
Ndiyende m’njira mwanga.
Lisangalatsa, lichiritsa, lin’chotsera
Zolemera zoti mbee!
mantha.
Zindilimbitsa monse;
Ndalema kuno, komweko
Dzinalo la Yesu,
N’kupuma nthaŵi zonse.
Dzinalo la Yesu1
Lindikomera dzina la Ambuye Yesu
4. Bwenzi ndinamkomanayo
wanga.
Wokoma mtima wake,
Wotsogolera nzeruzo
2. Lichiza mzimu wophwetekwa uka-
Zisunga m’njira mwake.
khale bata,
Palibe wondichotsa ‘ne
Lidyetsa mtima wonse, lipumitsa
Kwa Iye wondikonda;
thupi langa.
Pamoyo, imfa, nayeyo
Ndilipo nthaŵi zonse.
3. Nlokoma dzinalo la Yesu, ndilo
thanthwe langa,
Chikopa changa, linga langa m’mene 122
ndibisala. 1. NDIMKONDE Kristuyo,
Ndimkondebe;
4. Ambuye ndinu Mbusa, Bwenzi, ndi Pemphero langali
Wansembe wanga, Mlandiretu;
Ndi Mfumu, Moyo, Njira yomwe, Ndipempha Inutu,
Inde ndimatama, Ndimkonde Kristuyo,
Ndimkondebe,
5. Tsopano ndibukitsabe chikondi cha- Ndimkondebe.
nu chija,
Pakufa ine Dzina lanu lindili- 2. Ndatsatatsatabe
mbikitsa. Za pansipa;
Ndisiye zonsezi,
121 Nditate ’Nu.
M’mtimanga wonsewu
1. BWENZI ndinamkomanayo
Ndimkonde Kristuyo,
Anandikonda kale;
Ndimkondebe,
Kukonda kwandigwirako,
Ndimkondebe.
M’kukondamo nditsale.
Kumtima kundimangako
3. Chisoni chonsecho
Kosamasuka konse;
Chidzatha phe!
Ambuye ndine wanutu
Angelo anuwo
Kunthaŵi nthaŵi zonse.
Afiketu;
Nawo, ndiimbetu,
2. Bwenzi ndinakomanayo
Ndimkonde Kristuyo,
Anandifera yekha,
Ndimkondebe,
Anandipatsa moyowo,
Ndimkondebe.
Ndatenga ine ndekha.
Zimene ndili nazozi
4. Pakufa pangapo
Nza Yesu mwini zonse,
Ndinenebe;
Ndi moyo wanga wonse ndi
Myamiko wangawu
Wakenso nthaŵi zonse.

31
Ndikwezebe, Mnayamba kukonda;
Ndidzapempheradi, Mnafera pamtengo,
Ndimkonde Kristuyo, Munandiwombola.
Ndimkondebe, Mukhululukira
Ndimkondebe. Zoipa zanga zonse;
Ndikonda tsopano
123 Koposa kale lonse.
1. MWAKHULUPIRIRADI
3. Ndidzakukondani
Yesu Ambuyathu;
Mwa moyo ndi m’imfa;
Muli nazo zakezo,
Ndidzakutamani;
Zidzatu zinanso.
Chikondi n’dzaimba.
Mlungu wachisomocho
Mpakatu ndidzafa,
Mbuye wathu ndiye,
N’dzanena nthaŵi zonse;
Ati zinthu zonsezo
“Ndikonda tsopano
Nzathu mwa Iyeyo.
Koposa kale lonse.”
(Zina ndi zinanzo
Zidza kwa ifedi, 126
Inde mtima wakewo 1. AMBUYE, m’imfamo
Uli wokomadi.) Munandikonda ine;
Sindikaniza ’Nu
2. Mwamva Yesu m’mtimamo, Kanthu konse ’yi.
Adzanso kaŵiri, Ndimagwadira ’nu.
M’mene ali nanutu Ndikonda m’mtimamu,
Muli ndi Chimwemwe. Ndidzaperekatu
Ntchito zachifundozi Nsembe yangayi.
Iye watha izi,
Kuti mwawo m’Mwambamo 2. Kumwamba kwanuko
Naye tikhalebe. Mundipempherere;
Ndikhulupirako,
3. Mwamva Mzimu wakewo, N’dzalandiradi;
Zake zimvekanso Ndisenze mtandawo,
Kugwa ngati mvulayo Ndikhale mboniyo,
Yachisomo chake. Ndiperekeko
Mzimu ndiye mphamvudi Mitoloyi.
M’moyo mwathu muno,
Mpaka tidzafikako 3. Ndikhumba mtimawo
Komwe kuli Yesu. Wofatsa ndithu,
Kuti ndiyambe ’ne
125 Ntchito zanuzi;
Akusokerawo,
1. AMBUYANGA Yesu,
Abwere kwawoko,
N’kukondani Inu;
Inde,kwanutu.
Ndisiya zoipa
Chifukwa cha Inu.
4. Zambiri zangazo
Ambuye wabwino
Mnandipatsa kale,
Mundipulumutse konse;
Ndibweza zonsezi
Ndikonda tsopano
Kwa Mbuyanga ’Nu;
Koposa kale lonse.
Ndikadzaona ’Nu,
Mbuye wabwinotu,
2. Ndikonda chifukwa

32
Nsembe yokomatu Milandu yangayi.
Ndidzakhalabe.
3. Pamtanda woopsya
127 Adakandifera,
Natsika m’mtimanga
1. WAFUNAFUNA ine
Mukhale moyera.
Ambuye Yesuyo;
Wapeza ine ndithu
4. Tsopano Mulungu
Wodwala m’mtimamo:
Alandira ine,
Zochimwa zanga zonsezo
Popeza Mbuyanga
Wachotsa izo zomwezo.
Nawombola ine.
E! chikondi ndithu,
5. Padziko lapansi
E! chikondi ndithu,
Ndikumva chisoni,
Ndi chisomo chake chonsecho,
Komatu kumwamba
Ndi zozizwa zake zonsezo.
Ndikhala ndi Mboni.
2. Ndafoka ine kale
Ndafuna kufaku; 129
Zinthenda zangazo; 1. IMFA ndi mfumu ya mdimawo,
Ndi mwazi wake woti pyu! Anthu oipa imangawo,
Ndayera nawo m’mtimamu. Akhristu amapulumuka.
Omwe aimbira moyo,
3. Mabala ake m’manja Moyo ndi moyo ndi moyo,
Ndaona indetu, Wosalekana ndi moyo
Ndi minga ya pamutu Wosamaliza Mulunguyo.
Yolasa Mbuyeyu;
Etu, wakonda inedi, 2. Yesu anafa pamtandapo,
Pamtandapo kufera ’ne. Mzimu woipa nugomapo,
Ndi ife titame Mulungu.
4. Ndikhumba ine ndithu Ndife tamasudwa m’moyo
Madalo akewo; Imfa ithedwa ndi moyo,
Ndifuna kumyamika Tsiku lomaliza moyo
Masiku onsewo; Wosamaliza Kumwambako.
Ndikafa ine pansipa,
Kumwamba ndizamtamanso. 3. M’mitima mwathu mwakhala mbee!
Mtambo wamdima wang’ambwa ke!
128 Panyanjapo pagawanika.
Ndife tipita ku moyo,
1. AMBUYE Mulungu,
Mtima wabwino ndi moyo;
Ndikondwera maka,
Kumbanda kucha kwa moyo
Ndapeza chimwemwe
Kumatiuza za dzuŵalo.
Ndi moyo wosatha.
4. Akumangidwa ndi mzimuwo,
Aleluya, mlemekeze,
Mudze ndi ife kwa Yesuko,
Aleluya, ndiye Mfumu;
Akuchotsereni magoli,
Aleluya, mumpembedze
Nadzakupatsani moyo,
Ambuye Mulungu.
Mlandu walipa ndi moyo,
Moyo ndi moyo ndi moyo,
2. Ambuyanga Yesu
Tambirana za moyowo.
Nandikhetsera mwazi,
Nakonza ine

33
130 Ndifunitsa anthu onse
Adziŵenso Yesuyo!
1. ADALITSIKA munthuyo
Ndifunitsa anthu onse
Wopeza dalo lomwelo,
Adziŵenso Yesuyo!
Chisomocho cha Mlunguyo
Chogwera m’Mpingo wakewo.
2. Sindinanyengedwa konse:
Yesu wachotsera phe!
2. Chikhulupiro chomwenso
Zakuchimwa zanga zonse
Chogweratu m’chikondicho;
Zakupsinja mtimazo.
Akhala nazo nzeruzi
Yesu potsagana nane
Zofumatu mwa Mbuyedi.
Wandidzaza ndi mtendere;
Kundisunga, kundikonda
3. Adalitsika, indetu,
Sadzaleka konse ’yi!
Wodziŵa wadza Yesuyu
Kundisunga, kundikonda,
Nafera iye kalelo
Sadzaleka konse ’yi!
Ampatse moyo wosatha.
3. Sindinanyengedwa konse,
4. Akondwerera nthaŵiyi
Yesu adzabwerabe;
Pomvera mwini Mlungudi;
Mtima wanga undiuza
Mtendere ngwake panotu,
Akuyandikiradi
Nakhala nawo m’Mwambanso.
Omwe sangamzindikire
Andinyoza nandijeda,
131 Koma Yesu ati zedi;
1. NDIDZIŴITSITSA Yesu ndi wanga, “Ine ndidzabweradi.”
Tsiku ndi tsiku ndimakondwera. Koma Yesu ati zedi;
Anandigula ndi mwazi wake, “Ine ndidzabweradi.”
Anandipatsa Mzimu woyera.
4. Sandinyenga, salephera;
Mawu omwewo, nyimbo yomweyi, Yesu wadalitse ’ne
Yesu ndimtama tsiku lonseli; Mpulumutsi ndi Myeretsi
Mawu omwewo, nyimbo yomweyi, Ndi Mchiritsi yemweyo
Yesu ndimtama tsiku lonseli. Wandiyanjanitsa naye,
Mtima wanga nakhutitsa;
2. N’kamvera Yesu ndikakondwera, Sindinanyengedwa konse,
Ndiyang’anitsa nkhopeyo yake; Yesu akwaniradi!
Ndipo angelo anditengera Sindinanyengedwa konse,
Ine chisomo ndi chuma chake. Yesu akwaniradi!

3. Ndine kapolo wa Mbuye wanga;


Andigwiritsa zintchito zake.
133
1. MULUNGU wanga,
Ndimyembekeza adzabweranso,
Ndapeza moyo;
Adzanditenga kwawo ndikhale
Ndili wokondwera
Masiku onse.
132
1. SINDINANYENGEDWA konse Aleluya, muyenera!
Pakutsata Yesuyo; Aleluya, Amen.
Yesu apambana zonse Aleluya, ndidzamtama
Ndinalingalirazo. Mulungu wanga.
Pakuyenderana naye
Ndimamdziŵa ndi woona; 2. Mwazi wa Yesu

34
Unditsukatu, Utikonda ’fe.
Ndiye Mbuye wanga
Ndi Mpulumutsi. 135
1. YESU ndiye Mbuye wanga,
3. Pamtanda wake
Ndamva Mawu akewo
’Nafera ine,
Andilandira ine,
Ndi zoipa zanga
Nandipulumutsatu.
’Nazichotsadi.
Mwalembedwa mukalata
4. Mulungu wanga
Mawu ake omwewo,
Andilandira,
Kuti iwo akumvera
Chifukwa cha Yesu
Akalandiridwatu.
Mwana wakeyo.
2. Ndinakahala wakuipa,
5. Adzabweranso
Ndinamkana kalelo;
Kundilandira
Koma Yesu waiŵala
Ndikhale ndi Iye
Mphulupulu zangazo.
Masiku onse.
3. Wapumitsa mtima wanga,
134 Kaamba ndaphunziratu
1. TILI ndi mtendere Mau ake olembedwa
Wopambanatu, Mukalata mwakemo.
Monga ngati mtsinje
Mumitimamo; 4. Mumvetu abwenzi athu,
Koma mtsinje uno Musakanirire ’yi;
Umayenda phee, Yesu aitana inu,
Nthaŵi zonse mtima Zalembedwa zomwezi.
Nutonthozabe.

Tikakhulupira
136
1. MTENDERE uli m’mtima mwathumu,
Mlungu wathuyo,
Chifukwa mwazi watitsuka mbuu!
Tidzaona mwayi
Ndi mtenderewo.
2. Zakutsogolo sitidziŵa ’yi;
Adziŵa Yesu wathu zonsezi.
2. Dzanja la Mulungu
Litisunga nji!
3. Abale angakhale m’talimo
Nkhondo ya Satana
Mbuyethu asungira onsewo.
Sitiopa ’yi.
Zaphokoso zonse
4. Imfa ndi manda sitiopa ’yi,
Ndi zoopsyazo
Chifukwa Yesu wazithetsadi.
Sizibvuta mtima,
Siziloŵamo.
5. Mtendere wopambana m’Mwambamo
Pakufa ife tidzaonanso.
3. Masauko athu
Ndi zokondwazo,
Azilola zonse 138
Ndi Atatewo. 1. KHALANI duu! Ambuye adzatu;
Pokhulupirira Senzani chete mtanda wanuwu;
Tidzapezabe Mulungu adzakonza zanuzo,
Kuti mtima wake Sangasinthike mtima Iyeyu.

35
Khalani duu! Bwenzilo Yesuyo 140
Atsogolera m’njira mwathumu.
1. MULUNGU anditsogolera,
Ndapumula m’mtimamo;
2. Khalani duu! Mulungu wanuyu
Ayang’anira njira zanga
Akonzeratu nthaŵi zonsedi;
Nsiku zanga zonsezo.
Musakayike mtima; zo’psyazo
Zimasulidwa pomalizapo.
Mulungu anditsogolera
Khalani duu! A Yesu Mawuwo
Nsiku zanga zonsezo;
Ngamphamvu lero monga kalelo.
Ndidzatsatira Mbuye wanga
M’njira mwake momwemo.
3. Khalani duu! pakufa mnzathuyo,
Pakumlirira ndi misoziyo;
2. Masiku ena pali mdima,
Pa nthaŵizo abwera Yesutu,
Ndivutidwa m’mtimamo;
Mitima yathu natonthozadi.
Masiku ena ndikondwera
Khalani duu! Ambuye athadi
Ndi zabwino zangazo.
Kutibwezera zochotsedwazi.
3. Masiku onse m’mtima mwanga
4. Khaladi duu! pakufa ifetu,
Ndili ndi mtenderewo,
Ndi Yesu tidzakhala indetu
Chifukwa ndimakhulupira
Popanda mantha ndi zoŵaŵazi,
Mtsogoleri wangayo.
Chikondi chokha koma m’mtimamo.
Khalani duu! pakutha zonse phe
Tidzasonkhana tonse kuli ’Ye. 141
1. M’MENE ine ndisauka
Ndi zoipa zangazo,
139 Ndidzapita kwa Mulungu,
1. NAMONDWE akawombabe,
Adzandilandiratu.
Mafunde akakulanso,
Palipo pobisala ’fe.
Mlungu adzandilandira,
Ndi popemphera Yesuyo.
Iye ndiye ’Tate wanga;
Watumiza Mwana wake
2. Paja athira Yesutu,
Andifere kalelo.
Chimwemwe muli m’manthamo,
Paja pokometsetsatu,
2. Ngatitu abwenzi anga
Mwazi wa Yesu nukhapo.
Sandikonda ine ’yi,
Ndikhulupirire Mlungu,
3. Pakulekana ifetu
Iye sandikana ’yi.
Mitima ikomanapo;
Tikumbukana ’bwenzi ’fe,
3. Pansi pano ndili mlendo,
Popempherana komweko.
Kwathu ndi Kumwambako;
M’mene ndimalira ine
4. Tidzathaŵira kuti ’fe
Ndidzapita komweko.
Pochita mantha nkhaŵanso?
Pakuyesedwa, tinke ku?
Tipemphe Yesu mphamvuyo. 142
1. MBUYANGA Yesu, mundigwire
5. Tikhale ndithu pomwepo; Dzanja.
Zapansi zisaloŵe ’yi. Kuyenda ndekha sindikwana ’yi;
Sitidzapempha m’Mwambamo; Mukandigwira dzanja langa, Mbuye
Tidzayamika Mlungudi. Sindikaopa kanthu kena ’yi.

36
2. Mbuyanga Yesu, mundisunge ine Ambuye, Mpulumutsi.
Pafupi ndi ’Nu nthaŵi yonseyo;
Ndikasoŵatu Inu, Mpulumutsi, 146
Ndingosekera m’talimo.
1. PAMENE ndisauka,
Pamene ndivutidwa,
3. Mbuyanga Yesu, ndikapanda Inu
Mizimu yakuipa
Ukadza mdima m’mtima mwangamu;
Ikadza nindiyesa,
Koma ndinutu dzuŵa langa ndithu
Lakuwalitsa m’mtima momwemu.
Mulungu wanga,
Mwini mphamvu,
4. Mbuyanga Yesu, mundigwire dzanja
Mkandikumbukire ’ne.
Pamene ine ndimwalirapo.
Mkhaletu m’fupi nthaŵi yomwe Mbuye,
2. Pamene ndilemedwa
Mundiloŵetse ine m’Mwambamo.
Ndi zakuipa zanga,
Poloŵa mdima m’mtima,
143 Pochita ine mantha,
1. NDIFUNA Inu, Yesu
Ndadzala ndi machimo, 3. Masiku anga onse
Mumzimu muli mdima, Mulungu mundisunge;
Ndikufatu m’katimo. Pamene ndimwalira,
Ndifuna kutsukika Ndi tsiku lomaliza,
M’chitsimecho cha mwazi
Wa Inu wokondedwa, 147
Munandifera kale.
1. KHALA chete mtima wanga
Mlungu wako ndiye Mfumu;
2. Ndifuna Inu, Yesu,
Zinthu zonse zisinthika,
Lisoŵa bwenzi lina
Mlungu ndi wachikhalire.
Losungiritsa ine,
Londithandiza mwina.
(Khala chete,
Ndifuna mtima wanu
Chidzakupinga ninji?
Wodziŵa nkhaŵa zanga,
Usaope,
Wondisezera mtolo
Mulungu ali nawe.)
Wa tchimo lonse langa.
2. Anthu onse pansi pano
3. Ndifuna Inu, Yesu,
Sakhutitsa mtima wawo;
Ndimasauka ndithu,
Amadera zinthu zawo,
M’ulendo andisoŵa
Namakhumba zakutali.
Kambayo wa padziko.
Ndifunanso chikondi
3. Khala chete mtima wanga,
Cha Inu chondisunga,
Zikwanire zinthu zako;
Chakundisangalatsa
Usakhumbe zapansipa
Panjira ponse panga.
Koma Mlungu wako yekha.
4. Ndifuna Inu, Yesu,
Ndidzaonana nanu, 148
Mudzadza pamitambo 1. NGATI mtima sumakonda
Ikhale mpando wanu; Yesu supumula bwino;
Pamodzi ndi ananu Mbuye, suwu mtima wanga,
Ndidzakondwera kuti; Ndiwo wanu, mulandire.
Ndilemekeze Inu,

37
2. Dziko lonse ndilitaya; Mundigwiritse ntchito zanu
Ndikondetsa Yesu Mbuye; E! zanu zokhazo.
An’komera kopambana
Andikondweretsa ndiye. 4. Mulamulire mtima, Yesu,
Ndi chifuniro changa;
3. Ndakudani, mnandikonda Muloŵe mwanga ngati Mfumu;
Ndi kukhetsa mwazi wanu. Mundimveretsedi.
Simuleka kundikonda;
Ine sindidzalekanso. 152
1. “KHALA mwa Ine,” Yesu anatero;
4. Mndisungire mtima wanga,
Mawu abwino, koma Mbuye wanga
Uzikhulupira Inu,
Sin’ngathe ndekha, mukhalitse ine
Kuti moyo wanga wonse
Mwa ’Nu ndikhale nawo moyotu.
Ubisaletu mwa Yesu.
2. “Khale mwa Ine,” munachotsa tsoka,
149 Mletse Satana anganyenge ine:
1. NJIRA yanga sindiziŵa, Mibvi yamoto yake muizime
’Tate muikonza; M’mtimamo, ndikhulupirire ’Nu.
Komatu muzindikira
Kuti mundikonda. 3. “Khala mwa Ine,” ndinu mwini mphamvu,
Mundithandize ine ndikafoka;
2. M’mene mantha andigwira, Mzimu Woyera andiululire
Andidetsa m’mtima, Zoona zanu m’mtima mwangamu.
Mbuye, ndithaŵire kwanu
Poti mundikonda. 4. “Khala mwa Ine,” ndinu mwini moyo.
Nthambi zouma zidulidwa m’mtengo:
3. Sindidziŵatu zamaŵa, Ine wopanda Inu ndifokanso,
Koma sindiopa; Zipatso zikasoŵa msadze ’ne.
Ndidzakhulupira Inu
Kuti mundikonda. 5. “Khala mwa Ine,” Mbuye, ndifunitsa;
Mzimu Woyera mlonge m’mtima
4. Inde wakukonda ndinu; mwanga,
Mawuwo oona Akagonjetsetu machimo anga,
Andidzaza ndi chimwemwe: Mtima woyera andipatsenso.
Mlungu andikonda.
153
151 1. AMBUYE mundisunge
1. MNDIYANDIKITSE nanu. Pafupi ndinutu;
Yesu, Palibe malo pena
Ndiyenderane nanu; Popuma pansipa.
E, nditsamire panu, Yesu, Adani andizinga,
Panjira yonseyi. Zoipa m’katimo;
Chifundo chanu Yesu
2. Ndionetsere kuunika Chikonze m’mtimamo.
Kokoma kwanu, Yesu!
Yabwino mbiri ndibukitse 2. Ndikabisala mwanu
Yokondweretsayo. Ndilibe mantha ’yi;
Ndikasungidwa kwanu
3. Chitsime chakuyera ine Mumtima muti phee!
Ndifanefane nacho; Ndi mphamvu yanu yokha

38
Ndiposa ’daniwo; 4. Ndikhazikike inetu, mumtima muli
Chifundo chanu Mbuye mwai,
Chitchinjirize ’ne Ndi Yesu ndikondanetu, si kanthu
kena ai.
3. Ndidzaonana nanu
Mokondwakondwadi. 156
Oyera mtima onse
1. MBUYE ndamva mwawazira
Apenya Mbuyeyo.
Anthu ena madalitso;
Kumwamba n’dzaimbira
Mvula yanu yawagwera;
Kukoma kwanuku;
Mbuye, ine mudalitse.
N’dzatama nthaŵi zonse
Chikondi chanucho.
Etu ine, etu ine,
Mbuye, ine mudalitse.
154
1. KHALATU woyera, pempheratu 2. ’Tate, msandipitirire,
m’tseri; Ndimaipa mtima ine;
Werengani Mawu masiku onsewo. Ndiyenera munditaye,
Uthenga omwe ali akufoka, Koma mukhululukire.
Madalitso ake ufunefunebe.
3. Yesu, msandipitirire
2. Khalani woyera, dziko laipadi; Kuti ndinu ndikondane;
Pemphera kolimba kwa Yesu Ndinalira Inu Mbuye,
Mbuyathu. Msandileke poitana.
Yang’anitsa Yesu ndi kumutsatira,
Kuti anthu ena aonenso Iye. 4. Mzimu, msandipitirire,
Mupenyetsatu akhungu
3. Khalatu woyera, akutsogozetu; Mboniyo ya Mbuye Yesu,
Usamtsogolere munjira zakozo. Mundipatse ine mphamvu.
Pokondwa ndi m’nsoni tsata Ambuyako
Khulupira Yesu ndi Mawu akewo. 5. Ndinagona mwa zoipa,
Ndinakunyozani ine,
4. Khalatu woyera, khalatu wofatsa; Dziko lino ndinakonda,
Alilamulire ganizo lakolo. Mbuye, mukhululukire.
Utatsogozedwa ndi Mzimu wakeyo,
Msanga udzagwira m’Mwamba 6. Ha! chikondi cha Mulungu,
ntchito yake. Mwazi wa Mbuyathu Yesu,
Chiyanjano cha Mzimuyo
155 Zonse zidzalemekeza.
1. MUDZAZE Yesu mtima wanga ndi
chikondicho,
Ukhazikike pa Mulungu wosachokapo. 157
1. AMBUYE, thandizenitu
2. Mwa ine myatse moto wanu waku Ndi mphamvu zanuzo;
yera mbuu, Pantchito zathu zonsezi
Utenthemo zoipa zonse zidakhalamo. Mthandize Mbuyathu.

3. Mubweretu nomwe ’Nu munatsika kalelo; 2. Zochimwa zathu m’mtimamo


Ndilira Inu mundidzaze mphamvu Tilira nazotu;
yanuyo. Mumtima mwathu muti zii;
Mthandize Mbuyathu.

39
Zokoma zonse zapadziko
3. Mthandize Mbuye, timvetu, Sizindikwanira.
Tikalandiredi
Zimene muperekazo 4. Mubwere, Mzimu wa mpumulo,
Zakudalitsa ’fe. Mundileze m’kati;
Ndidana nazo zoipazo
4. Kumwamba Yesu mthandize, Zinakuchotsani.
Tilibe wina ’yi:
M’moyo, muimfa mthandize, 5. Mundichotsere tchimo lonse
Tikhale kwanuko. Ndinakonda kale,
E, muligwetse kuti ndinu
158 Mfumu mukakhale.
1. POKHALA mtendere mu mtima-
6. Mkatero ndidzayenda m’njira
ngamu,
Ndi Mulungu wanga,
Pamene ndisaukanso,
Idzandiunikira nyali
Pamene mabvuto ndi akuludi,
Njira ya Kumwamba.
Moyo wangawu ngwabwinotu.

Moyowo 160
Ngwabwino, 1. NDILIRA mtima wotamanda
Moyo wanga ulitu bwino. Mlungu, ndi woyera,
E, mtima woyamika mwazi
2. Ngakhale Satana andizunza ’ne, Munandikhetsera.
Chilipo chitonthozacho;
Chifundo cha Kristu anafera ’ne, 2. Mtimatu wopirira ndi
Kundipatsa ’ne moyo wake. Wofatsa mkati mwake,
Mumveka Mbuye Yesu yekha,
3. Uchimo unapachikidwa pomwe Ndiye Mfumu yake.
Pamtanda wa Yesu Mbuye;
Machimo angawo anatherapo; 3. Ndilira mtima wakulapa
Mbuye wanga, ndiyamika ’Nu. Ndi womvera Yesu,
Wosasiyana ndi Ambuye
4. Ambuyathu, ndikhumba tsiku lija Wakukhala m’mwemo.
Limene ndidzaona ’Nu;
Lipenga limveke, ndidzakondwatu 4. E, mtima watsopano ndi
Pakukomana ndi Yesuyo. Wodzala ndi chikondi,
Wangwiro ndi wokoma, Mbuye,
159 Wonga wanu wonse.
1. NDILIRA ine kukayenda
5. Mkhalidwe wanu mundipatse
M’njira ndi Mulungu;
Ndifanane nanu
Ndilira nyali ndikaone
Mulembe m’mtima mwanga Dzina
Njira Ya kwa Yesu.
La chikondi chanu.
2. Chimwemwe chija chamumtima
Ndinalaŵa kale 161
Poyambutsata ine Yesu, 1. Zoipa zangazi
Chili kuti tere? Zidetsa m’mtimamu;
Mnditsuke, Yesutu,
3. Kalelo m’mtima ndinakondwa, Kutsuka koti mbuu!
Tere ndingolira,

40
2. Ndafoka inetu, 4. Zonse umazinyadira
Ndalema m’mtimamu; Udzaleka kusirira;
Andilimbitsa ’Ye, Uli nazo zokwanira
Kulimba koti njo! Pakupeza Yesuyo.

3. Zin’soŵa indedi 5. Mbiri yake ubukitse,


Zabwino m’mtimamu; Anthu onse nuphuzitse,
Ambuye, mdzazebe, Kwa Mulungu nufikitse
Kudzaza koti tho! Osokera onsewo.

162 6. Yesu sakusiya konse;


Mphamvu, nzeru, chuma chonse
1. AMBUYE, ndifuna nditsukenitu;
Akupatsa nsiku zonse;
Mukhalire ndine mumtimangamu;
Tsata Yesu yekhayo.
Muthyole zonsezo zodetsa ’netu;
Musambitse ine, ndiyeretu mbuu!
164
Ndiyere mbuu! E, ndiyere mbuu! 1. MKRISTU, ulimbike
Musambitse ine, ndiyeretu mbuu! M’ntchito yakeyo;
Yesu anafera
2. Ambuye, chotsani zonse zomwezo Anthu akewo.
Zakundisautsa mumtimangamu;
Ndileke zangazo zoipsa ’netu 2. Mphamvu zathu zonse
Musambitse ine, ndiyeretu mbuu! Tionetsenso,
Kuti kudziŵike
3. Kumwamba ndiona Ambuyangayo, Tili akewo.
Mudzandithandiza, nditsate ’nemo;
Mudzandichotsera zoletsa ’netu; 3. Mtima wakufatsa
Musambitse ine, ndiyeretu mbuu! Amakondako;
Ndipo anthu onse
4. Chifukwa cha ichi ndipempheratu, Angatengero.
Ndidikira Inu Ambuyangayu;
Ndikhulupirira pa mwaziwo pyu! 4. Mapemphero athu
Musambitse ine, ndiyeretu mbuu! Tikakwezebe,
Dzina lake lomwe
163 Tiyamike ’fe.
1. USAFUNE, chuma chokha,
5. Limbikani nonse
Pena maseŵera okha,
Mpaka imfayo.
Koma za Mulungu zokha
Ndipo Mfumu yathu
Zipambana zinazo.
Idzakondwako.
2. Ukafuna kulemera,
Pempha chuma chosathera, 165
Ndiwo mtima wakuyera 1. GWIRA zintchito zako,
Ndi wokonda Yesuyo. Pomva usiku udza;
Yamba mamaŵa ndithu
3. Zosauka ubvomere, Potuluka dzuŵa.
Ndipo Yesu chaulere Gwiranso m’msana monse
Chikondano ndi mtendere Dzuŵalo likatentha;
Aloŵetsa m’mtimamo. Gwira tsopano ntchito;
Msanga udzaleka.

41
2. Ntchito za Yesu gwira 3. Anasauka Mbuyeyo,
Pomva usiku udza; Mwini nalola zonsezo;
Lero lonseli gwira, Anatsiriza ntchitozo,
Bwino udzapuma. Osabwerera imfayo.
Gwiratu tsiku lonse
Ntchito zakuyenera; 4. Ndikamayenda m’dimamo,
Gwira tsopano ntchito, Mletse zodandaulazo;
Tere udzaleka. Mundikumbutse mtandawo;
Zanga zichepa zonsezo.
3. Mkristu gwiratu ntchito
Pomva usiku udza; 5. Ine nditaya chumacho,
Dzuŵalo lopendeka Ndikondweretse Mbuyeyo,
Tere lidzaloŵa. Thupi liopa mingayo,
Gwiranso ’dzulodzulo Koma mlimbitse mtimawo.
Kutada mdima bii!
Tsono zintchito zonse 168
Zatha zonsezi.
1. YESU, afuna iwe unke kwawoko,
Loŵa m’njira yake yakuyerayeratu;
166 Anadzera m’Mwamba kutiperekezako;
1. TITHAŴIRENJI ifetu Yamba msanga iwe kunka kwanuko.
Mphamvu za Yesu nzathunso.
Kristu atithangatatu. Tsata, tsata, nditsatadi Yesu;
M’nkhondo ya moyo wathuyo. Iwetu, iwetu, ukatsatanso.
Tsata, tsata, nditsatadi Yesu;
2. Yendani bwino m’njiramo Inu nonse mukatsate Mbuyeyo
Ya kwa Mulungu wathuyo;
Kwezani maso kuli ’Ye; 2. Ngati umtsata Mpulumutsi wakoyo,
Kristu ndi njira yomweyo Udzakhaliranso kuli Mbuye wakoyo;
Adzapulumutsa thupi, mzimu wakonso,
3. Nkhaŵa tilbe; Yesuyo M’mphamvu ndi chilango cha zoipazo.
Atsogolera m’njiramo;
Tikhulupire Iyeyo, 3. Kunsi kudambo, pena m’mwamba
Kristu ndi moyo wathuwo. m’phirimo,
Pomwe pali Yesu ndidzayenda
4. Tioperanji ifetu? yendapo:
Ali pafupi Mbuyeyu; Andiperekeza bwino m’njira yakeyo,
Sangasinthike mtima ’yi; Kuli Mzinda wa Mulungu wangayo.
Kristu akonda ifetu.
169
167 1. MBUYE, mwatiuza ’fe
1. MBUYE, nditsate bwanjiko? Tizikhala mchere
Ine ndikonde bwanjinso? Wokometsa onsewo
Bwanji kuyenda m’njiramo Akumanga kwathu.
Yonka Kumwamba kwawoko? Mcherewu ndi ifetu;
Mtifanize nanu,
2. Kodi m’njiramo ndimvadi Tikakope ndi chitsanzo
Nsoni zoŵaŵa, nkhaŵazi Onse akuchimwa.
Ndi masauko, mingayi?
E, nkana izi n’tsatabe. 2. Mbuye, mwatiuza ’fe

42
Tizikhala nyali 171
Yoonetsa onsewo
1. M’MENE umauka m’maŵa,
Njira yonka kwanu.
Sunagwire ntchitozo,
Nyali ndi ifetu;
Sunayambe kukayenda,
Kuunika kwanu
Ugwadire Mlunguyo.
Mutipatse tiŵalire
Pena uli kusekera,
Osokera onse.
Pena nkhaŵa m’mtimamo,
Wachimwemwe, wachisoni,
3. Tisasungaluke ’yi,
Uza Yesu zonsezo.
Tisasiye Yesu.
Tisabise nyaliyi
2. Wakuchezacheza naye
Pakuchita mantha.
Ukagwira ntchitozo;
Mcheretu ndi nyaliyi
Pakukumbukira Yesu,
Tizikhala tonse;
Nkhaŵa zidzachokanso
Mbuye, mtiyeretse m’mtima
Ndi zapansi zikafuna
Tikatero ndithu.
Kukudzaza m’mtimamo,
Utsogole kopemphera,
170 Uza Yesu zonsezo.
1. M’MAŴA tizifesa
Mbewu zakukoma, 3. Ndi m’kutero udzadziŵa
Msana ndi usiku Chifuniro chakecho;
Tizifesa momwe. Iye adzakuthandiza
Nyengo yamasika Uthangate enanso:
Tidzatema m’munda, Ndi ofoka ulimbitse,
Tidzabwera tonse Akulapa bwezatu;
Ndi zipatsozo. Ndi za ntchito zake izi
Uza Yesu zonsezo.
Ndi zipatsozo
Ndi zipatsozo 4. Ndipo ngati ungolema,
Tidzabwera tonse Ulefuka m’dzulomo,
Ndi zipatsozo. Ndi Satana akayesa
Kukukola m’mtimamo:
2. Tizifesa m’dzuŵa Wakufoka, wakuopa,
Tizifesa m’mthunzi, Penyetsetsa Iyeyo;
Sitiopa ife Udzakhazikika m’mtima
Mtambo ndi chisanu. Pakumuza zonsezo.
Athatu masika
Ntchitozi zidzatha; 172
Tidzabwera tonse
1. HAYA! ’nzanga taonani
Ndi zipatsozo.
Yoonekayo
Yakumwamba iti: “Yesu
3. Tingolira kaya,
Alikudzako.”
Koma tidzafesa
Mbewu za Ambuye;
Kanganani nkhondo yanu
Ntchitoyo nja Yesu.
Ndi mbendera mbuu!
Adzachotsa msozi,
Tibvomere: ‘Inde Mbuye
Adzatilandira,
Mtithangatetu.”
Tidzabwera tonse
Ndi zipatsozo.
2. A! mizimu yakuipa
Isautsabe,

43
Tikaniza zakuipa Chita zolungama ’we,
Zotizinga ’fe. Yenda bwino, khulupirira
Mbuyeyo, Mbuyeyo,
3. Mdani adza nazo mphamvu, Ndikuchita zakezi.
Koma ifetu
Tidzamthetsa nkhondo yake 2. Taya zako zochenjera,
Timwingitsetu. Taya zamumdimanso;
Nthaŵi zonse khulupira,
4. Yesu ati, “Ndidza msanga!” Chita zolungamazo.
Thangateni phee! Usayang’anire wina
Mbweze mawu akulimba: M’khondo yake yomweyi,
Tikanganabe. Koma m’zonse khulupirira
Mbuyeyo, Mbuyeyo,
173 Ndi kuchita zakezi.
1. ANATILEMBA Yesu tikagwire
3. Leka zakuipa zako,
nkhondo yake,
Myambi yonse yoti bii,
Natilimbitsa tipirire osaopa kanthu.
Usakhulupire mommo:
Kwa Satana n’ziwembu zake
Tamveradi Mbuyedi.
Sitigonja konse;
Adzadana nawe ena,
Tiyenderana naye Mfumu
Ena adzakonda ’we;
yathu yopambana.
Kweza maso, khulupirira
Mbuyeyo, Mbuyeyo
2. Amaliwongo ochuluka amaloŵa
Ndikuchita zakezi.
m’mtima
Nafuna kuipitsa usana ndi usiku;
4. Mawu ake atipatsa
Tikatsatabe Mfumu yathu
Mphamvu ndi mtenderenso,
Sitidzagwa konse,
Bwino atitsogolera,
Pakuti atipatsa mphamvu
Tikhulupirira ’wo
tipambane nazo.
Limba mtima, usapunthwe
M’njira yamumdimayi;
3. Amatininkha zida zoteteza mtima,
Yenda bwino, khulupirira
Ndizo;
Mbuyeyo, Mbuyeyo,
Kupempherabe, kukhulupirira ndi kufatsa;
Ndi kuchita zakezi.
Mtheradi, ndi lupanga ndilo
Mawu a Mulungu;
Pogwira zida zakezi sitilephera 175
konse. 1. POYESEDWA ine
Yesu mudzetu,
4. Mafumu atiuza tikaletse ukapolo, Mundipempherere
Ndi kumasula goli la anzathu akuopa Ndisachimwetu.
Tiyeni, tiŵauze za Mbuyathu Mpulumutsi Mukaona kuti
Nitiŵanditse mbiri yake Ndilefukatu,
M’dziko lonse lathu. Mbuye mndilimbitse
Nazo mphamvutu.
174 2. Ndi zapansi pano
1. LIMBA mtima mbale wanga
Ndikokedwadi,
Usapunthwe m’njirayi;
Koma ndi chisoni
Onatu nyenyezi ija
Mndiphunzitsedi;
Ikutsogoleradi.
Ndisaiŵalire
Tamveratu Mlungu yekha,

44
Za Getsemane, 177
Pena mtanda wanu
1. TIYENI Akhristu,
Yesu Mbuye ’Nu.
Nkhondo tigwire;
Yesu Mbuye wathu
3. Mukandipweteka,
Atitsogolera.
Ndipirirapo:
Mfumu yathu mwini
Nsembe yanga ndiyo,
Atipatsa moyo;
Landirani ’yo.
Taonanitu mbendera
Ndikachita mantha
Yailoŵa nkhondo!
Sindithaŵa ’yi:
Mtima udzalimba,
Tiyeni Akristu,
Ndidzaima nji!
Nkhondo tiigwire;
Yesu Mbuye wathu
4. Pakumalizidwa
Atitsogolera
Moyo wangawu,
Pomwalira ine,
2. Nkhondo ya Satana
Mudze Mbuyetu.
Idzakuthaŵani;
Ndidzadzipereka
Tiyeni Akristu,
M’manja mwanumo:
Kaipambaneni.
Mpulumutsi Yesu
Idzanjenjemera
Mndilandireko.
Mukapfu’litsatu;
Imbitsanitu anzathu,
176 Mau mukwezetse.
1. AMBUYE wa Kumwamba,
Mundithangatetu 3. Mpingo wa Mulungu
Kuyenda bwino lomwe Uli ngati nkhondo;
M’ulendo unowu. Titsagane nawo
Kaŵiri ndi kaŵiri Ana a Mulungu.
Ndipunthwa m’njiramo Sitipatukana,
Mlimbitse mtima wanga, Ndifetu amodzi;
Ndingatayikeko. Ch’yembekezo, chikondano,
Chonse ndi chimodzi.
2. Ndikhumba Mzimu wanu
Kundiyeretsa mbuu! 4. Zonse zapadziko
Pang’ono ndi pang’ono Zidzamalizira,
Mundiphunzitsetu; Koma mpingo wake
Ndifuna nzeru zanu Uli chikhalire;
Zakundifitsako Udzakhala ndithu
Kumwamba kuli Inu, Mphamvu za Satana,
Ambuye wangayo. Yesu analonjezetsa,
Mawuwo sakana.
3. Yochita ndi yodikha
Mupatse mphamvuyo, 5. Tiyeni anzathu
Ndikhale wochenjera, Tizithandizana;
Wogwira ntchitozo. Imbirani nafe
Zoipa zanga zonse Nyimbo zopambana
Mufafanizezo, Kristu ayenera
Ndiyende nanu nokha Mphamvu ndi ulemu;
Masiku onsewo. Komwe kuli Yesu.

45
178 3. Tsopano timenyana
Ndi zakuipazi;
1. TIYENI, Akristu inu,
Pamene nkhondo yatha
Mumenyane nkhondo iyi,
Tidzanka kwathuko.
Mukafoka nonse, koma
Yesu adzalandira
Yesu akulimbitsani.
Ankhondo ake onse;
Adzakhalika naye
2. Muyendanso kunka komwe,
Kumwamba komweko.
Mugonjetse mdani wanu;
Musafoke, musaleme,
Musagone konse inu. 180
1. MBUYE, ndapangana
3. Musagonje, anthu inu, M’njira yanuyi,
Mtamiretu Yekha Mbuye; Kuti ndidzayenda
Ipambana mphamvu yake, Osaleka ’yi.
Ya Mtsogoli wanu yemwe. Mundipatse mtima
Wopiriramo,
4. Mtima wanu wonse ndithu Wakukana zonse
Udzakhala ndi chimwemwe. Zondipingazo.
Zida zanu mbvale bwino
Zakudzera m’Mwamba momwe. 2. Mzimu wakuipa
Undiyesa ’ne;
5. Limbikani inu nonse, Mundithangatire
Msangalalo ngwanu nokha; Ku’thaŵitsabe.
Musaope kanthu kena Akandisautsa
Mumtamire Mbuye Yekha. Kum’dzi kunoku,
Muloŵetse mphamvu
6. Tiyeni ku nkhondo iyi, M’mtima mwangamu.
Mugonjetse zonse konko;
Muingitse mdani uja, 3. Akathira nsembe
Muyendetse m’njira momwe. Ku mizimuyo,
Ndipenyera kwanu,
179 E, Kumwambako.
Tsoka ndi zonyenga
1. AKRISTU limbikani,
Za ufitizo,
Imani mtima nji!
Yesu mndilimbitse
Mbendera nyamulani,
Ndisaopezo.
Msatenthemere ’yi.
Wotsogolera wathu
4. Pena kumwa nawo,
Ndi Mwana wa Mulungu;
Ndisateroko,
Adzagonjetsa onse
Pena kukaona
Adani athuwo.
Gule woipa,
Pena kuwombeza
2. Tigwire nkhondo yomwe
Sindifuna ’yi;
Ya Mbuye wathuyo;
Yesu mundithandize
Tileke zakuipa
Kuzikanazi.
Zokhala m’mtimamo.
Sitikwanira tokha
5. Ndinu mbusa wanga;
Kuleka zathu zomwe,
Mndithandizetu;
Koma Mbuyathu Yesu
Ndisaipse nazo
Atithangatatu.

46
Mtima wangawu.
Osaopa konse, 182
Osachimwa ’yi.
1. ANA akumwamba ndife,
Mundiyendetse Yesu
Paulendo timaimba;
M’njira yanuyi.
Timatama Mbuye wathu
Wa ulemerero wonse.
181
1. AULENDO, munka kuti Tilikupita kwathu kuja
Ndi zindodo m’manja mwanu? Munjira ya atate athu,
Paulendo tizipita; Amakondwera lero lomwe;
Aitana Mbuye wathu; Tinka kuonana nawo.
Pamapiri, pamadambo
Tizipita komwe kwawo. 2. Mbuye anatiitana
Tizipita komwe kwawo Kukagwira ntchito yake,
Kuli dzikolo labwino, Kuitana anthu onse
Tizipita komwe kwawo Atsatenso njira yino.
Kuli dzikolo labwino.
3. Inde Mbuye, tibweradi,
2. Kodi simuopa njira, Zathu zonse tizisiya,
Inu anthu akufoka? Mtsogoleri wathu ndinu
Ayi, atiperekeza Titsatabe inu nokha.
Mbuye wathu wotikonda.
Iye amakhala nafe, 183
Natitsogolera ife.
1. MBUYE munditsogolere,
Atitsogolera ife
Ndine mlendo m’dziko muno;
Kuli dzikolo labwino.
Ndikafoka mundikweze,
Atitsogolera ife
Mundisunge m’manja mwanu;
Kuli dzikolo labwino.
Mundidyetse, mundidyetse,
Sindingamve njalayo.
3. Mundiuze, aulendo,
Muli chiani m’Mwamba muja?
2. Mundimwetse madzi anu,
Atibvekako zoyera
Andichize nthenda zanga;
Akorona natininkha;
Utsogole mtambo wanu,
Moyo, moyo atipatsa,
Ndikadziŵe njira yanga;
Kwa Mulungu tidzakhala.
Mpulumutsi, Mpulumutsi,
Kwa Mulungu tidzakhala
Munditchinjirizetu.
Kuli dzikolo labwino,
Kwa Mulungu tidzakhala
3. Ndikaloŵa m’mtsinje muja,
Kuli dzikolo labwino.
Mndichotsere mantha osne;
Mndiwolotse tsidya lija,
4. Kodi inu, aulendo,
Ndikondwere nthaŵi zonse;
Ife titsagane nanu?
Nyimbo zanga, nyimbo zanga
Inde, mudze inu nonse,
Zidzalemekeza ’Nu.
Mudze nafe paulendo.
Inde, mutiperekeze,
Yesu atilinda ife. 185
Yesu atilinda ife 1. NDIMAYENDA paulendo
Kuli dzikolo labwino, Ndi yaminga njira yake;
Yesu atilinda ife Tsoka ndikapeza, koma
Kuli dzikolo labwino. Ndinka kwa Atate;

47
Pena m’mtima mwanga mwada, M’tsogolomo.
Pena andibvuta ‘dani, Ndipo mamaŵa n’dzaonana ndi
Ndikatenga nkhaŵa, mantha, Abale anga adafikadi.
Amadziŵako.

2. Ichi chindisangalatsa
186
1. TIYENI nonsenu okonda YESUYO,
M’mene nkhondo indigwira,
Tiimbe nyimbo yabwino,
M’mene nsoni zazikulu
Tiimbe nyimbo yabwino,
Zimanditsatira;
Ku mpando wakewo,
Mtima ukhazika m’mene
Kumpando wakewo.
Kwathu kuja ndikumbuka
Kuti Mlungu ali ndine,
Tiyeni pamodzi
Andisungako.
Tilikupita Kumwamba;
Akristu tilikupita
3. Mbuye andipeza lero,
Ku mzinda wa Mlungu.
Andikonda, andisunga;
Adzapitikitsa mdani
2. Ngakhale enawo aleke kwimbako,
Akamandibvuta.
Akristu ’fe tidzaimba,
E, ulendo wanga utha,
Akristu ’fe tidzaimba,
Tsono ine ndimwalira;
Kumlemekeza ’Ye,
M’mene ndidzafika kwawo
And’landirako. Kumlemekeza ’Ye.

4. Komwe ndi chimwemwe ine 3. Akristu tonsefe, tikondwe m’Dzikoli


N’dzaonana ndi Atate, Koposa anthu enawo,
N’dzagwadira ndi kumtama, Koposa anthu enawo,
Amandikondabe. Tisanafikeko,
Sakandisautsa kanthu Tisanafikeko.
M’dziko lija lakukoma;
Adzandidalitsa Yesu, 4. Tiimbe mokondwa, misozi iume;
Ndidzakondwako. Poyenda kunka kwathuko,
Poyenda kunka kwathuko,
185 Kwa Mlungu wathuyo,
Kwa Mlungu wathuyo.
1. MUNDIŴALIRE m’njira mwangamo,
Mbuyanga ’Nu.
Kwada usiku, ndasokerako, 187
Mtsogoletu. 1. NDAMVATU kuti tifika komweko
Phazi langali mndisungirenso, Kuli Ambuye, Mtetezi wathuyo.
Ndilonde Inu m’njira monsemo. Ine, pakutha zobvuta zathuzo
Iye tidzamwona maso ndi maso.
2. Sindidapempha kale Mbuye ’yi,
Mtsogole ’Nu; Ndi Mbuyeyo tikhalamo,
Ndisankha ndine, koma leroli Kupenyanso wokondatu;
Nditsatatu. Tidzakondwera, E, nthaŵi zonsezo
Ndidadzikuza osaopa ’yi; Ndicho chimwemwe ndi ulemutu.
Ambuye, msakumbuke zomwezi.
2. Kaamba chisomo cha Mbuyathu
3. Ndi kale lonse mnandisunga ’ne; uyu,
Tsopanonso. Malo okoma tipeza m’Mwambamo;
M’khwaŵa, paphiri, mundisungebe Kumva mtetezi amene ndi Yesu,

48
Ndicho chimwemwe ndi chachikulutu.
2. Munabvala thupi lathu,
3. Onse aliko takonda kalelo, Munadziŵa masauko,
Kale napita kwa Yesu Mbuyawo; Mnalirira bwenzi lanu;
Koma kumwona Mtetezi wathuyo Yesu mutimveretu.
Ndicho chimwemwe choposa,
nchathucho. 3. M’mene imfa yathu idza,
Mweya wathu ukaleka,
188 M’mene ife timwalira,
Yesu mutimveretu.
1. UKATHA moyo wanga
Kumwamba kundichera;
4. Mnamwalira Inu paja,
Dzuŵalo ndimalira
Mwazi wanu munakhetsa,
Lafika lokomera.
Koma Inu munadzuka;
Usiku m’nali mdima,
Yesu mutimveretu.
Tsopano mbanda kucha;
Kudzaŵalitsa ndithu
5. Mtima ukachita nkhaŵa
Ku Dziko la Mulungu.
Ndi zoipa zotimanga,
M’mene tikachita mantha,
2. Chitsime chachikondi
Yesu mutimveretu.
Ndi Yesu Mbuye wanga;
Ndalaŵa mtsinje pano
Ndzamwetsa ine m’Mwamba. 190
Komweko zidzakula 1. KODI uli ndi chisoni
Chisomo ndi chifundo, Choliritsa mtima wako?
Pondiŵalira kuja Kweza maso, ndi Atate
Ku Dziko la Mulungu. Akumvetsa zonsezi.

3. A! Yesu Bwenzi langa 2. Kodi umadandaula;


Inenso bwenzi lake, “Mbale wanga waferanji?”
Woipa ’ne alola Kumbukira Wakumtenga
Ndiloŵe m’nyumba mwake; Saphophonya konse ’yi.
Ndikhulupira Iye
Achotsa mphulupulu; 3. Mbale wako unamkonda,
Kudzandiŵalitsira Koma Yesu amkondetsa;
Ku Dziko la Mulungu. Anamfuna nagomtenga;
Usammane Yesu’yi
4. Ambuye andisunga
M’chifundo chachikulu; 4. Pakutsazikana nanu
Zisoni zisanduka Ndi potseka maso ake,
Chimwemwe cha Mulungu. Imfa, bii! Anangogona
Dzanjalo ndilitama Koma adzadzukanso.
Ndi mtima wachifundo,
Mpakatu kwaŵalitsa 5. Usalire; Mpulumutsi
Ku Dziko la Mulungu. Analaŵa imfa Yekha;
Imfa yomwe nagonjetsa
189 Potuluka m’mandamo.
1. TIKAGWIDWA ndi chisoni,
6. Chikondano sichifera;
Ikayendanso misozi,
Mbale wako udzamwona
Poliriratu abale,
Kwathu komwe; zipirira
Yesu mutimveretu.

49
Mpaka ukafikako. Za midzi ya padziko
Lapansi lonseli;
7. Leroli chisoni chokha, Mtendere wake koma
Tsiku lija kungokondwa; Wa Mzinda wathuwo
Kweza maso osalira, Upambanditsa zonse
Yesu akukondadi. Zapansi pomwepo.

191 3. Ndi nkhondo ikaleka


Kwa Mlungu komweko,
1. NTCHITO yonse yakeyo
Ndi ukapolo watha,
Yatha m’dzikoli linoli
Udani wathanso;
Mlendo wafikatuko
Ndi zakuopsa zonse
Pokocheza leroli.
Ndi zosauka zii!
Ndi mwayi wa kwa Mlungu
’Tate, mwa kusunga kwanu
Udzoza mutu tho!
Timusiya mwana wanu.
’Tate, mwa kusunga kwanu
Timusiya mwana wanu. 194
1. NDIKONDWA kuganizirabe
2. Yathatu misoziyo Za Dziko la Mulungu;
Zobisika zonse mbee! Momwemo muli abwezitu
Aweruza bwinoko Okhala mumtendere.
Ndiye Wolungamayo. Iwo salekana, iwo salekana,
Ayi salekana abwenzi omwewo.
3. Komwe Mbusa kwawoko
Atengera nkhosa zonse, 2. Komweko akhala Yesuyo
Zake asungiramo Mtetezi wa inedi
Zosaopa kanthu konse. Pakati pa ’womboledwawo;
Sadzamva kuŵaŵanso.
4. Onse akulapawo Iwo asekera, iwo asekera,
Ayang’ana mtanda wake; Inde asekera kumwona Yesuyo.
Aphunzira komweko
Zonse za kukonda kwake. 3. Mulibe zoipa m’Dzikolo,
Nzokomazo zabwino;
5. Dothili kudothilo, Ndi nthenda, imfa, misoziyi
Pfumbili kupfumbi tere; Kumwamba kulibenso.
Mpaka adzadzukanso Dziko labwinotu, Dziko labwinotu,
Timusiya mumtendere. Nawo mtenderewo, tikhumba ilotu.

192 4. Ndikonda kuganizirabe


Za Dziko la Mulungu,
1. MUMZINDA wa Mulungu
Za zonse zotikondweretsamo,
Moyera mulimo,
Nzosathanso chikondi.
Ndiye amathu omwe
Ife tikondwera, ife tikondwera,
Olera ifewo;
M’mene tidzampenya Ambuye wathuyo.
Mitima yathu yomwe
Ikondwereratu,
Nikhala nawo Mzinda 195
Wakukongolawu. 1. ’TATE wa Kumwambako,
Likayere Dzinalo,
2. Akondwerera anthu Udzetu Ufumu wanu;
Zokoma zonsezi Chifuniro chanucho

50
Chichitike pansipa Pempheranso usana;
Monga chachitika kwanu. Pemphera m’dzulo momwe,
Pemphera ndi usiku.
2. Mutipatse leroli Ndi mtima wonse idza,
E, chakudya chathuchi Tulutsanso zachabe;
Tsiku n’tsiku tichilira. M’nyumbamo ugwadire
Mukhululukiredi Ndi kukapempherabe.
Tchimo lathu, monga ’fe
Iwo adatichimwira. 2. Kumbuka ’bale ako
Ndi onse uŵakonda;
3. Musatifikitsemo Pemphera ’dani ako
Muli mayeserowo, Amene akutonza.
Koma mutipulumutse. Dzipempherere wekha
Wanu ndi ufumuwo, Mulungu akusunge;
Mphamvu ndi ulemunso Tchulanso popemphera
Kufikira nthaŵi zonse. Dzinalo la Ambuye.

196 3. Akakusoŵa malo


Opempheramo m’tseri,
1. Mtima wanga ndikonzera,
Komatu m’mtima mwako
Mbuye Yesu aitana;
Mwaloŵatu zoyera;
Ati: “Mwana, tapemphera,
Anazilonga m’mwemo
Ine sindidzakukana.”
Ndi Mzimu Wakuyera;
Zolingirira zija
2. Mbuye ndinu Mfumu yanga
Kwa Mlungu zidzakwera.
Yolemera ndi yamphamvu;
Ndikapemphatu zambiri,
4. Tilibe madalitso
Simundimanira kanthu.
Akulingana n’lino
Atate atipatsa,
3. Ndikabwera nd katundu
Kupempherabe bwino.
Wa zoipa zanga zonse;
Ukamvatu chisoni,
Mwazi wake wa Ambuye,
Kwa Mbuye kapemphera.
Udzandiyeretsa konse.
Adzakusangalatsa,
Pemphero adzamvera.
4. Mbuye ndinalema ine,
Mloŵe Inu m’mtima mwanga;
Mkhale m’mwemo mwini wake, 198
Mantha mwandichotsera ’ne. 1. POKUPEMPHERANI
Mundiphunzitse ’ne
5. Ndine mlendo pansi pano, Ndi Mzimu wanu Woyera,
Mndilimbitse ndi chikondi; Ndikayanjane nanu, Atate,
Bwenzi mundilondolere Ndi kukulemekezani ’Nu
Njira pa ulendo wonse.
2. Mdikumbutse zomwe
6. Mndidziŵitse ntchito yanga, Munandichitira
Mphamvu yake mundipatse; Ndikakuyamikireni,
Mundilimbikitse m’mtima Ndikweze Dzina lomwe angelo
Ndikhale kwa Atate. Aliimbira Kumwambako.

197 3. Mndimvetse chisoni


Pakuululira
1. PEMPHERA m’mbanda kucha,

51
Zochimwa zanga zambiri; Ndiloŵa Dziko lakedi;
Mumtima ndi kupatsa mtendere Ndidzati nthaŵi yomweyo;
Mutachotsera zoipazo “Tsalani bwino pansipo.”
Ndidzati nthaŵi yomweyo;
4. Chikondi, chimwemwe, “Tsalani bwino pansipo.”
Chifatso, chiletso,
Zipatso zonse za Mzimu 201
Mundibalitse, ndikafanane
1. MTIDZUTSE, Mbuyetu,
Ndi Mbuyathu popempherapo.
Mtionekeremu:
Munene zakukmvekazi,
5. Pakupempherera
Timvere ifetu.
Anzanga ndi onse
Akusokera mumdima,
Mtidzutse, Mbuyetu,
M’wapulumutse ndi k’ŵachitira
Mtipatse moyonso;
Zomwe mufuna k’ŵapatsawo.
Mudzetu Mbuye, mudzetu,
Tidalitseni ’fe.
6. Poloŵa ndi Inu
M’chipinda cham’tseri,
2. Mtidzutse, Mbuyetu,
Posonkhananso pamodzi,
Tikweze Dzinali:
Muyandikire nafe, Atate,
Tiuzireni Mpweyawo
Mtibvomere, mtidalitsepo,
M’mitima yathuyi.

200 3. Mtidzutse, Mbuyetu,


1. ZOKOMA ndithu nthaŵizi Timvere Mawudi;
Kwa Mlungu zondifitsadi; Zoona zanu tonsefe
Kumpando wachifumuwo Tikhulupire ’zi.
Ndiuza zanga zonsezo.
Pobvuta ine mtimamo 4. Mtidzutse, Mbuyetu,
Nditulapo pa Yesuyo; Mthirenso moyowo;
Pakuyesedwa ndinkatu Ulemu ngwanu nokha ’Nu,
Kwa Mbuye, sindikhala duu. Dalitso nlathulo.
Pakuyesedwa ndinkatu
Kwa Mbuye, sindikhala duu. 202
1. AKRISTU ndi abale, tiziyenderana
2. Zokoma inde nthaŵizi
tonse,
Zotama Dzina lomweli
Mulungu mmodzi tili naye, ndi
La Yesu, ndiwoonayo
Ambuye yemwe,
Wopatsa dalo lonseli
Chitsime chomwe, njira yomwe yo-
Ndilakalaka Iyeyu
khulupirira;
Wofera ine pansitu;
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi
Pakuda nkhaŵa ine bii
tiziyenderana.
Nditchula Dzina lomweli,
Pakuda nkhaŵa ine bii
2. Atate yemwe anatuma Mpulumutsi
Nditchula Dzina lomweli.
mmodzi
Kudzatifera kuti atiyanjanitse tonse,
3. Zokoma etu nthaŵizi
Ndi Mzimu yemwe ayeretsa aku-
Ndicheza naye Mlungudi;
mvera onse;
Koma kwathu m’Mwambamo
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi
Kumwona ndi koposako.
tiziyenderana.
Pobvula ine thupili,

52
3. Anatipatsa Mawu omwe olimbitsa Kuti tilimbane naye Satanayo,
mtima; osamwopa.
Kumwamba komwe tinka ndi kulo-
nda njira yomwe. 5. Pakubweradi Woyesa tidzamlaka
Tibalalikiranji ife akutsata Yesu? ifetu;
Tiyeni tonse, mMpingo ’modzi Angelonso adzabwera kutithandizira ife,
tiziyenderana. Kuti tilimbike ife ndi kumchotsa
m’mtima mwathu.
4. Satana apambana tikayamba kusiyana;
Tikayanjana, yemwe adzagonja ndi 6. Pa la Mulungu tibwera kulandira
kuthaŵa; zidazo;
Mbuyathu adzamthyola konse ndi Mphamvu yanu ndi chikondi zititso-
kumlamulira. golere ife;
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi Machitidwe ndi mkhalidwe zikokere ena
tiziyenderana. kwanu.

5. Tiphatikane tonsefe okonda Yesu Kristu; 204


Tisalekane pakugwira ntchito za
1. AULENDO amayenda
Mbuyathu;
Muusiku wo’psyawo,
Tilimbitsane pakuyenda m’njira yonka
Namaimba nyimbo zawo
kwathu.
Kunka kwawo m’Mwambamo.
Tiyeni tonse, m’Mpingo ’modzi
tiziyenderana.
2. Kuunika kuoneka
Koingitsa mdimawu;
203 Mbale amakondwerera,
1. MBUYE, Mpingo wanu usauka Osaopa konse ’yi.
kwakukuludi;
Kale lija munatsitsa Mzimu wanu 3. Mlugu amaunikira
Wakuyera; Anthu ake onsewo,
Lero linonso muchite, ulimbike Namachotsa mantha omwe,
Mpingo wanu. Nayeretsa m’njira mbee!

2. Tidza kwa Mulungu Inu, ndinu wa- 4. Anthu osaŵerengeka


chifundodi; Amtamira onsewa,
Mutipatse Mzimu wanu tsopanoli, Nagonjetsa zosautsa
tere lino; Pomtamira Mbuyeyo.
Tikakhale ndi chimwemwe kuti tili
mbike ndithu. 5. Pakufika tsidya lija,
Zotibvuta zonse phe!
3. A! maliro m’Mpingo mwanu kulirira Mfumu yathu yopambana
’balewo Idzatikondwetsadi.
Adasokerera kale ndi zoipa zapa
dziko. 6. Nthaŵi yina adzadzuka
Muwabwezerenso kwanu kuti akakhale Ogonera m’mandamo,
mommo. Kuthaŵatu mphamvu zonse
Zotibvuta pansipa.
4. Ndi chikondi mtithandize kuigwira
nkhondoyi; 205
Mwa kulema ndi kulimba mutipe-
1. TADZUKA mzimu wanga’we
mpherere ife,
Ugwire ntchito zakozi;

53
Kukondwa ukutengedi, 207
Pemphero ulikwezedi.
1. AMBUYE munapatsa tsiku
Limene langopitali,
Pemphero, pemphero,
M’mamaŵa nyimbo zathu zomwezo
Pemphero ulikwezedi
Mukhale nafe nthaŵiyi
Pemphero, pemphero,
Pemphero ulikwezedi.
Mukhale, mukhale,
Mukhale nafe nthaŵiyi;
2. E, nthaŵi ya mamaŵayi
Mukhale, mukhale,
Umtamandire Mbuyeyo,
Mukhale nafe nthaŵiyi.
Nuyese lero ngatitu
Tsiku lakumalizalo.
2. Tipempha kuti Mpingo wanu
Ukhale ponse m’dzikoli;
3. Munkhani zako zonsetu
Mumdima monse muŵaletu,
Unene molungamadi,
Kuŵala kwanu kudzedi.
Nudziŵe kuti Mbuyako
Adziŵa zachinsinsizi.
3. M’maiko monse, zisi zomwezo,
Kuŵala kumafikanso;
4. Pa tsikuli, Mbuyanga ’Nu,
Kupempha sikuleka konse
Munditsogolere m’njiramo;
Kuyamikira Yesuyo.
Ulemerero wanuwo
Undilimbitse monsetu.
4. Pogona ife, amadzuka
Abale akutaliwo;
5. Timlemekeze Mlunguyu
Panthaŵi yonse anthu ena
Wa madalitso onsewo;
Alemekeza Mbuyeyo.
Timlemekeze tonsefe,
Atate, Mwana, Mzimunso.
5. Ufumu wanu, Mbuye Yesu,
Ukhale nthaŵi zonsedi;
206 Magulu onse adzagonje,
1. KRISTU wakuyeratu, Naloŵe m’njira mwanumu.
Kristu wakuŵalayo,
Wolungama mdzuketu, 208
Muingitse mdimawo.
1. MUKHALE ndine, dzuŵalo laloŵa,
Dzuŵa lathu m’Mwambamo
Wagwa usiku, bwenzi lindisoŵa;
M’wale m’kati m’mtimamo.
Ndilibe wina wakundithandiza,
Wamphamvu ndinu, mkhale ndinetu.
2. Konse kuli mdima bii
Kosakhala Inutu;
2. Kamoyo kanga katha lero lino,
Nlosakondwa tsikuli
Zidzachokanso zinthuzo za dziko;
Mosaŵala Inu ’mu.
Zimasinthika zonse zooneka,
Ndionetu m’katimo
Simusinthika, mkhale ndinutu.
Mwakuŵala kwanuko.
3. Koma kalelo mnakhalitsa pano,
3. Mudze, mloŵe m’mtimamu,
Mukhale ndine, msandichokerenso,
Mchotse monse mdima bii;
Sin’pempha kuti Mbuye mungotsotse,
Mdzaze ndi kuyeraku,
Komatu mukhalitse ndinetu.
Mchotse zosamverazi;
Ndi kuyera kwanuku
4. E, tsiku lonse Inu ndifunitsa;
Ndikaone bwinotu.
Ndi mphamvu yanu yokha ndisungika;
Mukatsogola ndidzadikha m’mtima;

54
Usiku, msana, mkhale ndinetu. Alotemo mbee;
Anthu aulendo
5. Adani sindiopa mukalipo Msungesungebe.
Muletse tsoka ndi chisoni chino;
Ikadza imfa n’dzalimbika m’mtima; 5. Mutonthoze mtima
M’moyo ndi m’imfa mkhale ndinetu. Wopwetekawo;
Akutsata tchimo
209 Mletse onsewo.
1. ATATE ndiyamika, mwandisama-
6. Wonsewu usiku
lira leroli;
Andisunge ’ne
Mulungu wandikonda, mndisungenso
Amithenga anu
m’mdima muno bii.
Akuyera mbee.
2. Mundikumbutse, ndikapanda tulo, za
7. Ndidzukanso m’maŵa,
Kumwambako;
Kucha koti mbuu,
Zoganizira zoipitsa m’mtima
Ndiyeretu mtima
muchotseremo.
M’maso mwanumo.
3. Zochimwa za usana uno mndikhulu-
8. Titamadi ’Tate,
lukire ’ne;
Mwana wakeyo,
Mtendere wanu muloŵetse m’mtima
Mzimu Woyeranso,
ndikagone phee.
Nthaŵinthaŵizo.
4. Mundilimbitse ndikayese manda
ngati mphasayi, 211
Nditagonamo ndikadzuke tsiku 1. DZUŴA lapita,
lomalizalo. Dzuŵa lapita,
Mlungu, mutigonetse phee.
5. Tiyamike Mlungu wotipatsa
zachifundozi, 2. Mdima wafika,
Amyamikire onse a Kumwamba ndi Mdima wafika
apansipa. Mutisunge tonse bwino.

210 3. Tibvomereze,
Tibvomereze
1. DZUŴA lapitira,
Zakuchimwa zathu zonse.
Wadza mdimawo,
Mthunzi wamadzulo
4. Mkhululukire,
Wagwa m’mwambamo.
Mkhululukire
Zoipa zathu zonse.
2. M’mwambamo nyenyezi
Zithwanima mbee;
5. Lero tigone,
Zonse zili m’tulo
Lero tigone,
Pansi pali duu.
Tigonemo mumtendere.
3. Yesu mutipatse
6. Ndife ananu,
Tulo toti phee;
Ndife ananu,
Ndi mdalitso wanu
’Tate Mlungu wotikonda.
Mndigonetse ’ne
7. Aleluya!
4. Mpatse ana ’ng’ono

55
Aleluya! Mtiukitse m’maŵa kwanu,
Aleluya, Aleluya! Mpatsenso zoyerazo.

212 214
1. MADZULO aja kalelo 1. MULUNGU wanga, Dzuŵatu
Odwala anagona duu; La mtima wanga ndinudi;
Opwetekedwa nthendazo Palibe mdima ngatitu
Munachiritsa Inutu. Mukaŵalira inedi.

2. Tsopano lino kwada bii, 2. Muchotse zonse zoti bii


Nafenso timva m’mtimamo; Zobisa nkhope yanuyo;
Simuoneka, komatu Mudzazetu mtimangawo
Tidziŵa muli nafedi. Ndi kuunika kwanuko.

3. Wopulumutsa mudzetu; 3. Madzulo ano mkhaletu


Adwala ena m’mtima bii, Pafupi ndine, Yesudi;
Ena sakukondani ’Nu, Ndisanagone tuloto,
Ena sasamalira ’yi. Ndilingalira Inudi.

4. Ndi ena sanamvera ’yi 4. Kapena wina leroli


Enanso alemedwatu, Wasokerera m’njirayi
Zoopsya nazo tifadi; Ya Inu Mbuye, mbwezetu,
Mukadza tidzaposatu. Mumpulumutse iyedi.

5. Wopulumutsa, Inunso 215


Munasauka kalelo;
1. LERO mwatipatsa moyo,
Muona zoda m’mtimamo
Wadza mdima, kwada bii;
Tibisa ndi manyaziwo.
Mtigonetsetu usiku,
Mchotse zakuipazi.
6. Mutichiritse ifenso,
Yesu mutisunga ife;
Mutiphunzitse zanuzi;
Tidzakhulupirabe.
Timve tsopano mawuwo
Yesu mutisunga ife;
Ochiza nthenda yathuyi.
Tidzakhulupirabe.

213 2. Ndife anthu aulendo,


1. MPULUMUTSI, tikagona Tili ndi adaniwo;
Mtidalitse m’mtimamo; M’manja mwanu mtigonetse,
Tingolapa zakuipa, Mtichotsere manthawo.
Muzichotse zonsezo. Ndipo pakumuka ife,
Kukadetsa bii usiku, Kwanu tidzapumabe.
Inu mutipenya ’fe; Ndipo pakumuka ife,
Simulema, simugona; Kwanu tidzapumabe.
Anthu anu msungabe.

2. Atipsinjadi masoka,
216
1. KWACHA lero kwati mbee,
Mibvi iponyekatu;
Tsiku la Mulunguli;
Atisungadi angelo,
Dzuŵa liŵaliradi
Moyo mutipatsa ’Nu.
Thambo ndi zapansipa
Ngatitu usiku uno
Upumira mpweyawu
Ikabwera imfayo,

56
Wa Mulungu konseku.

2. M’nyumba yanu, Mlungu, ’yi


218
1. DZUŴA la Mulungu
Tisonkhana teretu,
Ladzatu labwino;
Ndi mitundu yonseyi
Ndi chimwemwe ife
Tikulambireni ’Nu:
Tiliona lero.
Yesu Mbuye wathuyo
Lithaŵitsa nkhaŵa,
Ndiye Mfumu ponsepo.
Lichotsanso mantha
Ndimo m’mtima mwathu
3. Inu Mlungu kalelo
Likhalitsa bata.
Mutalenga zonsezi
Munapuma tsikulo;
2. Tikondwera kuti
Tipumadi ifenso.
Tipumula lero;
Mommo tilandiratu
Tazileka ntchito
Zopumitsa mtimawu.
Kuti tipemphere.
Koma ntchito zathu
4. Yesu munadzukanso
Za palero lino
M’manda lero lomwetu;
Nzakumvera Yesu,
Ntchito munayambayo
Kumlandira bwino.
Yakudzutsa anthu ’fe,
Kuti ndi mitimayi
Tigwirebe ntchitozi. 219
1. NDI lokoma m’Mwambamo,
Mbuye, Bwalo lanulo;
217 Ndi mwabwino muli ’Nu
1. AMBUYE, tasonkhana
Dziko losachimwali;
Tsiku lino lopatula,
Mtima wana wonsewu
Tidzapembedza Inu
Umakhumba m’Mwambamo
Tsiku lino lopatula.
Nkhope ya Mbuyathuyu,
Bwenzilo lakufatsa,
Mlungu wa chisomoyo.
Mbweretu kutipatsa
Mtima wakumvesetsa
2. Zimbalame zonsezi
Tsiku lino lopatula.
Zimayamikira ’Nu;
Anthu amakondwanso
2. Sitinanyalanyaza
Okhumbira m’Mwambamo;
Tsiku lino lopatula.
Njiŵa yosapumayo
Tigwadirira m’mantha
Inafika m’chombocho;
Tsiku lino lopatula.
Okhulupirira ’Nu
Mbwezetu maganizo,
Amapuma kwanuno.
Mtimvetse malangizo;
Tchimo mufafanize
3. Anthu opembedzawo
Tsiku lino lopatula.
Amakondwa m’mtimamo;
Munapatsa madzitu,
3. Timvere Mawu anu
Munagwetsa manawo;
Tsiku lino lopatula
Mumakoma mtimatu
Muŵadalitse ndithu
Tidzayamikiratu,
Tsiku lino lopatula.
Pachimpando chanucho
Mtiperekeze kwathu,
Mkhale Mfumu yathudi.
Msunge mitima yathu;
Mpatse chisomo chanu
Tsiku lino lopatula. 220

57
1. YESU mkhale nafe Wolemereroyo.
Nthaŵi yomweyi, Mulungu wa makamu ndiye,
Kuti mphamvu zanu Wolemereroyo.
Tilandirezi.
Aleluya, aleluya, aleluya, aleluya,
2. Mzimu Wakuyera aleluya.
Mutipatsetu, Amen, amen, amen.
Mtima wathu wonse
Usakhale duu. 223
1. MLUNGU ali muno,
3. Moyo watsopano
Tonse timgwadire,
Ulimbitse ’fe,
Mantha omwe timchitire;
Mlungu wathu yemwe
Ali mukachitsi,
Timdikirabe.
Tonse tili chete,
Ndi ulemu timpembedze;
221 Ndiye yekha Mlungu wathu
1. ANTCHITO a Mulungu ’nu Atipulumutsa,
Olinda m’nyumba mwakemo. Tidzamlemekeza.
Myamike, muimbiretu
Mlungu Mbuye wathuyo. 2. Mwini madalitso,
Mndikonzere m’mtima,
2. Mugwade pansi m’nyumbayo Mbuye, ndingokhulupira.
Mpembedze nonse Mlungutu; M’Mwambamo angelo
Mugadamire m’mwambamo. Agwadira inu,
Mtamande Mbuye wanutu. Ife tigonjanso kuno;
Mpingo wonse uchiitse
3. Yehova adalitse ’nu, Chifuniro chanu.
Ndiye wachifundocho, Ponse pansi pano.
Asunge moyo wanuwu;
Amtame anthu onsewo. 3. Yesu Mbuye wanga,
M’khale m’mtima mwanga,
222 Ndiwotu kachisi wanu.
Ikafika imfa,
1. KWEZANI mitu yanuyo,
Mundisunge kwanu
Zipata zamuyaya,
Kuli inu ndi angelo.
Ikaloŵemo Mfumu ya
Moyo wanga ulimbike
Ulemereroyo!
Kufikira ine
Amfumu awa ndaniko?
Ndidzakupenyani.
Ambuye ndiyeyo,
Mulungu wogonjetsa onse,
Wolimba mphamvu njo! 224
Mulungu wogonjetsa onse, 1. MTSINJE woyerawo
Wolimba mphamvu njo! Wotuluka m’nyumbayo
Ya Mlungu wathuyo
2. Tatsegukani inutu, Uyeretse tonsefe.
Zitseko zosathera,
Amfumu akumwambako Ife tifikeko
Aloŵe mwanumo. Tibatizidweko,
Amfumu awa ndaniko Tiyeretsedwedi
Wolemereroyo? Ndi Ambuye leroli.
Mulungu wa makamu ndiye,

58
2. Mwa anthu onsewo Zomera m’mundawo;
Umayenda mtsinjewu, Mumtima mutidyetsedi,
Nuŵachiritsadi Tikule bwinomo;
Okhulupirirawo.
4. Ndi kutsukidwa m’mwazimo
3. Tikondwereratu Mumtima mwathu mbee,
Pakumvera Yesuyo, Tionetsedwe konseko
Abwere onsewo A Mlungu ana ’ke.
Ndi kuloŵa m’mtsinjewu.
227
225 1. USIKU uja kalelo
1. ATATE, muwapenya Anampereka Yesuyo,
Anzathu ali pano, Usiku womwe m’manja mbuu
Abvomereza Inu ’Natenga mkate Iyeyo.
Ambuye Mfumu yawo;
Alonjezetsa lero 2. Natamandira Mlunguyo
Kutsata Mbuye onse Wolamulira pansipa,
M’ŵathangatire iwo Natema mkate, natitu
Asabwerere konse. Kwa omwe anatsatawo;

2. Tsopano alandira 3. “Ndi thupi lopatsidwali


Chizindikiro chanu La Ine, mtenge, mudye, ndi
Munachiika ndinu Muchite ichi nonsenu,
Cha Ubatizo wanu Ndi chikumbutso changatu.”
Mulembe dzina lanu
M’mitima mwa onsewa; 4. Ndiponso m’manja chikhocho
M’ŵabatizenso Mbuye, ’Nakweza, natamandamo
Ndi Mzimu Wakuyera. Mulungu, mtima wake mya,
Nanena mawu omwewa:
3. Muŵalimbitse onse
Akhazikike m’mtima, 5. “Chikho cha mwazi wangachi
Akhale chikhalire Chitsuka mtima woda bii,
Oyera ndi olimba; Cha mapangano omwewo
Mutithandize tonse Chisomo cha Kumwambako.
A Mpingo wa Mulungu
Tikhale oyenera 6. “Chikho cha mwazi wangachi
Ndi okondana ndithu. Chitsuka mtima woda bii,
Cha mapangano omwewo
226 Chisomo cha Kumwambako.
1. MONGA zomera zonsezo
Zikula ponsepo, 228
Mulungu mumeretsazo, 1. SINDILI woyenera ’ne,
Momwemo anawo. Ambuye, kudzamo;
Munene mawu, ndimvebe
2. Munali mwana, Yesu ’Nu Okondweretsawo.
Wamng’ono kalelo,
Ndi munakula m’msinkhu ndi 2. Sindili woyenera ’ne,
Kutama ’Tatewo. Mumtima mwanga zi;
Munene, ndikachiradi,
3. Ndi ife tinga, mbewuzo Ndilibe moyo ’yi.

59
5. Tadzanitu, okhulupiradi,
3. Sindili woyenera ’ne; Talandirani zachinsinsizi.
Pamtanda panupo
Munamaliza mlandu phe 6. Ndiye wa moyo wonse Mwiniyo,
Ndi mwazi wanuwo. Moyo wosatha atipatsa ’fe.

4. Ndilaŵako tsopanoli 7. Ndiye wodyetsa anthu omwewo,


Zakudya zanuzo; Napatsa mwazi, moyo wakewo.
Mudzaze mtima wanga ndi
Kukonda kwanuko. 8. Yesu Mbuyathu, Inu nomwe ’Nu,
Tsopano mkhalebe ndi ifetu.
229
1. MONGATU mawu anuwo, 231
Ndi Mtima chete phee, 1. MOMMUNO, Mbuye tionanetu,
Mbuyanga kufa kwanuko Mommuno ndizikhudza zanu phee,
Ndikumbukire ’ne. Mommuno zachinsinsi zanu mbuu,
Mwa Inu mtima ndipumirabe.
2. Chakudya chakumwambachi
Ndi thupi lanudi; 2. Mommuno, Mbuye, mkate wanuwu,
Chikho cha chipanganochi Mommuno vinyo wakumwambako,
Ncha mwazi wanuwo. Mommuno zolemera zanga du,
Chisomo chanu ndidzalaŵanso.
3. Getsemane ndionako
Ndi nkhope yanu dwii, 3. Ndilibe wondithangata ‘ne ’yi,
Thukuta la pamphumilo Ndilibe wina wondisunga ’ne;
La myazi yanuyi. Zikwaniratu mphamvu zanuzi,
Ine, Ambuye, mphamvu nzanudi.
4. Ndi mtanda uli m’maso mbuu,
Ndiona m’menemo, 4. Tsopano nthaŵi yake phwandoli,
A Yesu kufa kwanuko, Loyala ili m’gome mwanumu;
Kuthetsa imfazo. Ndidye ndimwere zakukomazi,
Ndiyanjanabe nanu, Mbuyathu.
5. Pamene padzakhalapo
Milomo yanga phee, 5. Chakudya ichi chidzapita du,
Mukadza ndi Ufumunso, Chizindikitsa za Kumwambazo;
Mukumbukire ’ne. Zosapitazo tidzalaŵatu,
Za Yesu mwini wakukondako.
230 6. Tikadya phwando zaka zonsezi,
1. MUDZE, anthuni, talaŵani ’nu
Ndipo zakudya zimalozatu
Mkate ndi chikhocho cha Mbuyathu.
Kuphwando lija la Kumwambako,
Komwe tidzadya kwa Mulungutu.
2. Khristu ndi mwini moyo wathuwu,
Pamtanda anafera ifetu.
232
3. Anatifera nsembe Iyeyo, 1. NDIMAMVA njala, Yesu,
Ndiye Wansembe wake Iyenso. Ya mtima wakusoŵa;
Mdidyetse ngati mana
4. Imfa ndi mdima zinathaŵa zii! Anagwa m’chipululu.
Ndipo chisomo chikuŵala mbuu.
2. Ndimamva ludzu, Yesu,

60
Muloŵe mwanga lero; Munjira monsemo;
Mndimwetse ngati madzi Ndithangateni ine
Anatuluka m’mwala. Ndisalefuke ’yi;
Mundilandire m’Mwamba
3. Ndi mkate wanu, Yesu, Ndikamwaliradi.
Ndi thupi lobvulala,
Mndilimbikitse, Mbuye 234
Mundikhutitse mtima.
1. MUNDIMVERE, Mbuye wanga
Nkana ine ndimalakwa,
4. Mwa chikho chokumbutsa
Koma ndinu moyo wanga;
Chikondi chopambana,
Mbuye, mkhale ndine.
Mndipatse moyo wanu,
Ndikayanjane nanu.
2. Ndine mlendo pansi pano,
Msanditaye m’dzanja lanu,
5. Mndidyetse m’chipululu
Mundisunge mwana wanu;
M’ulendo wanga wonse;
Mbuye, mkhale ndine.
Mdimwetse, ndipirire
Osalefuka konse.
3. Munafera ine kale
Kuti mukandimasule,
233 Lero lino mndinyamule;
1. A!YESU, ndapangana Mbuye, mkhale ndine.
Kutumikira ’Nu
Ndi moyo wanga wonse, 4. Mundidzaze ndi chikondi,
Mbuyanga ndinutu; Mndiyeretse m’mtima monse,
Mukhaletu pafupi Chifuniro changa mthyole;
Masiku onsewo, Mbuye, mkhale ndine.
Sindidzaopa konse,
Mutsogolereko. 5. Imfa ikandifikira,
Inu ndidzakangamira
2. Ndikufuna kumva Inu, Ndikaloŵa ine m’mdima,
E, Mawu anuwo, Mbuye, mkhale ndine.
Ndisamve za satana
Zonyenga zakezo; 235
Adani anga onse
1. ANU Mbuye ndifetu!
Andizingiratu;
Mutimvere kwanuko;
Mukhaletu pafupi,
Anu tikhalirebe
Mundithangate ’Nu.
Kuno ndi Kumwambako.
3. A! Yesu mwapangana
2. Anu Mbuye ndifetu!
Ndi anthu anuwo
Mwanu tipumiredi;
Adzakhala ndinu
Ndinu Mbale wathu ’fe,
Ku Dziko lanulo;
Mutusunge nthaŵizi.
Inenso ndapangana
Ndisabwerere ’yi;
3. Anu Mbuye ndifetu!
Mndipatse mphamvu yanu
‘Dikireni tonsefe;
Ambuye ndinudi.
Moyo ndinu, n’choona,
M’njiramo tiyendebe.
4. Mundionetse, Yesu,
Mapazi anuwo,
4. Anu Mbuye ndifetu!
Ndidzapondera awa
Ndife nkhosa zanuzi;

61
Mwanu tibisalemu, 3. Ife tonse tichenjere
Mwanu mosungikadi. Tingadzachite zomwezo:
Tisaname ndi kunena:
5. Anu Mbuye ndifetu! “Zopereka ndinapereka.”
Tsogolani nthaŵizo;
Mtiyendetse m’moyomu 4. Mulungu akondadi leroli
Kunkabe Kumwambako. Wopereka mokondwera;
Tikapereka motero
236 Tidzalandira dalitso.
1. AMBUYE, Mwini zonsezi,
Ulemu tiperekadi; 238
Chikondi tionetsanji? 1. MBUYE wathu, mutipatsa
Mwapatsatu. Zonse tili nazozo,
Mutikomeratu mtima
2. Dzuŵa ndi mvula yonseyo Osaleka konseko,
Ndi mame mwatipatsanso, Mutikonda, mutisunga,
Masika ’dzera kwanuko; Mutisamalira ’fe.
Mwapatsatu.
2. Dzuŵa, madzi, kudya, mpweya,
3. Mwapatsa Mwana wanu, ndi Moyo, zonse nzanuzi,
Mwapulumutsa dzikoli; Si za ife, nzaulere,
E, zaulere zonsezi Tingozilandiradi;
Mwapatsatu. Zifumira kwa Aate
Wotikondakondatu.
4. Tibwezeretu bwanjiko
Ziperewera zathuzi; 3. Monga tilandira, Mbuye,
Ndi moyo tili nawowo Mtiphunzitse tonsefe
Mwapatsatu. Tipere chuma chathu
Ndi kusangalalatu;
5. Ambuye zathu zonsezi Zakukhala m’manja mwathu
Kwa Inu tibwezeredi; Tiziyese nzanudi.
Tingopereka zanuzi,
Mwapatsatu. 4. Tikhaletu nawo, Mbuye,
Mtima wosauma ’yi
237 Ndi wofatsa ndi wabwino
Ndi woyerayeradi,
1. PETURO ’nafunsa Hananiya:
Kuti tiyenere Dzina
“Zopereka zili kuti?”
La Mbuyathu Yesuyo.
Hananiya ananena:
“Zopereka ndinapereka.”
5. Tisaiwalire ’bale
Athu osadziŵa ’Nu,
Munthu aganize
Akulira ndi odwala
Zimene anachita Hananiya
Tiŵapemphereratu;
Munthu aganize
Titsanzenso Mbuye Yesu
Njira yakuunika.
Ndi k’ŵathangatira ’wo.
2. Mbiri ya Hananiyayo
6. Dalitseni, Mbuye, zonse
Inali yodabwizatu;
Zomwe taperekazi,
Ananyengatu Peturo;
Mzilandire, nsembe yathu,
“Zopereka ndinapereka.”
Mziyeretse Inudi

62
Ndi mitima yathu yonse Poimba nyimbo zawozo.
Tikuyamikirani.
4. Ufumu wake udalitsa
239 Osauka onsewo;
Otopa amapuma chete,
1. POLENGA dzikoli
Magoli amathyoka thyo!
Pakumva Inudi,
Kwayeratu;
5. Zolengedwa zonse zidze
Mumve pempheroli,
Kugwadira Mfumu yathu,
Ndipo pamenepo
Amlemekeze akumwamba,
Palibe mawuwo,
Tiimbe pansipa; Amen.
Muŵaletu.

2. Inu wakudzatu 241


Kuŵachiritsadi 1. ANTHU akum’maŵa
Anthendawo, Nanka msangako,
Kupatsa moyowo, Nzeru ’nali nazo,
Kuona m’masomo, Nafatsansowo;
Pa anthu onsewo Nanka kuli Mwana
Muŵaletu. Anabadwayo;
Anatsogozedwa
3. Mzimu woonadi Ndi nyenyeziyo.
Ndi wachikondicho,
Idzanitu; 2. Anapeza Mwana
Muunikirepo Ali m’kholamo,
Pali zamdimazo, Nagwadira Iwo
Pa dziko ponsepo Mbuye wawoyo;
Muŵaletu. Anthu onse omwe
Ali pansipa,
4. Inu atatuwo, Azitsata Mbuye
Wodala Mlunguyo, Ndi nyenyeziyo.
Timveretu;
Pa dziko ponsepo 3. Mu ulemerero,
Muchotse mdimawo, Yesu m’Mwambamo
Mutume Mawuwo, Muli eni ake;
Muŵaletu. Anthu onsewo
Osadziŵa konse,
240 Akutalinso,
Akokedwe iwo
1. ADZAPAMBANA Yesu ponse
Ndi nyenyeziyo.
Pakuyenda dzuŵalo;
Adzamverabe namgwadira
4. Akukhala kunja,
Pa dziko lonse pansipa.
Osokeranso,
M’ŵaŵalire Mbuye,
2. Sadzalekeza kuyamika
Asagone’wo;
Ndi kuimbaimbabe;
Amumdima omwe,
Adzapemphera nsiku zonse
Olemedwanso,
Natchula Dzina lakelo.
Mtsogoleri wawo
Ndi nyenyeziyo.
3. Pomveka konsekonse mbiri
Yake ya Wokondayo,
5. Paulendo wathu
Ang’ono akwezanso mawu

63
Tili pansipa, Woti nji paphiripo
Muŵalire tonse Mbiri yanu, mbiri yanu
Tili m’njiramo; Ibukitse ponsepo.
Mutitsogolere
Anthu tonsefe, 3. Ponse padakhala mdima
Mutifitse tonse Pakaŵale dzuŵali;
Ndi nyenyeziyo. Kumalire konsekonse
Muthaŵitse mdima bii!
243 Mpulumutsi, Mpulumutsi,
Muyeretse zonsezi.
1. ZIPATA zachitsulo zitseguke
zonse mbee!
4. Ibukitse mbiri yanu,
Ambuye wa Kumwambako aloŵe
Ifikire konseko,
momwemo.
Iŵagwire anthu mtima,
Iŵathyole m’katimo
2. Mbendera yake ikupiza
Mphamvu yanu, mphamvu yanu,
m’mlengalengamo,
Idziŵike konseko.
Kufana ndi nyenyezi younika
m’mdimamo.

3. Ankondo a Mulungu ’nu, 245


Yendani m’njiramo,
1. MBWERE Mlungu Mbuye
Mitima yanu yonseyo iyeretsedwe
wathu,
mbuu!
Msunge zakuonazo,
Mudalitse anthu onse
4. Tsatani Mbuye Yesuyo ndi
Ndi chifumu chanucho.
mtanda wakewo;
Mlaliketu Uthenga kwa anthu
2. MMbwere Yesu Mwini moyo,
onsewo.
Ukuletu ’lemuwo;
Gonjetsani anthu onse,
5. Musamaopa kanthu ’yi tamani
Mpatsenso mtenderewo.
Yesuyo;
Kaimbireni nyimboyi ndi
3. Mbwere Mzimu Wakuyera,
mphamvu zonse.
Mutitsitsimutseko;
Muthaŵitse mdima wonse,
6. Zipata zatsegudwa mbee! za
Muŵalitse m’mtimamo.
m’dziko monsemo;
Ambuye wapambanatu ndi
4. Anthu onse taukani,
mtanda wakewo.
Imbirani Mlunguyo;
Zichuluke zomtamanda
244 Pansi ndi Kumwambako.
1. PAMAIKO pali mdima,
Penya mtima chetetu, 246
Leroli malonjezano
1. ANYAMATA a Mulungu,
Angokwaniridwatu.
Muzigwira nkhondoyo,
Kondwerani, kondwerani,
Mumenyane ndi Satana
Yesu mulitsetu.
Mzimu wakunyengayo.
2. Adze amitundu yonse,
2. Komwe asauka anthu
Adze akutaliwo;
Akukhala m’mdimamo
Ayang’ane mtanda uja

64
Osadziŵa Mpulumutsi, Ndidziŵitse nzeru zanuzo;
Phunzitsani konseko. Munole mibvi yangayi,
Ipyole yonse m’mtimamo.
3. Pomangidwa anthu nayo
M’yambo yoipitsayo, 5. Ndipumulire panupo,
Pomwe amaopa chabe, Ndinene motonthoza phe!
Masulani golilo. Ndi mawu opumitsawo
Olema ndikanenebe.
4. Walitsani nyali yanu
Ikachotse mdima bii! 6. Ambuye, ndi chikondi tho!
Mpaka ikainga zonse Mudzaze mtima wangawu;
Zosautsa m’dzikoli Ndinene zachikondicho,
Ndiyamikire monsemu.
5. Akutopa ndi ofoka
M’ŵatonthoze mtima phee! 7. Ndichitireni, Mbuye ’ne,
Osokera, onyozeka Monse mufuna mwanumo;
Muŵafunefunebe. Kumwamba tionane mbee,
Maso ndi maso kwanuko.
6. Achisoni obvutidwa,
M’ŵathandize msangatu; 249
Zosautsa zawo zonse
1. MULUNGU wa Kumwamba
Yesu azichotsadi.
bwera kunoku
Ndi mtima wokondwera kuloŵa
7. Anyamata limbikani,
m’nyumbayi;
Gwiranitu nkhondoyi;
Chifukwa cha zabwino
Yes salephera mwini,
mwatichitirazi
Sitiiŵalira ’yi.
Tikukuyamikirani leroli.
8. Isaleke ntchito yake
Inde, tikuyamikani, Atate, leroli,
Mpaka anthu onsewo
Mwatimangira ’fe kuno kachisi
Alambira Mfumu yathu,
wanuyu!
Nagonjera konseko.
Ndi ulemerero wanu mudzaze
m’nyumbayi;
248 Muyeretse, mudalitse munomu.
1. MUNENE Mbuye, ’nenetu,
Nditsanze mawu anuwo; 2. Tikondwa tonse ndi
Munandifuna Inetu, kukuthokozani ’Nu
Ine ndifune zanuzo. Poyamba kupemphera ndi
kuimbiramu;
2. Nditsogolere m’njirayi Mommuno nsiku zonse mukhale
Nkhosazo zisokerazo; nafetu,
Ndidyetse Mbuye, zanuzi Monga ndi angelo anu
Zimene zifa njalayo. m’Mwambamo.

3. Ndilimbikitse, Mbuye, nji! 3. Ikhale ngati nyali yoŵala


Pamwalapo ndiimebe; nyumbayi,
Onse alibe mphamvu ’yi Yakutsogoza onse ophunthwa
Omwe ndithangate ’ne. m’mdima bii;
Akunja ndi Akristu
4. Ndiphunzitseni, Mbuyetu, m’ŵapulumutse ndi

65
Kuunika kotuluka munomu. 252
1. YEHOVA Mlungu wathu,
250 Amene mumapatsa
1. KRISTU ndiye Mwala wathu, Zipatso za chikondi
Kristu timangirapo; Polenga anthu anu,
Wosankhidwa ndi Mulungu, Mupatse awa ‘ŵiri
Atimange tonsefe; Mitima yokondwetsa,
Iye ndi Mthandizi wathu, Yofana m’munda muja
Timkhulupirira ’Ye Munayendamo kale.

2. Mudalitse nyumba yathu; 3. Mbuyathu wokondedwa,


Mbuye, nthaŵi zonsetu Pokhala m’dziko muno
Muthandize anthu onse Munadza ku ukwati,
Odza kuphunzira ’mu, Naŵadalitsa onse;
Ndi antchito anu omwe Ukwatiwu mukonze,
Odza k’ŵaphunzitsa ’mu. Mukhale nafe pano;
Iwowa m’ŵadalitse
3. Tiyamike Mlungu ’Tate, M’chifundo chanu chonse.
Tiyamike Mwanayo,
Tiyamike Mzimu wake; 4. Ndi Mzimutu Woyera
Onse omwe Mmodzitu, Mufike nayo mphamvu,
Waulemerero wonse Mukatsangane nawo
Ndi wamphamvu ponsepo. Akupangana omwe;
Mupatse ’wo chisomo
251 Chokometsetsa mtima;
Chikuletu chikondi
1. ANAKWATIRA kale
Chitsazo nchanu chomwe.
Pa Eden pajapo;
Ulipo lero lino
5. Mulungu mwa Atatu,
Mdalitso womwewo.
Atate, Mwana, Mzimu,
Tikhaletu wokondwa
2. Aŵiri aimamu,
Ndi Inu m’chiyanjano;
Mwamuna ndi mkaziyu;
Titama Inu Mlungu,
O! Mzimu Wakuyera,
Wokonda ife ndinu;
Mdalitso mpatsetu.
M’ulendo wathu wonse
Tiyende m’chikondano.
3. Mulunzanitse awa,
Atate, leroli;
Munakwatits’ Adamu 253
Ndi Hava kalelo. 1. MULUNGU wa Yakobo Inu,
mdyetsa anthu anu,
4. Mukhale nawo, Yesu, Kalelo munatsogolera makolo
Mongatu kalelo athuwo.
Ukwati mnadalitsa
Pa Kana pajapo. 2. Tsopano tipereka mapemphero
athu ano.
5. M’ŵasunge, m’ŵayendetse Mulungu wawo mukhalenso
Munjira yanuyo, Mlungu wa anawo.
Akhale ndi kudala
Pabanja pawopo. 3. Tikasokera m’njira mutilondolere
ndithu,

66
Chakudya ndi chobvala mutipatse 255
tsiku n’tsiku.
1. MBUYE, tikuthokozani,
Ndinu mwatitsogolera;
4. Mtifungatire ndi mapiko
Zaka zonse mwatisunga;
paulendo pathu,
Tiyamika mokondwera,
E, tikafike okondwera kwa Atate
Zotibveka, zotidyetsa,
wathu.
Mphamvu, moyo, zonsezi;
’Tate tikuthokozani
5. Tipempha madalitso ano mpatse
Chaka chatsopanochi.
ife tonse;
Tisankha Inu ndinu Mlungu wathu
2. Ndinu mwatithangatira
nthaŵi zonse.
Pakuona zosautsa;
Polefuka ndi podwala
254 Ndinu mwatitsitsimutsa.
1. MLUNGU wathu mwatifitsa Munatiteteza bwino
Kufikira leroli; Tili ana kalelo,
Moyo wathu munasunga Ndipo zomwe mwazichita
M’njira yonse yathuyi; Chaka chotitheracho.
Mtsogoleri wathu ndinu
Paulendo pomwepo 3. Chaka chino mutipatse
Tingakutameni bwanji Mphamvu zosachimwa konse,
Kaamba zonse zanuzo? Zoipitsa ndi zodetsa
Mtima mtichotsere zonse.
2. E! Chisomo chosaleka Mtithandize tizimvera
Tachiona kalelo; Kuyambira leroli,
Masungidwe ndi chikondi Ndi kugwira ntchito zanu.
Zikalimo momwemo; Chaka chatsopanochi.
Pausana, pausiku,
Muli nafe ponsepo; 4. Inde,’Tate, mtiyendetse
Madalitso anu omwe M’njira yolungama yanu,
Tiri ndi ambiriwo. M’mtima mwathu mtiyeretse
Kuti tikondane nanu.
3. Tinayenda muli mdima Zaka zonse muli nafe,
Wotidetsa nkhaŵawo, Sitiopa konse ’yi
Pena tinangosauka ’Tate tikuthokozani
Ndi zobvuta zathuzo; Chaka chatsopanochi.
Koma Inu munalimo
Mumitambo yomweyo, 256
Nafe tinathandizana
1. TILIMALIMA m’minda,
Ndi mdalitso wanuwo.
Tibzala mbewu zathu,
Komatu zibvumbidwa
4. Ena atsagana nafe
Ndi Mlunguyo wamphamvu.
Natsiriza njirayo,
Dzuŵalo aŵalitsa
Nafikira kuli Inu,
Namatumiza mphepo,
Natilindirirako;
Mbewuzo nameretsa
Tithadi ulendo wathu
Mulunguyo wabwino.
Ndi kupita komweko,
Mutitsogolere ’Tate
Mphatso zonse zathu
Kukuŵala kosatha.
Zifuma kwa Mulungu,
Tilemekeze Mbuye wathu,

67
Atikondadi. Anthu anu onsewa
Muŵapulumutse ’wo;
2. Wolenga ndi Yemweyo Zopweteka zawozo
Wa zinthu zonse zathu; Ziŵathere zonse phe;
Maudzu ameretsa, ’Dzani mu Ufumu ndi
Nayatsanso nyenyezi. K’ŵasonkhetsa onsewo.
Mphepo zonse zimva,
Nyamazo aziŵeta; 258
Sadzaiŵala konse
1. OYAMIKA Mlungu mbwere,
Anake kuŵadyetsa.
Za masika mudzaimbe;
Dzinthu zathu takolola,
3. Tiyamikira ’Tate,
Sizionongeka m’minda.
Zabwino zonse zino,
Mlungu Mlengi asamala,
Kubzala ndi kukunkha
Zotisoŵa akonzera;
Ndi moyo tili nawo.
Mloŵe m’nyumba ya Chauta,
Kuninkha Inu Mbuye
Mkweze nyimbo zamasika.
Tilibe mtulo wina,
Komatu tipereka
2. Dziko lonse nla Mulungu
Mitima yoyamika.
Kuti limbalire dzinthu;
M’munda zonse zimamera
257 Zakukoma ndi zoipa;
1. YAMIKANI nonse ’nu, Mmera udza, bwino ngala,
Pomwimbira nyimbozi Maso omwe amakhwima;
Za masika athuwa; Mutilole, Mwini dzinthu,
Potumiza mvulayi, Tikakhale dzinthu zanu.
Mlungu wathu yemwedi
Atipatsa zonsezi; 3. Adzabwera Mbuye wathu
Timwimbire m’nyumbayi Kukolola dzinthu zawo;
Za masika athuwa. M’munda mwawo akachotse
Minga ndi zoipa zonse.
2. Dziko lathu lonseli Adzatumanso angelo
Nla Mulungu yemweyu; Minga akaponye m’moto,
Atumiza mphatsozi Koma tirigu amsunge
Zakutilimbitsadi, M’nkhokwe yake nthaŵi zonse.
Mmera wathu wonsewu,
Mbewu zathu zonsezi; 259
Timtamande Mbuyeyu
1. CHIFUKWA cha zokoma mtima
Wotipatsa zonsezi.
zonse za ulerezo,
Timlambire Mbuye;
3. Nthaŵi yina Mbuyeyu
Tikweze nyimbo yathu
Adzafika pansipa,
yakukondwa kuli ’Ye,
Nadzakonza zonsetu;
Tigwadiretu.
Zosakondweretsazi
Naziponya m’motowo,
2. Dzinja lokondweretsa lafikanso,
Koma m’nkhokwe mwakemo
litapumatu,
Mudzadzala mbewu tho!
Timlambire Mbuye;
Zokomera bwinotu.
Mvula igundanso, Mulungu
wotikonda ’fe,
4. ’Dzani Mbuye msangatu,
Tigwadiretu.
Msonkhanitse zonse phe;

68
3. Dziko lonse lilikukondwa, Akondwere mwa chikondi
mlengalenga mpheponso, Chanucho.
Timlambire Mbuye;
Zapansi pano zonse zimtamandire 4. Mpulumutsi wakukoma,
Mlungu wathuyo, Muŵagwirize;
Timgwadiretu. Nsiku zonse akulemekezeni,
(Akuleme-keze.)
4. Maluŵa abwino aphuka m’mapiri
ndi m’madambomo, 5. Mzimu wanu Wakuyera,
Timlambire Mbuye; Aŵayeretse;
Masamba aŵisi ang’ono Agonjetse ndi chisomo
agwedezekanso, M’nkhondoyi.
Timgwadiretu.
6. ’Tate, Mwana, Mzimu ,ndinu
5. Zanu zapansi nzokoma Mbuye; Mlungu mmodzitu,
Tikondwera ’fe, Muŵasunge m’fupi mwanu
Timlambire Mbuye; Ponsepo.
Koma kwanu Kumwamba komwe
Kwapambanatu, 261
Timgwadiretu.
1. YESU, munditsogoza
M’njira yanga yonseyo;
6. Nafenso tidzadzuka kwa ’kufa
Wakunditsogozatu
ngati maluŵawo,
Ndinu, mundisungetu;
Timlambire Mbuye;
Inde, paulendowo
Oyera mtima adzabvala mbuu! pa-
Mundisunge kolimba.
kudza Kristuyo,
Timgwadiretu.
2. Monga may’asusunza
Mwana wake polira,
7. Tidzakhala naye nthaŵi zonse ndi
Wakunditonthozatu
kuimbako,
Ndinu, munditonthoze,
Timlambire Mbuye;
Ine, m’njira yanuyi
Kumene moyo wa anthu
Munditsogoleretu.
okhululukidwa uli wokomatu,
Timgwadiretu.
3. Mbuye, ndinu wamphamvu,
Mumatola ananu.
Aleluya, Amen!
Anthu onse pansipa
Ali otaikatu;
260 Muchitire chifundo,
1. MLENGI wathuWakuyera, Muŵatole onsewo.
Mutimvere ’fe,
M’ŵasungire akutali, 262
Bwinodi.
1. MLUNGU alinane;
Amadziŵazi
2. Mbuye Yesu, myandikire
Ndizinena, penanso
M’ŵakondwetsebe;
Za mumtimamo.
Mulimbitse mphamvu zawo
Zonsezo.
2. Mlungu alinane
Ndi usikuwo,
3. Akaona masautso
Nandiona momwemo
Mkhale nawodi;
Mu usanamo.

69
Ife anthu muzoipa
3. Mlungu alinane; Zonse tazichita.
Zachinsinsizo
Zosaonekerako 5. Yesu Mfumu
Azidziŵatu. Yesu Mfumu,
Timagonja, mutisunge
263 Moyo wathu wonse.
1. MLUNGU, Inutu,
6. Mutisuke,
Mwalenga dzuŵali,
Mutisuke
Nyenyezi, mwezi mbee,
M’mwazi wanu, tikakhale
Ndi dzikoli.
Ana anu tonse.
2. Koma ineyu
Simuiŵala ’yi; 266
Mundisamala ’ne 1. TIIMBE ndi kulalikira
Ndisagwe ’yi. Mthenga wa chikondicho
Anamva Mlungu m’Mwambamo
3. Mbuye, Msungi ’Nu, Kulira kwathu pansipa.
Mutuma indedi
Za moyo wangawu (Ndikhulupirira Yesu
Zokomazi. Wobadwira m’kholamo;
Iye ndiye Mfumu yathu,
4. Yesu Mwanatu Timtame nthaŵi zonse.)
Anafa imfayo
Achotsa zoti bii; 2. Kwa ife lero anabadwa
Nadzukanso; Mwana wa Mariyayo,
Pamsinkhu, ine mng’ono koma
5. Kuti m’Mwambamo Mwini dziko lonseli.
Ndikatamandetu
Wondisamalabe, 3. Anadza nazo mphatso zake
Mbuyangayu. Anatikonzeratu;
Anatitseguliradi
264 Pakhome pa Ufumuwo.
1. A! MULUNGU
4. Ambuye takutamandani
A! Mulungu
Tsiku lakubadwali,
Anatuma mwana wake
Mwa Inu tonse tikondwera,
Uja, ndiye Yesu
Tiseke tonsefe.
2. Anabadwa,
5. A! Yesu Mbuye wakuyera,
Anabadwa
Munagona m’kholamo;
Ndi Maria Mbeta ija
Mudzikonzere leronso
M’Betlehem muja.
Mogona m’mtima mwangamu.
3. Ndi angelo,
6. Ulemerero m’Mwambamwamba
Ndi angelo
Ndi mtendere pansipa;
Anaimba: “Ndiye Yesu
Tiimbe nafe nyimboyi,
Mpulumutsi wanu.”
Timyamikire Mbuyathu
4. Alanditsa,
(Yesu ndiye Mfumu,
Alanditsa

70
Yesu ndiye Mfumu! Amay’ wake namvabe;
Ndikhulupirira Yesu wobadwira Ndipo ana nonsenu,
m’kholamo.) Mukamtsate bwinotu.

267 4. Ndipo Mwana uyu Yesu


Anakulakulabe;
1. ANA inu, ana inu,
Ndi wamng’ono ndi wofoka,
Taukani ndi kumvera
Anagona enawo.
Amithenga akumwamba;
Nsoni zathu anazimva
Anafika kalelo,
Ndi chimwemwe chathunso.
Natiuza Mpulumutsi
Anabadwa pansipa.
5. Ndi chifukwa atikonda,
Zaka zonse, tsiku lomwe
Tidzampenya masowa,
Umamveka mthengawu.
Kuti Mwanayo wofatsa
Ndiye Mwini m’Mwambamo;
2. M’nyumba zonse ponseponse
Atengera ana ake
Zimamveka nyimbo izi,
Komwe adapitako.
Kuti Yesu anabadwa,
Anagona m’kholamo,
6. Koma sitimpenya m’khola
Anafika Mpulumutsi
Muli ng’ombe momwemo;
Wotikondweretsadi,
Ayi, tidzamwona m’Mwamba
Kondwerani, kondwerani
Muli Mlungu ’Tatewo.
Inu nonse ana ’nu.
Ana akuyera mbuu
Adzamzunguliratu.
3. Taukani, taonani
M’mwamba monse mwakuyera;
Amithenga a Mulungu 271
Aimbabe nyimboyo. 1. KULI kaphiri m’talimo
Yesu Kristu anatsika, Kunja kwa mzindawo,
Anachoka kwawoko; Kwapachikidwa Yesuyo
Lero lonse tiimbenso Nafera ifetu.
Nyimbo yathu yomweyo.
(Kuli kaphiri m’talimo
268 Kunja kwa mzindawo,
Kwapachikidwa Yesuyo
1. KALE m’mzinda wachifumu
Nafera ifetu.)
Munalimo m’kholamo,
Momwe mkazi anaika
2. Zoopsya sitidziŵapo
Mwana wake m’ndyeromo.
Anazitengazo,
Ndiye mkaziyo Mariya,
Komatu tidziŵitsa ’fe
Yesu Kristu Mwanayo.
Anatiferapo.
2. Uyu ’natsikira kuno,
3. Anatifera tonsefe
Mlungu Mbuye wathuyo;
Tiwomboledweko,
Anabadwa uyu m’khola
Tifike momwe m’Mwambamo
Anagona m’ndyeromo.
Ndi mwazi wakewo.
Mwa osoŵa ndi oipa
Yesu anakhalamo.
4. Kulibe wokwanira ’yi
Kulipa mlanduwo,
3. Mwa ubwana wake wonse
Wina wakutsegula ’yi
Anakula m’mtima phee!
Pakhomo pakepo.
Anakonda, anafatsa,

71
Ambuye akumvani,
5. Anatikondakonda ’Ye, Aleluya, Amen.
Timkonde ifenso; Amatitsogolera,
Tizimtsatira, tithetu Kalelo natifera,
Zintchito zakezo. Kukonda salekera,
Aleluya, Amen.
272 3. Mbuye timlemekeze,
1. ANA inu, myamikeni
Aleluya, Amen.
Mpulumutsi Yesuyo,
Kwawo tikabwereze,
Kaamba ka chikondi chake
Aleluya, Amen.
Ndi chipulumutsocho
Kumwamba timtamire,
Tikamgwadire ife,
Aleluya! Aleluya!
Tikhale chikhalire,
Timwimbire Yesuyo.
Aleluya, Amen.
Aleluya! Aleluya!
Timwimbire Yesuyo.
274
2. Iye anachoka kwawo, 1. MNANDIDZERA, Ambuye,
Anakhala pansipa. Kumwambako,
Kale ana ’namwimbira Munasiya akuluwo;
Namukondweretsadi. Koma m’mudziwotu
munabadwamo
3. Anafika ’kazi omwe Munasoŵa pogonapo.
Ndi tiana taoto;
Yesu anatiyangata, Idzani mumtima mwanga,
Anatidalitsatu. Muli malo a Inu ’mo.

4. Amithenga akumwamba 2. Amithenga ’naimba pamlengapo,


Amamyamikiratu Nalalika ulemuwo;
Zikwi zosaŵerengeka Koma Inu munadza mofatsatu,
Zimtamanda Mfumuyo. Munabadwa mukholamo.

5. Ana inu, yamikani 3. Zili nazotu nkhwimba zirombozo,


Bwenzi lanu lomweli; Ndi mbalamenso zisatu;
M’Mwamba momwe Koma Inu Ambuye mwapandadi
mudzampenya Potsamira mutu duu!
Ndi kumtamandirabe.
4. Munanenatu mawu a moyonso
273 Omasula ochimwawo;
Koma omwe ochimwa
1. ANANU, ziimbani,
’nanyozatu,
Aleluya, Amen.
Nakuphani pamtandapo.
Ambuye tamandani,
Aleluya, Amen.
5. Pakubweranso Inu m’Ufumuwo
Kwezani mawu anu,
Ndi zamphamvuzo zanunso,
Patsani mtima wanu,
Mundimvetse za kwanu
Afuna kumva inu,
Kumwambako
Aleluya Amen.
Kuli malo a ine ’ko.
2. Bwerani, kondwerani,
Ukondwere mtima wanga
Aleluya, Amen.

72
Pakumvera zokomazo. M’njira mwake tiyendemo,
Tiziimba nyimbo zake.
275 3. Aphunzitsi, ana omwe,
1. AKAZI anadza kwa Yesu
Ndi akulu, t’imbe tonse;
ndi anawo,
Nyimbo zathu zidzakwera
Anaŵaletsa anyamata nawakana
Zikamveke m’Mwamba monse.
ndithu;
Ambuye naŵapezadi,
Anati: “Musatero ’yi 277
Lolani ana abwere kwa Ine, 1. OSANATU, osana,
Lolani ana abwere kwa Ine. ’Naimba anawo;
M’kachisi wa Mulungu
2. “Ndidzaŵalandira, k’ŵasunga Mwamveka nyimboyo.
M’manja mwanga; ’Nalemekeza Yesuyo
Ndi Mbusa wao Inetu, msachotse Wak’ŵadalitsayo;
ana anga; Anamuyamikira
Akandipatsa mtimawo, M’ubwana wawowo.
Adzanka ndine Kwathuko;
Lolani ana abwere kwa Ine, 2. Kuphiri la ’Zitona,
Lolani ana abwere kwa Ine.” Mumpingo wa ’nthuwo,
’namkupizira mnjedza
3. Wokoma Mbuyathu kwitana ana Naimba nyimboyo,
onse; Angelo akumwambako
Atsalanso ambiri ena sanamvera Napokerezanso:
zake; “Osana m’Mwambamwamba
Sanamva mawu akewo, Kwa Mlungu wathuyo.”
Sadziŵa kuti ’natinso:
“Lolani ana abwere kwa Ine, 3. Zitsamba zakuyera
Lolani ana abwere kwa Ine.” ’Naponya pansipo;
Kukondwa kunamveka
4. Afike masiku akuti anthu onse Paphiri ponsepo.
Adzamva mawu anu ndi kutsata Ambuye yemwe Mfumutu
Inu nokha; Nakwera cheteko;
Muwale m’mtima mwawomo, Tiana toyamika
Adziŵe muŵakondanso; Sanatinyozato.
Kopani anthu abwere kwa Inu.
4. “Osana m’Mwambamwamba!”
276 Nyimboyi t’imbenso,
Pokhala Kristu Mfumu
1. ANA a Yerusalemu
Ndi Mpulumutsiyo.
Anatama Mbuye wawo;
Timtamandire Iyeyu
Lero lomwe ife ana
Ndi mtima wonsewo;
Timwimbira nyimbo yawo.
Tipite kwawo komwe
Tikaimbirenso.
Mverani, aimba anawo,
Mverani aimba anawo
Zakutama, zakutama, 278
Zakutama Mbuyeyo. 1. NGOLIZO zilira
Za ’mithengawo,
2. Tamva tikondane naye, Ndi zipata zonse
Tiŵerenge Mawu ake, Zatsegudwa mbee!

73
Kristu, Mfumu yathu, Amandimveradi;
Mbuye wathudi, Pakuti walonjeza
Wapambana monse, Adzalandira ’ne
Alamulabe. Ndiimbe ndi angelo,
Pakundikondadi.
Ntchito zake zatha,
Timwimbiretu; 281
Yesuyo wakwera,
1. YESU andikonda ine,
Timtamandetu.
Amatero m’Buku Iye;
Akafoka mwana wake
2. ’Natipulumutsa
Adzamlimbikitsa Mbuye.
Natiferako,
Ali mfumu ndithu
Yesu akonda,
Kwa Atatewo;
Yesu akonda
Osasautsidwa,
Yeu akonda,
Osafanso ’yi
Atero m’Bukumo.
Yesu, Mfumu yathu
Adakweradi.
2. Anandifera Mbuye wanga
Anditsegulire m’Mwamba,
3. Atipempherera
Ndi machimo anga onse
M’malo ’dalawo,
Adzandichotsera konse.
Tinke kwathu komwe
Ndi chisomocho;
3. Mbuye Yesu andisunga
Akonzera malo
M’njira ya Kumwamba kuja;
Ana akewo;
Andigwira m’dzanja langa
Yesu alipobe,
Ndingagweremo m’makwaŵa.
Atikondanso.
4. Yesu andikonda ine;
280 Ndikadzafa tsiku lina
1. NDIKONDA mbiri yomwe Atengera ine kuno,
Ya amithengawo Ndikakhale naye Kwawo.
Ya Mbuye, Mfumu yathu
Pofika pansipa; 282
Zochimwa zindizinga,
1. YESU Mbuye ’Nu wofatsa
Koma ndidziŵatu
Muyang’anedi kamwana,
Anawombola ine
Mndichitire chifundo;
Pakundikondadi.
Mundilole kwanutu.
2. Ndikondwa kuti Yesu
2. Ndimalira kwa Inutu,
’Nakhala mwanatu,
Mpatse mtimawo wabwino;
Chitsanzo atipatsa
M’Dziko lanu loŵalalo
Cha moyo wakewo;
Mulandire mwana wanu.
Ndikati ndimtsatire
Zochita zakezo,
3. Yesu, E, ndikufunani,
Sadzandinyoza konse
Ndinu chuma change chonse;
Pakundikondadi.
Mtima wanu ngwofatsadi;
Kale munali kamwana.
3. Pakumyamika Iye
Ndidzamwimbiratu;
4. Wonga Inu ndikhaledi,
Ngakhale sindimwona
Mtima wanu mundipatse;

74
Yesu ndinu wokomatu, 4. Mutiletse, Mbuye,
Mndiphunzitse kukonda ’Nu. Lero tisachimwe;
Tikondane ndinu
5. Yesu Mbuye ’Nu wabwino, Mutitsuke m’mtima.
M’manja mwanu ndikhalemo;
Mzimu wanu mundipatse, 5. Mukatiitana
M’mtima mwangatu mukhale. Tikakhale kwanu,
Tidzayankha, “Mbuye,
283 Tsopano tili pano.”
1. YESU, ndikabwera
(Yesu, Yesu,
Mundikondweretsa,
Tikugwadirani
Nsoni zanga mun’chotsera
Mwana wa Mulungu!)
Zonsezo.

Ndikabwera, Mbuye; 285


Ndidzakondwera ine; 1. MPULUMUTSI, Mbusa wathu,
Muitana ana onse Mutitsogolere ife;
Onga ‘ne Mutiŵete, mutisunge,
M’khola mwanu mtilandire
2. Yesu, ndikabwera, Yesu wathu, Yesu wathu,
Mumva mapemphero Mnatigula ana anu.
Mundikonda, mnandifera
Inetu. 2. Ndife ana, mutikonda,
M’njira mutiperekeze;
3. Yesu, ndikabwera Mchotse nsoni ndi zoipa,
Dzanja mdzandigwira Osokera muŵabweze:
Nokha mdzandilongolera Yesu wathu, Yesu wathu,
Njirayo. Mumve mapemphero athu.

4. N’takafika kwanu 3. Munanena mulandira


Ndidzakhala bwino, Osauka ndi oipa;
N’dzaonana ndi ananu, Inu ndinu wachifundo
Ndi Yesu. Ndi wamphamvu yolanditsa
Yesu wathu, Yesu wathu,
284 Tidzatu tiana tanu.
1. YESU wa Kumwamba,
4. Tifunitsa Inu tere,
Mutimvere ife;
Chifuniro chanu ndicho;
Tikugwadirani,
Mbuye wathu, Mpulumutsi,
Mwana wa Mulungu.
Mutikonzetu m’katimo;
Yesu wathu, Yesu wathu,
2. Ndinu wakuyera
Mutikondebe ana anu.
Mfumu yakumveka;
Ife sit’yenera,
Koma mutimvere. 286
1. MZINDA woyerawo
3. Ndife akuchoka, Konse nkotsekako;
Mwina tisokera; Kanthu koipa,
M’njira ya Kumwamba Kanthu koipa,
Mutitsogolere Sikangaloŵemo.

75
2. Yesu ndafikatu, Tiyamika mphamvu yanu;
Mbuyanga kwanuku; Mutimvere, Yesu.
Mundiyeretse,
Mundiyeretse, 4. Lero mkhale nafe ndithu,
Mnditsuke m’mtimamu. Poseŵera ndi pantchito,
Popemphera ndi poimba;
3. Mbuye, ndikhaletu Mutimvere, Yesu.
Mbuye wokonda ’Nu,
Ndi wosungidwa, 5. Mutiletse tisaname
Ndi wosungidwa, Ndikunena zotukwana,
Ndi mphamvu zanuzo. Mtiphunzitse kukondana;
Mutimvere, Yesu.
4. Mpaka ndabvala mbuu!
Wowomboledwatu, 289
Woyera mtima,
1. YESU atiuza tiŵale ’fe.
Woyera mtima,
Monga nyali m’mdima
Kwanu Kumwambako
tiunike mbee!
Pansi pali mdima ŵalanitu,
287 Inu m’malo mwanu ndi ine ’mu.
1. MBUYE, tili ana anu,
Tiyamike Inutu; 2. Yesu atiuza tiyambemo,
Zinthu zonse zili zanu, Ationa bwino ndi kuŵalako;
Tingadike m’mtimamo. Ayang’ana pansi poŵala ’fe,
Tiganize zake Yesu, Inu m’malo mwanu ndi ine ’mu.
Za Kumwamba kuli ’Ye;
Tisachite zomsautsa, 3. Yesu atiuza tiŵale pa
Aziona zonsezo. Anthu ali m’mdima osaukawa;
Tiŵalire onse, tonsefetu,
2. Amakumbukira zonse Inu m’malo mwanu ndi ine ’mu.
Tizichita zomwezo.
Tidzamukomana tonse, 290
Sitinyazitsidwako.
1. ANYAMATA inutu,
Mukhululukire ife
Anamwali inunso,
Tchimo lathu lonselo.
Muti: “Tingachitenji,
Mutitsogolere ife
Ang’ono ndifetu,
M’njira ya Kumwambako.
Kuthandiza Ufumu
Wa Yesu?”
288
1. YESU, muli pa chimpando 2. Aphunzitse anthuwo,
Chakuŵala mbee! Kumwamba; Aŵalalikiredi,
Mutipenye ife ana; Akukhala moipa
Mutimvere, Yesu. Mumdima wakunja,
Aloŵetu m’Ufumu
2. Ife ana sitiopa, Wa Yesu.
Mukabwera mutiona,
Tamva kale mutikonda; 3. E! ang’ono ndifetu,
Mutimvere, Yesu. Nzeru sizimafika
Kuti tingaphunzitse;
3. Ife tikondana nanu, Titani tonsefe
Tiimbira nyimbo zanu, Kuthandiza ufumu

76
Wa Yesu? Uli mwana wake,
Mwana wa Mbuyathu.
4. Inu nonse anzanga,
Tiziganiza bwino, 2. Yesu ndi wofatsa,
Tinganene mofatsa, Yesu ndi woyera;
Timverenso Mbuye Ana ake omwe
Kuthandiza Ufumu Aziyera m’mtima
Wa Yesu.
3. Mzimu wakuipa
5. Pothandiza amathu, Ukusuzumira,
Pak’ŵakonda anzathu, Umakuyesera
Pakusiya zoipa, Kuti ukachimwe.
Pokhaladi bwino,
Tithandiza Ufumu 4. Koma usalole
Wa Yesu. Mawu a Satana;
Bweza tchimo lake,
291 Chita zolungama.
1. TIANA ife tingofoka,
5. Yesu ndi Mbuyako,
Sitikhala ’mphamvu ’yi;
Mbuyeyo ngwabwino;
Tikhoza kukachitiranji
Ana ake omwe
Yesu kumkondwetsadi?
Aziyera m’mtima.
2. Tiana ta Ambuye tili
N’ntchito yaikuludi, 293
Kudzichepetsa ndi kusiya 1. TCHIMO musalole,
Tchimo lili lonseli. musadziipitse,
Myese kudzikana, muzilimbikadi;
3. Kapena m’mtima ndimakwiya, Mwamphamvu mpirire, mgonjetse
Nditukwana mnzangayo, zabiizi;
Kapena ndidzitama – izi Mpenye kuti Yesu adzakusungani.
Ndilekere Mbuyeyo.
Mpemphe Mbuye asunge,
4. Ndileke kulimbana ndi Atonthoze m’mtimamu,
Kuŵanamiza enawo; Alikukufunani,
Ndinene zakufatsa, Akasunge inutu.
Zakukondweretsa Yesuyo.
2. Mleŵe oipawo, ayi musatukwane,
5. Tizikondana, tisekere Dzina la Mbuyathu
Tsiku lonse kwathuko, muzilikwezadi;
Muyere m’mtima popeza Khalani achangu, oona, abwino;
Yesu ndi Woyerayo. Mpenye kuli Yesu,
adzakusungani.
6. Palibe mwana wakuchepa
Kunyamula mtandawu; 3. Yesu alandira akupirirawo;
Ambuye Yesu mutipatse Chikhulupiriro chiŵathandizadi
Mtima wokondanatu. Mbuye athangata onse akumvera;
Mpenye kuli Yesu,
292 adzakusungani.
1. USACHIMWE konse,
Lekatu kukwiya; 294

77
1. NTHAŴI yaubwana yatha, Ali wachifundo
Sukulu yathu yathanso; Chachikulu ndithu;
Nkhaŵa ndi zoŵaŵa zomwe Sitiopa imfa
Zitibisaliranso. Akakhala nafe,
Yesu Mbuye wathu
2. Yesu wakufatsa mtima Alandira ife.
Mlendo pansi pano ’Ye,
’Natifera, natisunga, 296
Atitsogolere ’fe.
1. POMPANO pandikonda
Poyendayenda ’ne;
3. Tamverani, aitana;
Paŵala mosekera
“Ana, munditsatetu,”
Ndi dzuŵa loti mbee!
Yesu, tisapite kwina,
Ndikondwa nsiku zonse
Tizikutsatani ’Nu.
Ndikali m’dzikoli,
Potsata Yesu m’njira yake
4. Posachedwa tilekana
Yonseyi.
Osalankhulananso,
Koma tidzaona tonse
2. Ulendo ungoyamba
Wina mnzake m’Mwambamo.
Wakunka kwathuko;
Amati: “Udzapeza
295 Zakusautsa ’mo”
1. YESU ndiye Mbusa, Zobvuta ndi chisoni
Mbusa wakukoma, Sindiziopa ’yi;
Anyamula ana Ndidzangomtsata Yesu m’njira
Ake akuopa; Yonseyi.
Tizitsata Yesu,
Atitsogolera, 3. Zoipa ndi zabwino
Kwina kuli mdima, Zakundigwerazo,
Kwinanso koyera. Ndingonka nazo zonse
Ndimuze Yesuyo;
2. Yesu ndiye Mbusa Zoŵaŵa adzachotsa
Atipenyetsetsa, Zondiliritsazi;
Mawu ake onse Ndikangomtsata Yesu m’njira
Atikondweretsa.
Mwina alangiza 4. Zondipingitsa zonse
Mwana wakulakwa; Zoloŵa m’mtimamo
Atsogola bwino, Achotsa, nandisunga
Ife tizimtsata. M’ulendo wonsewu.
Sindidzaopa kanthu,
3. Yesu ndiye Mbusa, Ngakhale imfayo,
Anafera kale Pomtsata Yesu yekha kunka
Kuyeretsa ana Kwathuko.
Nawo mwazi wake,
Tsono awalemba 297
Ndi chizindikiro;
1. MPULUMUTSI Yesu,
“Ana anga onse
Mumve nyimbo yathu;
Andikhulupira.”
Tikuyamikani
Mumitima mwathu
4. Yesu ndiye Mbusa
Zonse tili nazo;
Wakutisunga ife,
Thupi, mzimu womwe,

78
Inde, moyo wonse,
Tipereka zonse. 4. Yesu, mndiyeretse,
Mndimveretsedi;
Komwe ndi Chimwemwe Mzimu, mndiyendetse
Tidzaimba tonse, Mn’jira yanuyi.
Tidzatama Mbuye
Osalema konse. 5. Ine ndine mlendo
Wa Kumwambako;
2. Tiyandika, Mbuye, Kundiyandikira
M’fupifupi ndinu, Kwathu komweko.
Tikugwadirani,
Mutilandire bwino. 299
Inu munatsika
1. M’MANJA a Yesu wanga
Kutifera ife;
Ndilikugonamo,
Inu munakwera
Mommo aphimba ine
Kuti titsatire.
Nacho chikondicho.
Mvera! Mudzera m’Mwamba
3. Haya! Tipitenso
Mawu a Yesu wanga:
M’njira yomwe ija
“Mwana, ndidzakusunga
Ana a Mulungu
Pano pamtima panga,”
Onse adaponda.
Tizisiya zonse,
M’manja a Yesu wanga
Tiziyenda msanga,
Ndilikugonamo,
Tisamachewuka
Mommo aphimba ine
Mpaka tipambana.
Nacho chikondicho.
4. Tero tidzakwera
2. M’manja a Yesu wanga
Kwawo kwa Mulungu,
Nkhaŵa zonsezo zi!
Tidzaziiŵala
Momwe zoipa zanga
Zotibvuta ife.
Sizindibvuta ’yi
Komwe ndi Chimwemwe
Mmomo mulibe nsoni,
Tidzaimba tonse,
Mommo mokoma monse
Tidzatama Mbuye
Sindiliramo msozi,
Osalema konse.
Ndikondwa m’mtima monse.

298 3. Mtima umabisala


1. Ine ndine mlendo M’manja mwa Yesumu;
Wa Kumwambako; Mbuye, musunge ine,
Pansi pandikonda, Munandifera ’ne.
Koma mpoipa. Ndilinda mopirira
Mpaka wochoka mdima.
2. Kwathu nkopambana, Ndikaonana naye
Nkosachimwako; Yesu Ambuye wanga.
Zosautsa zonse
Sizikhalamo. 300
1. YESU ndiye Bwenzi lathu,
3. Koma azibvala
Kumwamba kuli kwao;
Mwana zoti mbuu!
Amatikonda tonse,
Wosachimwa konse
Akulu ndi tiana;
M’mtima mwakemu.
Anzathu sapirira

79
Amalekana nafe, 3. Oipa tili tonsefe;
Komabe kutiyanja Mwaziwo, mwaziwo,
Saleka Yesuyo. Wa Yesu watigulatu;
Mwaziwo! Mwaziwo!
2. Ana ake adzapuma Tiyeretsedwa nawowo,
Kumwamba mokondwera, Mtendere wa Mbuyathuyo
Amene anamkonda Ukhala nafe komweko.
Namtsata Yesu yekha; Mwaziwo! Mwaziwo!
Sauko ndi zobvuta
Zotitopetsa kuno, 303
Sitiziona konse
1. DZIKO lilipolo
Kumwamba kwathuko.
Lokondwatu
Oyera ’khalamo,
3. Tidzalandirabe komwe
Abvala mbuu!
Zobvala za mitima
Tamvani nyimboyo:
Yoyera, ndi kubvula
“Mfumu tiyamikeyo,
Zakale za kuchimwa;
Mkwezeni Dzinalo
Chimwemwe ndi chikondi
Mwimbenibe.”
Tidzangokhala nazo,
Za ndewu ndi chisoni
2. Tiye kudzikolo,
Sitizipeza ’yi.
Tiyeni ’nu;
Musakayikebe,
4. Woyenera ndani kunka
Muchedwatu.
Kukhala ndi Atate,
Tikondwekondwedi,
Kuimba nyimbo zake,
Tchimo ndi zoipa zii!
Za Mpulumutsi wathu?
Mbuye timwona ndi
Tidzamka ife tonse
Kukondwabe.
Tamtsata pansi pano;
Tiyeni ana onse,
3. Maso a m’dzikomo
Yambani leroli.
Onse nga mbuu!
Mkono wa ’Tatewo
302 Ngwosungatu.
1. KWA Yesu ndi kwabwinoko, Tiye ku dzikolo,
Nkoti mbee! Nkoti mbee! Mgwire ’nu ufumuwo.
Kulibe zoipitsako, M’mwamba mwa dzuŵamo
Nkoti mbee! Nkoti mbee! Tikhalebe.
Kuimba amaimbako,
Ndi amithenga omwewo 304
Akondwerera kokhako.
1. DZUŴA liŵala, m’tulotu
Nkoti mbee! Nkoti mbee!
’Tate chikondi chanucho
Chindidalitsapo.
2. Zochimwa siziloŵako,
Mwayitu! Mwayitu!
2. Dzuŵa la lero lonseli
Misozi m’maso mwawo yi.
Mundisungire ’ne;
Mwayitu! Mwayitu!
Mchotse zoipa zangazi,
Chisomo chili m’mtimamo,
Nanu ndikhalebe.
Aona nkhope yakeyo
Ya Yesu adalitsawo.
3. M’mtima mwangamu mloŵemo,
Mwayitu! Mwayitu!
Mwini chifundocho,
Kuti ndikafananetu

80
Ndinu Mbuyangayo.
2. Laloŵa dzuŵa, kwada bii!
305 Mwapenya ntchito zathuzi;
Taletsa mwini tchimolo,
1. Yesu Mbusa, mutimvere,
Mwinanso tangolakwapo.
Dalitsani ifetu,
Ndi usiku mutisunge,
3. Mufafanize m’bukumo
Tidzukenso bwinotu.
Zolakwa zanu zonsezo,
Ndi kutipatsa ifetu
2. Lero lino mwatipatsa
Mtendere wanu m’katimu.
Zonse tili nazotu,
Moyo womwe; miyamiko
4. Chimwemwe chomwe mpatseko
Landireni Mbuye ’Nu.
Ndikukondana ndinunso
Tifuna kufananadi
3. Tchimo lathu lonse, Yesu,
Ndi Yesu Bwenzi lathuli.
Mukhululukire ’lo;
Mtitengere kwanu komwe
Kumpumulo wanuwo. 308
1. TIKUTHA kupemphera,
306 Tipita kwathu tonse;
Mtiperekeze Mbuye,
1. TILIKUIMBA nyimbo yomweyi,
Panjira zathu zonse;
Yakuyamika Mbuye wathuyo;
Titamva Mawu anu,
Mtendere wake tiufunadi,
Mawuwo ndi amoyo,
Titapemphera tinke kwathuko.
Aloŵe m’mtima mwathu,
Akhazikikemo.
2. Titanka kwathu mkhale nafeko,
Tikufunani Yesu Mbuyathu;
2. Ambuye, Mzimu wanu
Musunge ife nthaŵi zonsezo,
Atikumbutse tonse,
Mutiyeretse m’mtima mwathu
Atithandize lero
mbuu!
Kumvera Mawu onse.
Kumudzi mkhale nafe,
3. Usiku uno mutisungedi,
Musatisiye konse;
Khalani m’fupi m’nyumba
Machimo onse mletse,
mwathumo;
Tiyere m’mtimamo.
Mamaŵanso mudzatidzutse nji!
Kuti tigwire ntchito zathuzo.
309
4. Mtitsogolere nthaŵi zonsezo; 3. TIMYAMIKIRE Mlunguyo,
Kuyenda tokha sitikhoza ’yi, Anthu ndi zinthu zonsezi,
Ngati mukhala Mbuye m’fupimo, Ndi onse a Kumwambako
Sitidzaopa kanthu kena ’yi. Mlungu amyamikiredi.

307 310
1. AMBUYE, mtidalitsetu, 1. MULUNGU akhale nawo
Musunge Mawu m’mtimamu; ulemerero ndi dalitso,
Muyatse moto wanuyo, Ndiye Atate, Mwana,
Chikuletu chikondicho. Mzimu Woyera, Mlungu mmodzi;

Pokhala moyo imfanso, 2. Tsopano, poyamba paja,


Ambuye mtiŵalirepo. Masiku onse alinkudza

81
Mphamvu, ulemerero, 3. Ayamikire ’Nu
dalitso, chipambano. Padziko ponsepa,
Mitundu yonse ipfuule
311 Mokondweratu.
1. YEHOVA, Mbusa wangadi,
4. Pakuti mfumuyo
Ndilibe kusoŵa;
Ndi Inu nokha ’Nu;
Andigonetsa bwinoli
Mudzalangiza bwinotu
Mumsipu wokoma.
Mafuko onsewo.
2. Ku madzi ake odikha
5. Zipatso zakezi
Anditsogolera;
Labala dzikolo;
Ndi moyo wanga wofoka
Adzadalitsa ifetu
Aulimbikitsa.
Mulungu wathuyu.
3. Anditsogolera m’njira
6. Adzadalitsa ’fe
Zakulungamazo;
Mulungu mwiniyo;
Chifukwa changa ay’, koma
Padziko ponse anthuwo
Cha dzina lakelo.
Adzamuopatu.
4. Ndipyola kodi chikhwaŵa
Cha mthunzi wa imfa? 313
Ndilibe mantha ngati ’Nu 1. NONSE okhala pansipa,
Mundiperekeza. Muyamikire Mlunguyo;
Ndi nyimbo mtumikire ’Ye;
5. Chakudya changa chabwino Mubwere mokondweratu.
Mwandikonzera pha!
Pamaso pa adaniwo 2. Yehova ndiye Mlungudi,
Mudyetsa mtimanga. Anatilenga yekhayo;
Amatidyetsa ake ’fe,
6. Mwadzoza mutu wanga ndi Ndi nkhosa zake ifetu.
Mafuta okoma;
Mwadzadza chikho changadi, 3. Loŵani m’Nyumba mwakemu
Inde, chisefuka. Ndi nyimbo zokondweretsatu;
Mumyamikire Mlunguyo.
7. Zokoma ndi zakuyanja Mulemekeze Dzinali.
Zidzanditsatako;
Ndikhala m’nyumba ya Mlungu 4. Pakuti Mbuye Mlunguyo
Ku nthaŵi zonsezo. Wokoma mtima ndiyedi,
Woona adzakhalabe
312 Kunthaŵi nthaŵi zonsetu.
1. MULUNGU, anthu ’fe
Mutidalitsetu; 314
Chisomo chiŵalire ’fe 1. MULI ndi ludzu, idzani
Cha nkhope yanuyo. Kumadzi amoyo
Imwani monse kolere
2. Potero onsewo Kuchitsime konko.
Okhala pansipa
Adzamva bwino msangatu 2. Munka kangati kulaŵa
Za njira yanuyi. Madzi onyengera?
Musataye mphamvu yanu,

82
Musataye chuma. Koma osampeza mommo
(Osampeza).
3. Imvani, Yesu akuti;
“Chuma ndili nacho, 6. Yesu ndiye Mtetezi,
Landirani, yemwe amva Yesu ndiye Mtetezi,
Akhale ndi moyo.” Wina saoneka ayi
(Saoneka).
4. Funani Mlungu tsopano.
Akulindirani; 7. Dzina lake Yesuyo,
Iye ndiye wachifundo, Dzina lake Yesuyo,
Akulandirani. Lidzakhala nthaŵi zonse
(Nthaŵi zonse).
5. Ali wokhululukira;
Imvani ananu: 8. Tonse timyamiketu,
Mtima wake usiyana Tonse timyamiketu,
Ndi mitima yathu. Mpulumutsi wamuyaya
(Wamuyaya).
6. Monga m’Mwamba mupambana
Zonse pansi pano; 316
Choncho maganizo ake
1. AITANA, aitana dziko lonse,
Apitira athu.
Imvani mukhaliranji chete?
Aitana,
7. Anthu onse a padziko
Aitana aitana dziko lonse.
Adzamvera Mlungu:
Adzakhala ndi chimwemwe,
2. Mfumu iyi, Mfumu iyi ya
Nadzamtama ndithu.
Kumwamba
Ndi Yesu, ndi Mpulumutsiyo wa
315 anthu onse.
1. TIYAMIKE Mlunguyo, Anthu onse, anthu onse, tinke
Tiyamike Mlunguyo, kwawo.
Watidzera ndi mtendere
(Ndi mtendere). 3. Aitana,aitana inu mayi,
Ndi Yesu, amene anakhetsa
2. Anatuma, Mtetezi, mwazi wake;
Anatuma Mtetezi, Mwazi wake unagwera inu mayi.
Ndiye Mfumu Yesu Kristu
(Yesu Kristu). 4. Aitana, aitana inu ’tate,
Ndi Yesu amene anakhetsa mwazi
3. Tifunafunatu, wake;
Tifunafunatu, Mwazi wake unagwera inu ’tate.
Osapeza Mpulumutsi
(Mpulumutsi). 5. Yesu ati, Yesu ati; “Muzisiye
Zoipa zimene muzichita,
4. Tifunafuna m’phirimo, muzisiye,
Tinafuna m’phirimo, Muzisiye, muzisiye inu nonse.”
Koma osampeza mommo
(Osampeza). 6. Titi bwanji? Titi bwanji ife anthu?
Ndi Yesu anatifera ife
5. Tinafuna m’nyanjamo, akuchimwa;
Tinafuna m’nyanjamo,

83
Akuchimwa, akuchimwa tinke
kwawo. 2. Tsegulani mtima wanu
Nonse, Yesu akaloŵemo;
317 Akuchimwa, Iye adzaloŵa nazo
zakukomatu.
1. ’TATE, ’Nu.
’Tate ’Nu, mtione ’fe
3. Mtembenuke mtima wanu,
Tadza kupemphera kwa Inu.
Inu osamvera Mlunguyo;
Yesu aitana ife
2. Imvani,
Tikamtsate m’njira yakeyo
Imvani Amfumu ’Nu
Mawu athu tinena lero.
4. Perekani mtima wanu
Kwa Mbuyathu Mpulumutsiyo,
3. Tipempha,
Ndiye wakudziŵa kuchiritsa
Tipempha mdalitsetu
Anthu akuchimwatu.
Mpingo wanu woyera uno.

4. Imvani, 319
Imvani akunjawo 1. YESU, Bwenzi la ochimwa,
Akulira opanda Yesu . Yesu wondikondable,
Ena samandikwanira,
5. Ayenda, Yesu salephera ’yi.
Ayenda munjirazo
Zakupita kuchitayiko. Aleluya Mpulumutsi!
Aleluya Bwenzilo!
6. Ambiri, Amakonda, amasunga;
Ambiri akufadi Ndimufuna Yesuyo.
Osadziŵa za Kristu Yesu.
2. Yesu ndiye mphamvu yanga,
7. Auke, Andilimbikitsatu;
Auke akristuwo, Poyesedwa ndi adani
Akakhale antchito anu. Andipambanitsadi.

8. M’ŵatume, 3. Yesu atonthoza mtima


M’ŵatume antchitowo Ndikadera nkhaŵa ’ne
Alalike Uthenga wanu. Pakukhala ndi chisoni
Andisangalatsabe.
9. Ubwere,
Ubwere Ufumuwo, 4. Yesu ndiye Mtsogoleri
Uoneke padziko ponse. Pakuyenda m’njiramo,
Ndipo ndikafuna kugwa
318 Andigwira dzanjalo.
1. PEREKANI mtima wanu,
5. Yesu ndimafuna Inu,
Yesu aitana nonsenu;
Mwapambana zonsezo;
Osauka, amasiye,
Mlamulire mtima wanga,
Yesu anakuferani ’nu.
Mndikhalitse wanutu.
Perekani, perekani
Mtima wanu nonsenu; 320
Yesu akulindirani, 1. ŴALIRA Yesu m’dziko linoli,
Perekani mtimawo. Ŵalira Yesu m’ntchito zakozi,

84
Ŵalira Yesu pofanana ndi Ndi makwaŵa, indetu,
Ambuyathu Yesu Kristu. Kunakwera kupfuula
Kumwambako,
Tiŵaliretu, tiŵaliretu “Kondwani, ndaipeza yanga!”
Ambuye Yesu wotikonda ’fe; Nd’ angelo a Mlungu
Mlemekeze ’Ye tsiku lonseli, nabwezanso,
Ine tiŵalire Yesu. “Kondwani, Ambuye ’napeza
yawo.”
2. Ŵalira Yesu pazobvutazo,
Ŵalira Yesu pakukondwanso, 322
Ŵalira Yesu, imbirani ’nu
1. MUTHIRE, Yesu, m’mtimanga
Ambuyathu Yesu Kristu.
Kukonda kwanuko:
Mwa Mlungu ndidzalimbika,
3. Ŵalira Yesu wolimbitsayo,
Ndisasokerenso,
Ŵalira Yesu m’moyo monsemo
Ndisasokerenso.
Ŵalira Yesu; tidzaonatu
Ambuyathu Yesu Kristu.
2. E, moto wanu woyera
Uyake mwa ine;
321 Utenthe zonse zoti bii,
1. ZAMBIRI zogona m’kholamo, Undiyeretsedi,
Zosungika bwino ’mo; Undiyeretsedi.
Koma imodzi inasokeradi,
Nitayika m’thengomo 3. Munagwa pa Atumwiwo;
Kutali kuphiri loopsalo, Dzazani mwa ine;
Kutali ndi mbusa wakeyo. Mzimu wamoto Woyera,
Ndipempha mudzetu,
2. Ambuye, muli nazo zambirizi, Ndipempha mudzetu.
Kodi sizifikirazi?
Koma Mbusa nanena, “Yangayo 4. Ndikhazikike inetu,
Yatayika naneyo; Maumtima muli mwai;
Ngakhale njira njoopsadi, Ndi Yesu ndikondanetu,
Ndilinga kuphiri kuipezanso.” Si kanthu kena ’yi,
Si kanthu kena ’yi.
3. Koma zina sizinadziŵa ayi,
Makwaŵa ’napyola ’Ye, 323
Ndi mdima woopsa wa usikuwo
1. ATATE Wamkulu ndi
Ambuye nailonda yake.
Wamphamvu zonse,
Anamva kulira kutaliko,
Atate Wamkulu ndi wamphamvu
Naipeza yofoka, yakufayo.
zonse,
Khalani ndi chifundo ndi ife lero.
4. Ambuye, wakuti ndi mwaziwo
Panjira ponsepo?
2. Ifetu kuchimwa timachimwa,
“Ndaukhetsa potsata iwetu,
Mbuye,
Kukubweza ku kholalo.”
Ifetu kuchimwa timachimwa,
Ndi m’manja mwalaswa
Mbuye,
bwanjimo?
Mutume Mzimu wanu
“Ndalaswa ndi minga pofuna
atiphunzitse.
iwe.”
3. Mwa Mzimu muloŵe mumitima
5. Ndi ponse paphiri ndi padambopo
yathu,

85
Mwa Mzimu muloŵe mumitima M’ngelo anasimba za
yathu, Kubadwa kwake.
Zoipa zathu zonse mtiululire.
Kubadwa kwa Yesu
4. Tafika kwa inu mutiunikire, M’Betlehemumo;
Tafika kwa inu mutiunikire, Khandalo linagona
Chifundo chanu chonse taleka M’khola la ng’ombe.
lero.
2. Mngelo anatumidwa
5. Tifuna kuchita chifuniro chanu, Kuŵasimbira
Tifuna kuchita chifuniro chanu, Abusa a nkhosa za
Chifundo cha Mulungu Kubadwa kwake.
nchabwino chokha.
3. Anapita nasiya
6. Atate, mupatse zomwe Nkhosa zawozo;
tapemphazi, Anapita kumudzi
Atate, mumpatse zomwe Kukamlambira.
tapemphazi,
Tapempha m’Dzina lake la 4. “Tadodoma, abusa,
Mpulumutsi. Kwachitikanji?
Mwazisiyira yani
324 Nkhosa zanuzo?”
1. ONA Mwanawankhosayo
5. “Posunga nkhosa ife
Wakuseza zakuipa zathu zonse.
Kubusa kwathu
Mngelo anasimba za
Mwanawankhosa
Kubadwa kwake.”
Watisenzera
Zakuipa zathu zonse.
326
2. Anazenza m’thupi mwake; 1. ATATE, tifika pamaso panu;
Pakukhomedwa pa mtanda anali Mukomane ndi ife, Mbuye wathu.
duu.
2. Mitima yathu iyi nayo njanu,
3. Ona pamtanda Yesuyo Muiyeretse, muikonze Mbuye.
Anabvutika chifukwa cha anthu
’fe. 3. Ndi maso athu awa nawo nganu,
Muŵapenyetse zinthu zanu zokha.
4. Imva kulira kwa Yesu
Pamene anasiyidwa muimfayo. 4. Ndi manja athu awa nawo nganu,
Agwiretu ntchito yanu yokhayo.
5. M’mwazi wake tisambamo;
Zichotsedwa zakuipa zathu zonse. 5. Ndi miyendo yathu iyinso njanu,
Ithamange m’ntchito yanu
(Ona Mwanawankhosayo yokhayo.
Wakusenza zakuipa
Zathu zonse.) 6. Ndi milomo yathu iyinso njanu,
Ilalike Mawu anu kwa onse.
325 7. Ndi makutu athu awanso nganu,
1. YESU analikhanda
Muŵamvetse Mawu anu okhawo.
M’Betlehemumo;

86
8. Tidziperekadi konse kwa Inu 330
Tikakhale anthu anu okhawo.
1. POTULUKA m’mudzimo
Yesu anasenza mtanda,
327 Pokwera ku Gologota
1. ATATE, ndipempha Kukampachikatu Mbuye.
Tsopano mundimvere, Pilatoyo, mfumu yawo,
Ndipempha kuti mundithandize. Inampereka kwa ’Yuda,
Kuti ampachiketu
2. Ine ndili munthu Kufera zoipa zathu.
Wochimwa pansi pano,
Munditsuke Mbuye, ndiyeretu. (Atate ’nu amayi ’nu, nonsenu,
Onani Yesu wasenza mtanda;
3. Ndalema ndathodwa Atate ’nu, amayi ’nu, nonsenu,
Ndi zinthu zapadziko, Onani Yesu wasenza mtanda.)
Zakhalatu goli londimanga.
2. Zoopsya zopambana
4. Yesu Mfumu Inu Zinachtika pamtanda
Mumandiuza kuti: Kuti mdima unadza,
“Pemphera, ndipo udzalandira.” Dzuŵa linabisikanso.
Chinsalucho cha m’kachisi
5. Ndipempha, Ambuye, Chinang’ambika pakati,
Mundidzaze n’chikondi, Myala inaswekanso,
Mtima wangawu ukukondeni. Dziko linagwedezeka.

328 3. Pomwalira Mbuyeyo


Anapfuula kokweza
1. DZIKO lonse mlambire
Naitana atate
Yesu Mbuye wathuyo,
Kupereka mzimu wake:
Muimbire ndi chimwemwe
“Mlungu wanga, Mlungu wanga.
Dzinalo.
Mwandisiy’ranjitu Ine,
Mundikweze m’Mwambamo,
2. Mbwere nonse muone
Landirani mzimu wanga.”
Zomwe achita Yesu:
Nzozizwitsa, nzodabwitsa
4. Ankhondowo poona
Ntchitozo.
Zinachitika pamtanda,
Anabaya m’nthitimo,
3. Aweruza ndi mphamvu
Munatuluka magazi.
Ku nthaŵi yamuyaya;
Paphirilo la Golgota
Dizo lake lisamala
Anaferapo Mbuyeyo
Am’dziko.
Nasauka koopsya
Ndi zoipa zathu izi.
4. Mbwere mudzamve nonse
Zamphamvu za Yehova;
Mumwibire, mumyamike 331
Yehova. 1. TUMPHATUMPHA moyo wanga,
Sangalala ndi Mtetezi;
5. Tisonkhane tonsefe, Kuwombola kwa Yehova
Tigwadire Ambuye; Kwatuluka m’dziko lako.
Timlambire, timlambire
Yehova. Mulungu wakwezekatu,

87
Mpulumutsi m’dziko lako,
Wakwezekatu Chitetezo. 5. Angelo aitana,
Wabvundikira iwedi Aitana Kumwambako,
Mzimu wanga’we wafunda, Tiyeni, tikwere!
Lulutiratu moyo wanga.
6. Munafera pa mtanda
2. Bvinabvina moyo wanga, Chifukwa cha inedi,
Lulutira mtima wanga; Si cha wina ayi.
Wa mawuwo a Yehova
Watuluka m’dziko lako. 333
1. LIDZE msanga dzuŵa lanu
3. Imbirira moyo wanga,
Lolonjezedwa, Ambuye.
Mtendere wako wafika;
Mnalinena polaŵira
Mbendera ya Chitetezo
Kwa anyamata, Ambuye.
Waikwezetsa ndi Yesu.
Kuli chimwemwe m’dzuŵalo
4. Ukondwere moyo wanga,
Lakufika Ambuye.
Kuunika kuoneka,
Ha! Ambuye bwerani.
Ndi mdimawo uthaŵatu;
Ha! Ha! Ambuye bwerani.
Lulutira moyo wanga.
2. M’dziko lino chimwemwecho
5. Usekere moyo wanga,
Chakudza ndi Yesu Mbuye.
Ndi Yehova akufuna;
Mfumu yathu ya Kumwamba
Wakwezatu mbenderayo
Ndi dziko lonse lapansi.
Ya Chitetezo, sekera.
3. Adzakhala pampando
332 Wakuweruza makamu;
1. PAKUONA imfayo Amitundu adzaima
Chisonicho chikula Pamaso pa Mbuye Yesu.
Ndilira misozi.
4. Adzanena kwa anthuwo
Ndilira, ndilira, Akudzanjatu lamanja,
Ndilira Mbuye Yesu wangadi. “Loŵani ’nu m’chikondwero
Ndaimba ndi kulira ndi kusisima, Cha Atate nthaŵi zonse.”
Ndaimba ndi kulira ndi kusisima,
Ha! Ha! Aleluya! 334
Ha! Ha! Aleluya!
AMEN, Amen, Amen.
Mwasiyiranji Ambuye Yesu?

2. Ndinasiya amayi, 335


Ndinasiya atate, 1. NDIDZE pafupi pa
Abale komweko. Mlungu wanga,
Ngakhale pamtanda
3. Kazembe wanga m’matenda, Mundikweza;
Ndili m’manja mwa Mbuye. Koma ndiimbabe
Abale tsalani. Mbuye mndikhalitse,
Mbuye mndikhalitse,
4. Zoipa zakanikadi, M’fupi Ndinu.
Sizikhoza kuchotseka,
Ndilira misozi. 2. Ngakhale kuthengo

88
Ndasokera,
M’mdima ndigonapa Ndisamba ndiyera,
E, pamwala; Ndisamba ndiyera;
Koma m’kulotako Ndimo inenso mwa uyu
Ndiyandikizanso, Ndisamba ndiyera.
Ndiyandikizanso
M’fupi Ndinu. 3. Mwazi wa Yesu wokondwa
Ukhala wamphamvu
3. Pajapo ndipenya Kwa ana onse a Mlungu,
Pokwerapo, Uchita kwombola.
Angelo atsika
Kumwambako, Uchita kwombola
Ndiwo akodola Uchita kwombola;
Kuti ndikabwere, Kwa ana onse a Mlungu
Kuti ndikabwere Uchita kwombola.
M’fupi Ndinu.
4. M’mene ndapenya mwazi wa
4. Tsopano poukanso Mabala anuwo,
Wokondwatu, Kukonda kwathu nditama
Ndipeza pomwepo Kwa kutha kwa moyo.
Pali Mlungu;
Ndipo masautso Kwa kutha kwa moyo,
Andisendezanso, Kwa kutha kwa moyo;
Andisendezanso, Kukonda kwanu nditama
M’fupi Ndinu. Kwa kutha kwa moyo.

5. Pena pakufadi, 5. Kumwamba ndikaimbanso


N’kwera m’Mwamba, Zimphamvu za Mlungu,
Dzuŵa ndi nyenyezi Zopulumutsa onsewa
Zitsalira; Omvana ndi Yesu.
Pomwe ndiimbanso,
Ndidza pafupi pa, Omvana ndi Yesu,
Ndidza pafupi pa Omvana ndi Yesu;
Mlungu wanga. Zopulumutsa onsewa
Omvana ndi Yesu.
337
1. KASUPE ali wodzaza 340
Ndi mwazi wa Yesu; 1. MALO alimo m’nyumba ya Yesu,
Omwe asamba mwa uyu Ndi nyimbo zake zakuitana:
Ataya zoipa.
“Loŵa, loŵa,
Ataya zoipa, Tsopano loŵatu.”
Ataya zoipa;
Omwe asamba mwa uyu 2. Mdima ufika, dzuŵa laloŵa,
Ataya zoipa. Nthunzi zilipo, wadza usiku.

2. Woba wakufa ’napenya 3. Nyumba yodyera ilikudzaza;


Kasupe, nakondwa, Idza nuloŵe, Mkwati anena:
Ndimo inenso mwa uyu
Ndisamba ndiyera. 4. Chakudya ichi ndi cha iwenso,

89
Madzi amoyo umwe kolere. 1. M’DZIKO lino tikhalamo
Utibvuta moyo,
5. Onse am’Mwamba ali momwemo, Koma dziko la mtendere
Ndipo angelo akuitana: Lili kwa Mulungu.

6. Mawu a Yesu ati: “Msangatu 2. Watitsogolera Mbuye,


Idza, wochedwa, loŵa Komwe kwa Atate,
m’nyumbamo.” Ndimo tidzatsata naye
Moyo wathu wonse.
7. Msanga adzachitseka chitseko,
Adzakuuza: “Choka, chokatu.” 3. Ndi tsopano tilindira
M`dziko lathu lino;
Choka,choka, Ntchito atipatsa Mlungu,
Anena chokatu. Tizigwira bwino.

341 4. Ngati zakuipa zathu


Zikatisautsa,
1. PAMTANDAPO, pamtanda,
Tithaŵire kwa Mbuyathu,
Yesu ’nafera;
Atipulumutsa.
Pamutupo chilemba,
Chisoni ine.
5. Timpemphere kutipatsa
Analira, “Eloi, Mlungu wanga!
Mtima watsopano,
Lama sabakatani,
Kutithandizira kunka
Mwandisiyiranji?”
Paulendo uno.
2. Kumandako, kumanda
Yesu nauka; 344
Anaposa imfayo, APITA anzathu dzuŵa lino
Watha zonsezi. Kosaoneka,
Ndikondwera, Mbuyanga Apita anzathu dzuŵa lino,
’naukadi; Apita anzathu dzuŵa lino
Sekerani nonsenu, Kosaoneka.
Yesu ngwamoyo.
A! Kumwamba
3. Pakukwera Kumwamba A! kuli a Yesu.
Yesu anati,
“Musachoke m’mudzimu, 345
Pempheranitu;
1. INE ndili ndi manyazi
Mzimu Wakuyeradi adzabwera,
Kuti kale lomwelo
Kuthangata nonsenu,
Ndinanyoza kudza komwe
Kuti msafoke.”
Kwa Mtetezi wanga Yesu,
Ndati, Sindimfuna `yi.
4. Uzanitu abale,
Onse alongo,
2. Koma Iye wandipeza;
Ndi amitundu yonse
Ndamuona m`mtandamo,
Adzakondwera.
Mwa kufera ine momwe;
Musaope ntchitoyo yokomadi,
Ndipo ndati m`mtima mwanga:
Mphotho yake Kumwamba,
Mbuye, ndikufunani.
Moyo wosatha.
3. Nsiku zonse kwanja kwake
342 Kunandithandizatu,

90
Kunandichiritsa mtima; Khululukireni.
Ndipo ndati: Mpulumutsi,
Ndinu Mbuye wangatu. 2. Ndinachimwa poganiza
Ndi polankhulanso,
4. Sindifuna Mbuye wina, M'ntchito zanga ndachimwanso;
Koma Yesu yekhayo; Khululukireni.
Ine ndili munthu wake,
Iye anandigonjetsa 3. Ndinachita mphulupulu,
Ndi kukonda kwakeko. Ndinakunyozani,
M'ntchito zanga ndalephera;
346 Khululukireni.
1. KONDWANI nonsenu,
4. Zonse ndinakonda kale
Mpulumutsi anadza;
Ndi zopanda pake,
Onani kukhola,
Sindinakhuta nazotu;
Ndi mtanda ndi manda
Khululukireni.
Mlemekeze, bukitsani,
Naferatu kale; 348
Kondwerani, mlemekeze 1. MEMA nkhondoyo, wadza
Akhaladi moyo. mdaniyo,
Kweza mbendera ya Mbuye.
2. Kondwani nonsenu, Bvala zidazo, imba nyimboyo,
Anakhetsatu mwazi, Khazikikatu pa Mulungu.
Natiwombola nawo,
Tikhale ana ’ke. Haya, anzathu, itilinda nkhondo;
Limbanitu, nkhondo nja Yesu.
3. Kondwani nonsenu, Musafoke, m’thyole linga lawo;
Atikhululukira, Mbuye ndiye Wopambanayo.
Wosachimwa nafera
Anthu ’fe oipa. 2. Mlungu mverani, mphamvu
patseni,
4. Kondwani nonsenu, Tithandizeni, tipempha.
Mfumu yathu yakwera; Nkhondo itatha, titapambana,
Kwa Atate Kumwamba Tidzalandiratu korona.
Atipempherera.
3. Mlake mdaniyo, mwimbe
5. Kondwani nonsenu, m'njiramo
Adzabweranso Yesu, Mpaka nkhondoyo ileka.
Waulemu, wamphamvu, Zida konzani, mantha tayani,
Kuweruza dziko. Pitikitsani adaniwo.

347 349
1. TATE ndili mwana wanu, 1. M'MANDA, nagonamo
Nkana ndinachimwa, Yesu Ambuye,
Ndingolirira kwa Inu; Anadikiratu
Khululukireni. Tsiku lija.

Machimo anga ngambiri M'manda naukamo


Osaŵerengeka, Napambana ’'dani akewo;
Ndingoyang’ana kwa Inu; Anauka kupambana imfayo,

91
Ali moyo ndi oyeramtimawo. Kukabatiza ’menewa;
Wauka, wauka! Muŵachitire chifundo.
Aleluya wauka! M’ŵapatse Mzimu Woyera.

2. M'manda munalibe 4. Angelo anu asunga


Yesu Ambuye, Tiana tathu tofoka;
Nadikira chabe Pa njira yanu tiyenda,
Alondawo. Mulembe m’Mwamba maina.

3. Imfa yalephera 5. Mukonda nyimbo za ana,


Kumutsekera, Kokoma amaimbatu;
Anachotsa zonse Ndi ana athu atama
Zomzingazo. Atate, Mwana ndi Mzimu.

350 352
1. YENDANI, Mfumu yamtendere 1. YESU Mbuye, onani
Anthu akuimbirani; Tadza poitana Inu;
Apfuuletu Hosana, M’dzina lanu tifika
Agonjeranso anthuwo. Osekera kwa Atate;
Mkhale nafe Inu nokha
Yendanitu m'ulemudi, Tikaimba nkupemphera.
Pulumutsani anthuwo.
2. Mbuye, Mzimu Woyera
2. Yendani, Munthu Wachisoni, Munapatsa ana anu
M’mudzi wa Yerusalemu; Kukalonga mumtima
Angelo amapenya ’Nu Mawu ndimo mvanu womwe:
M’mene mwafera anthuwo. Zinthu zonse pansi pano
Sizikondweretsa ife.
3. Yendanitu, Wansembe wathu,
Mtanda wanu mwanyamula 3. Mzimu, mlonge m’mtimamo
Watisandukira dalo, Maphunziro achifundo;
Watitengera moyowo. Timve lero ndi maŵa
Ndi masiku onse Yesu.
4. Yendani mwaulemerero, Ndimo m’Mwamba tidzaona
Akulindirani mphotho, Tidazimva pansi pano.
Moyo wanu wosatha
Watilonjezera moyo. 353
1. PEMPHERO ndiko kufuna,
351 Kulakalakatu;
1. KAMWANA Yesu ’nabadwa, Ndi monga moto liyaka
Ndi Iye Mlungu Wamphamvu; Mumtima wa munthu.
Angelo anapembedza
Mwana wakhanda Iyeyu. 2. Pemphero ndiko kulira,
Ngakhale misozi,
2. Kamwana kaja ’nayamba Kupenyetsetsa Kumwamba,
Kuonetsera Atate, Mulungu mpafupi.
Lero anena Kumwamba:
“Tiana tidze kwa Ine.” 2. Pemphero ndiko kufuna
Kwa mwana wamng’ono;
3. Tibwera ndi tianato Ndiponso mawu amphamvu

92
A munthu wamvanu. Mwa Yesuyo, yenda!

3. Pemphero ndiwo mweyawo 2. Kukondwa kwa wodwalayo


Apuma akristu; Kunali kopambana;
Ndi mapemphero tiloŵa Iye anatumphatumpha,
Dziko la imfalo. Kuzungulira
Sunagoge yense.
4. Mutiphunzitse, Mbuyathu,
Kupempha kotero, 3. Lero lino Mbuye Yesu
Kuyandikira kwa Mlungu Aitana nonsenu;
Ndi mtima wabwino. Mukamvera ndi kumtsata,
Mudzakondwera
355 Ndi mdalitso wake.
1. YESU, ndipemphera
Mndithangate 357
Kukonda Inutu, 1. YESU watidzera, watidzera,
E, kwambiri. Way’tana anthu onse.
Koposa zonsezo Udzimvere wekha.
Za pansi panopo,
Ndikondane Aleluya, Aleluya!
Ndinu Mbuye. Aleluya, Aleluya!
Udzimvere wekha.
2. Kale ndinafuna
Za pansipa, 2. Kudziŵa ukudziŵa, ukudziŵa,
Tsopano ndilira Kulibe zachisoni.
Inu nokha. Udzimvere wekha.
Ndifuna kukonda
Inu kopambana 3. Atumwi atumika, atumika,
Zinthu zonse Akulalika Yesu.
Za pansipa. Udzimvere wekha.

3. Inu ndidzatama 4. Yesu Mpulumutsi, Mpulumutsi


Nthaŵi zonse, Wa dziko lili lonse.
Imfa ikafika Udzimvere wekha.
Ndidzanena:
“Ndifuna kukonda 5. Kumva ulikumva, ulikumva,
Inu, Mbuye wanga, Ungonyalanyaza.
Kopambana Udzimvere wekha.
Zonse zanga.”
6. Bwerani inu nonse, inu nonse,
356 Mudzalandire moyo.
Mudzimvere nokha.
1. PANALITU wakudwala
Amene akakhala
Pakhomo la sunagoge: 358
Kuti anthu ena 1. MUDZE kwa Yesu, musachedwe.
Amuone iye. Kalata ilozera njira;
Amaitanatu tonsefe,
Yenda iwe, yenda. Bvomerani Iye.
Yenda iwe, yenda,
Siliva ndilibe; Tidzakondweradi m’Mwambamo

93
Posonkhana komwe kuli ’Ye; Dzimbiri ndi njenjete
Tidzakhala naye komweko zimachiononga.
Ku Dziko losafa.
3. Koma mudziunjikire chuma cha
2. Lolani ana, mumve Mlungu, Kumwamba
Tsegulani mitima yanu, Kumene anapita Mtsogoleri wanu.
Sankhani Iye, Bwenzi lanu;
Musachedwe, mudze. 4. Aliponso adani am’kati ndi
akunja;
3. Ganizansoni, ali pano, Yesu watisekera, tidzakuimbirani.
Mthenga wake mverani lero;
Mawu okoma ati lero, 5. Aliponse mabvuto, ena ndi oipa;
Musachedwe, mudze. Yesu mutimasule kwa adani athu.

359 363
1. MWA ine, moyo wanga ndi Yesu 1. TIYAMIKE mbuye Yesu
(Yesu) Yemwe anafera ine, Yemwe anatifera
Ndiye anandiwombola; Imfa ija yoopsetsa
Yesu, Yesu. Kuwombola tonsefe.

2. Mwazi wake ndi chitsime changa, Ife


(Yesu) Pamene ndikasambamo tapulumukadi,
Zochimwa zanga zidzatha; Ife
Yesu, Yesu. Tapulumukadi,
Imfa,
3. Yesu Mfumu, ine ndingadzafe Imfa yoopsa ija yapamtanda,
(Yesu) ngati mundisiya ndekha, Imfa,
Kukhala ndekha sinditha; Imfa yoopsa ija yapamtanda.
Yesu, Yesu.
2. Panalibe mwa abale
4. Yesu Mfumu, ine ndisekere Yemwe akadakhoza
(Yesu) Inu Mpulumutsi wanga Kupereka moyo wake
Pamene mukhala nane; Kuwombola tonsefe.
Yesu, Yesu.
3. Tikondwera ife tonse
360 Pakuona ntchitoyo
Anachita Mbuye Yesu
1. LEKANI kubvutika ndi zinthu za
Kuwombola tonsefe.
padziko,
Musekerere kuti tidzaimbira Yesu.
364
Imbira! 1. MZIMU ndi mtogoleri
Timwimbire Yesu, M’njira yachikristuyo,
Mpulumutsi wathu! Atitsogoleratu
Imbira! Paulendo wathuwu.
Timwimbire Yesu, M’yoyo ikondweratu
Tonse tidzakondwera. Pomva mawu akewo,
Pakunena Mzimuyo,
2. Musadziunjikire chuma cha “Osokera, bwerani.”
padziko
2. Bwenzi lathu ndinutu,

94
Mkhale m’fupi nafetu; Mwana wa Mlungu pa mtanda.
Msatisiye tokha ’fe Anatani?
Pakuyenda m’mdimamu; Anafera.
Pakuwomba mphepozo Ali kuti?
Timaopa m’mtimamo, Akhaladi m’Mwamba
Tsono timve mawuwo: Kutipempherera.
“Amantha ‘nu, bwerani.”
2. Palibe m’modzi akanatha
3. M’mene ntchito yathatu, Kuloŵa m’malo mwake;
M’mene tidikira ’Nu, Ngakhale anali wamkulu
Pakukhumba m’Mwambamo, ’Nasiyidwa namnyoza.
Tsono tipempherabe.
Nthaŵi ya mabvutowo 3. Kodi mudzampembedza Mbuye
Tikhulupirira ’Nu, Mpulumutsi wathuyo?
Tsono timve mawuwo, Kodi inu mudzaloŵamo
“Okondedwa, bwerani.” Mu Ufumu wakewo?

365 368
1. MASO ndi maso ndi Kristu, 1. MPULUMUTSI Wokondedwa,
Kodi ndidzachitanji Mwandipulumutsa ine;
M’mene ndidzaona Yesu, Ndine wanu, wanu nokha,
Yemwe anandifera? Wotsukidwa m’mwaziwo.

Ndidzamwona maso ndi maso Aleluya, Aleluya,


Kuseri kwa mitambo; Mwanawankhosa ndinutu:
Posachedwa ndidzamwona Mwazi wanu wanditsuka,
M’ulemerero wake! Aleluya kwa Yesu.

2. Tsopano ndimwona Iye 2. Mtima wanga wabvutika,


Mwa chizimezimetu; Zaka zonse ndingochimwa;
Tsiku lija ndidzaona Tsono sindikangalika,
Ulemerero wake. Ndingopuma mwa Yesu.

3. M’mene masautso onse, 3. Mwandipatulira ine,


Nthenda, imfa, zidzatha, Kwa Inu ndidzipereka,
Dziko likadzakonzedwa, M’moyo, m’imfa mboni yanu
Ndidzakondwa koposa. Ya chipulumutsocho.

4. Lodala tsiku lomwelo 4. Aleluya, mwandigula,


Ndidzamwona Yesuyo, Ndipo mudzandisungabe;
Mpulumutsi wanga yemwe Mwazi wanu ndi wamphamvu
Anandikonda ine. Kuyeretsa konseko.

366 369
1. MVERANI mbiri yozizwitsa 1. MLENDO ali pakhomo,
Ya Yesuyo kalelo; Mloŵetseni
Iyeyo ’nadza pansi pano (mloŵetsenitu),
Kutipulumutsa ’fe. Wadza kalekalelo,
Mloŵetseni
Ndani anatiwombola? (mloŵetsenitu);

95
Mtsegulire msangatu, Ndipereka zonse kwa ’Nu,
Wakuyerayerayo, Dalitsenitu.
Mwana wa Mulunguyo,
Mloŵetseni 2. Ndipereka zanga zonse
(mloŵetsenitu). Pamapazi a Yesu;
Zapadziko ndazikana,
2. Utsegule mtimawo, Nditengeni Yesu ’Nu.
Mloŵetseni
(mloŵetsenitu), 3. Ndipereka zanga zonse,
Ukachedwa achoka, Ndipo n’khale wanutu;
Mloŵetseni Mzimu wanu ’ndidziŵitse
(mloŵetsenitu): Kuti ndine wanudi.
Ndiye Bwenzi lakolo,
’Dzapulumutsa ’we; 4. Ndipereka zanga zonse,
’Dzakusamaliranso, Ndili wanu ndense ’ne;
Mloŵetseni Nditamanda Dzina lanu,
(mloŵetsenitu). Aleluya, Ambuye.

3. Imva mawu akewo, 373


Mloŵetseni
1. CHITETEZO chachikulu
(mloŵetsenitu),
Chotuluka m’mwaziwo
Sankha Iye leroli,
Wa Ambuye Yesu Kristu,
Mloŵetseni
Mpulumutsi wathuyo.
(mloŵetsenitu);
Mpulumutsi, chitetezo
Wangoima pa khomo,
Chipezeka m’mwaziwo.
’Dzakusangalatsa ’we,
Udzamlemekezatu,
2. Ndi chimwemwe ndimaona
Mloŵetseni
Mtsinjewo wa mphamvutu;
(mloŵetsenitu).
Zonditsutsa zachotsedwa,
Yesu wanditsuka mbuu!
4. Mlendo wa Kumwambayo,
Mpulumutsi, chitetezo.
Mloŵetseni
Chindisangalatsatu.
(mloŵetsenitu),
’Dzakupatsa zonsezo,
3. Tchimo lonse ligonjera
Mloŵetseni
Chikondicho cha Yesu,
(mloŵetsenitu);
Maganizo ’yeretsedwa;
’Dzakhululukira ’we,
Ndingofuna zakezo.
Ndipo potsirizapo
Mpulumutsi, chitetezo
’Dzakutenga m’Mwambamo,
Chigonjetsa mtimawu.
Mloŵetseni
(mloŵetsenitu).
4. Ndili nawo moyo w’satha
Wochuluka mwa Yesu,
370 Mzimuyo wadzaza mtima
1. NDIPEREKA zanga zonse Ndi chimwemwe chakecho.
Mwaufulu kwa Yesu; Mpulumutsi, chitetezo,
Ndidzamkonda kopambana, Chiyanjano chomwenso.
Tsiku lili lonsetu.
5. Mantha, nkhaŵa, ndi chisoni
Ndiperekatu Zachotsedwa zonsezo;
Zonse kwa Yesu; Mbuyeyo ndimkhulupira,

96
Anditsogoleratu.
Mpulumutsi, chitetezo, 3. Dalitsani mafuko onse,
Ndimkondadi Yesuyo. Aweruze bwino maiko;
Adzichepetse ndi kuopa,
374 Ndipo mtidalitse tonse ana anu.
1. AMBIRI tikondwera mwa Yesu,
Nanga inu? Nanga inu? 376
Tapeza chipulumutso ndithu; 1. MLUNGU dalitsani Malaŵi,
Nanga inu? Mumsunge m’mtendere;
Gonjetsani adani onse,
Masiku onse timakondwera Njala, nthenda, nsanje;
Pakumva Mawu ake a Yesu; Lunzitsani mitima yathu
Wolalikira tidzamumvera; Kuti tisaope,
Nanga inu? Mdalitse Mtsogoleri, nafe,
Ndi Mayi Malaŵi.
2. Ife tiyembekezera YESU,
Nanga inu? Nanga inu? 2. Malaŵi dziko lokongola,
Chimwemwecho chili La chonde ndi ufulu,
mumtimamu; Nyanja ndi mphepo ya m’mapiri,
Nanga inu? Ndithudi tadala;
Zigwa, mapiri, nthaka, dzinthu,
3. Titasokera tinabwerera, Mphatso zaulere;
Nanga inu? Nanga inu? Nkhalango, madambo abwino,
Tidziŵa kuti ndiwo uchimo; Ngwokoma Malaŵi.
Nanga inu?
3. O! Ufulu tigwirizane
4. Tinachoka munjira ya imfa, Kukweza Malaŵi;
Nanga inu? Nanga inu? Ndi chikondi, khama, kumvera,
Takopeka ndi Mawu a Yesu; Timutumikire;
Nanga inu? Pankhondo nkana pa mtendere
Cholinga n’chimodzi,
375 Mayi, Bambo, tidzipereke
Pokweza Malaŵi.
1. MBUYE dalitsani Afrika,
Itukulidwe nyanga yake;
Mverani mapemphero athu, 377
Ndipo mtidalitse ife ana anu. 1. ANTHU m’maiko onse
Akhala mitundu;
Mbwere Mzimu, Kapena m’dziko lino
Mbwere Mzimu, mbwere! Akhala anzathu;
Mbwere Mzimu Agona mwa zoipa,
Mbwere Mzimu,mbwere! Apulukiradi,
Mbwere Mzimu Ati, Mutilangize
Woyera, Woyera. Abale, bwerani.
Mbuye, dalitsani
Ife ana anu. 2. Ngakhale alemera
Ndi chuma cha dziko,
2. Dalitsani mafumu athu, Kodi akakondwera
Akumbukire Mlengi wawo; Opanda Mulungu?
Aope ndi kunjenjemera, Kodi akhala mwaŵi
Ndipo m’ŵadalitse iwo ana anu. Otsata zawozo?

97
Iyai, awonongeka, M’dziko la Mulungu,
Apeza tsokalo. Tidzakondwera chikondwere
Nthaŵi zonse zathu.
3. Ndi ife akudziŵa
Chikondi cha Mlungu, 379
Kodi tidzaŵamana
1. POZUNZIDWA inu ponseponse
Kuŵala kwa Kristu?
Ndi kufoka m’mtima nazo
Chipulumutso! Inde,
zonsezo,
Tichibukitsetu,
Ŵerengani madalitso anuwo
Kuti mitundu yonse
Ndipo mudzazizwa potsirizapo.
Ibwere kwa Yesu.
Ŵerengani madalitsotu,
4. Akristu nyamulani
Anakupatsani Mlungudi.
Maneno a Mulunguyo,
Ŵerengani lina linanso,
Ndi moyo lalikani
Ndimo mudzazizwa potsirizapo.
Pa dziko lonselo;
Ndi Yesu Mpulumutsi
2. Kodi muvutidwa naye katundu?
Anatiferatu;
Ngwolemera mtanda muusenzatu?
Adzabvomera onse;
Ŵerengani madalitso anuwo,
Ndi Mwana wa Mlungu.
Ndimo mudzaimba dzuŵa
lonselo.
378
1. PADZIKO pano tikhalira 3. Poyang’ana ena ndi ndalamatu,
M’moyo wosauka; Ganizani kuti Mbuye wanudi
Komatu kwa Mulungu kuli Adzakupatsani zake zonsezo,
Dziko lakudala; Chosagula chuma chanu
Mbuyathu Yesu wapitako, chonsenso.
Iye ’natsogola;
Tidzamtsatira ife tonse, 380
Tsiku lomaliza.
1. YESU Mbuyetu, mwafera
Mphulupulutu zanga,
Tiyeni, tiyeni,
Ndimo ndamva mund’itana,
Ku dziko lakudala;
Mutitu, Msachedwa.
Tidzafikira m’dziko ilo
Tsiku lomaliza.
2. Zonse za m’dziko zidzatha,
Koma za moyo m’Mwamba
2. Masiku tikatsala ife
Zomwe zidzakhalitsatu,
M’dziko mwathu momwe
Chakatu ndi chaka.
Mulungu watipatsa ntchito,
Tikazigwiritse.
3. Nyengo ifika, chenjera!
Pamene zakuipa zathu
Adzakukana m’Mwamba.
Zisautsa ife,
Lapa zoipa zakozo,
Tikapemphere Mbuye wathu,
Kuti ukaloŵe.
Atipulumutse.

3. Ulendo wathu ukadzatha 381


Tidzafika kwathu, 1. TAMANDANI Mbuye,
Adzatifitsa ife komwe Inu atate,
Yesu Mbuye wathu. Mpatse Yesu mitima yanu.
Sitidzapeza masautso

98
2. Tamandani Mbuye, Utsani anthu akufa
Inu mafumu, Ndi mawu a mphamvu.
Mpatse Yesu mitima yanu.
2. Mbuye mtsitsimutse
3. Tamandani Mbuye, Ntchito zonse zanu!
Inu abale, Tauzirani pa ife
Mpatse Yesu mitima yanu. Ndi mweya wa Mzimu

4. Tamandani Mbuye, 3. Mbuye mtsitsimutse


Inu nonsetu, Ntchito m’mitimamo!
Mpatse Yesu mitima yanu. Mumvetse njala kwa Inu—
Mutikhutitsenso.
5. Tamandani Mbuye,
Mipingo yonse; 4. Mbuye mtsitsimutse
Aleluya, Aleluya! Ntchito m’kati mwa anthu!
Chikondi chawo chikule
382 Muchikolezetu.
1. MVERA mtima wanga ’we
5. Mbuye mtsitsimutse!
Akufunsa Ambuye;
Mawu alimbike,
“Wosauka wa’mphaŵi,
Pamene aphunzitsidwa
Kodi undikondadi?”
Onsewa amvere!
2. “Ndakupeza womanga,
6. Mbuye mtsitsimutse!
Ndamasula zinsinga,
Mzimu adzazetu!
Ndakulonda kutali,
Kwa ife kudzakhala mwayi,
Kodi undikondadi?”
Kwa Inu ulemu.
3. “Akaleka amake
Kusungira mwanake, 384
Ine sin’kuleka ’yi, CHIKHULUPIRIRO chathu
Kodi undikondadi?” Tatchulachi pakamwapo,
Mulungu athandize ’fe
4. “Ndakukonda ku imfa Chikhale cha mumtimamo.
Ndi chikondi chosatha,
Kwaulere, kwambiri,
Kodi undikondadi?”

5. “Msanga ndidzabweratu,
Udzaona ulemu,
Udzakhala ndi Ine,
Kodi undikondadi?”

6. Mbuye ndisaukadi,
Chimachepa chikondi,
Mtima wanga mudziŵa,
M’ndipunzitse kukonda.

383
1. MBUYE mtsitsimutse
Ntchito zonse zanu!

99

You might also like