DZINA_________________________________________________________________________________________
NGABU CLUSTER MOCK EXAMINATION
2024 JUNIOR CERTIFICATE EXAMINATION
CHICHEWA
Subject Number: J032/II
Time Allowed: 1 h 45 Min
Tuesday, 26 March 8:00-9:45 am
PEPALA LACHIWIRI
(MALIKISI 50)
MALANGIZO
1. Onetsetsani kuti pepala ili lili ndi masamba Funso Chongani zomwe Muno
asanu ndi anayi. mwayankha musalembemo
2. Lembani dzina lanu pamwamba pa tsamba 1
lililonse.
3. Yankhani mafunso onse m’gawo A, B ndi C. 2
4. Muchitebulo chili pambalichi chongani funso
3
lomwe mwayankha mubokosi lili kutsogolo
kwake. 4
5. Perekani pepalali kwa oyang’anira mayeso
5
nthawi ikakwana.
© NGABU CLUSTER Onani paseri/…
Page 2 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
GAWO A (Malikisi 20)
KUMVETSA NKHANI
1. Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala ndipo muyankhe mafunso otsatirawo pa mizere ili pansi pa
funso lililonse.
BANJA LA A CHITHODWE
Mu mudzi wina mudali banja la a Chithodwe. Bambo ndi mayi Chithodwe adali alimi. Tsiku lina a
Chithodwe adali kukambirana ndi akazi awo nkhani zaulimi wathonje. A Chithodwe adati,” Amake
Kantchowa, nkhanga zidapangana kusanapse. Mudaona muja anzanthu adaphera makobiri ndi thonje
chaka chatha. Nane ndaganiza zoti chaka chino ndilime thonje. Ndifuna kuti ndigule mbuzi ndikagulitsa
thonjeli.”
“Bambo, mwaganiza mozama. Tilimedi thonje ndipo tikagula mbuzizo mbusa wake akhala Mwamadi,
chisamba chathuchi,” adatero mayi Chithodwe.
“Ayi, pokhapo tisemphana Chichewa. Mwamadi sangabuse mbuzi chifukwa ndi wofuntha zedi. Ufuna
kuti mwana wakoyu andithyolere mbuzi zanga miyendo?”
“Nanga awete mbuzizo ndani? Ngati mwaganiza zoti aphwanu ndiwo awete mbuzizo apo mwalemba
m’madzi. Mwamadi aweta basi chifukwa chumachi ndi chake.”
Awiriwo adapsetsana mtima kwambiri moti adayamba kukangana kenako adagwirana m’thupi.
Bamboo Chithodwe amangoti, “Sindifuna kuti Mwamadi andithyolere mbuzi zanga miyendo.
Akazi awo amangoti, “Awetabe chifukwa chumachi ndi chake.”
Kenaka awiriwo adayamba kumenyana kwambiri.
Page 3 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
Anansi awo atamva phokoso ndi mfuwu, adakhamukira kunyumbako ndipo adalanditsa ndewu ija.
Anansiwo adawakhazika pansi a Chithodwe ndi akazi awo ndipo adawafunsa kuti afotokoze chomwe
chidautsa mapiri pa chigwa.
Bamboo Chithodwe adangoyankha moduduka nati, “Sindifuna kuti Mwamadi andithyolere mbuzi
zanga miyendo.”
Anansi aja adazizwa kwambiri ndi mawu a bamboo Chithodwe chifukwa banjalo lidalibe ngakhale
chikopa cha mbuzi.
Mayi Chithodwe adafotokoza mwatsatanetsatane chomwe chidachitika kuti awiriwo alongozane.
“Bambowa agula mbereko mwana asanabadwe. Ati akuti alime thonje ndipo akagulitsa thonjelo agule
mbuzi. Ati Mwamadi sadzabusako mbuzizo chifukwa ndi wofuntha; ndiye ine poti aa! Mwana wathu
asadzaweteko mbuzizo ngati si zake, basitu chinkhondo n’kuyambika. Ndipo tatchayanadi,” mayiwo
adatero.
Anansi aja atamva nkhaniyo adafa ndi phwete. Iwo adalidzudzula banjalo chifukwa chokangana ndi
kumenyana popanda mfundo yeniyeni.
(Nkhaniyi idalembedwa ndi William V.C. Lwanda ndipo ili mu buku la Nsinjiro za chiyankhulo.)
MAFUNSO
a. Kodi Mwamadi adali yani?
_____________________________________________________________________(malikisi 1)
b. “Awetabe chifukwa chumachi ndi chake.” Kodi chuma chinkanenedwacho chidali kuti?
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
c. Kodi bambo ndi mayi Chithodwe akadachitanji kuti asakangane?
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________(Malikisi 2)
d. Fotokozani phunziro lalikulu lomwe likupezeka mu nkhaniyi.
Page 4 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________(Malikisi 2)
e. Perekani matanthauzo a mawu otsatirawa:
i. Adaphera makobiri
_____________________________________________________________________(Malikisi 2)
ii. Mwalemba m’madzi
_____________________________________________________________________(Malikisi 2)
iii. Adagwirana m’thupi
_____________________________________________________________________(Malikisi 2)
f. Chinachititsa anansi awo athamangire ku nyumba kwa a Chithodwe chiyani?
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
g. Pezani mkuluwiko umodzi nkhaniyi.
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
h. Tchulani njira zitatu zomwe mungatsate pofuna kuthetsa mkangano pakati panu.
a. ___________________________________________________________________________
_________________________________________________________________ (Malikisi 2)
b. ___________________________________________________________________________
_________________________________________________________________ (Malikisi 2)
c. ___________________________________________________________________________
_________________________________________________________________ (Malikisi 2)
GAWO B (Malikisi 20)
NKHANI ZA MCHEZO NDI ZOLEMBEDWA
2. Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala ndipo muyankhe mafunso otsatirawo pa mizere ili pansi pa
funso lililonse.
Page 5 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
MUNTHU WA MULUNGU (DYSON GONTHI)
Mtauni ina yake mumakhala munthu wa Mulungu, munthu ameneyu ntchito ina yomwe amagwira idali
yogulitsa zovala ndipo pa chifukwa ichi adali ndi ndalama zambiri. Iyeyu adalinso wokonda kupereka
chuma chake ku ntchito ya Mulungu. Mkulu ameneyu ngakhale adali wopemphera sanali kukhulupirira
wina aliyense kotero ndalama zake samasungitsa munthu wina koma amasunga yekha. Wina mwa
anthu omwe amakhala nawo adali Juni. Iyeyu nthawi zambiri amasilila ndalamazo ndipo amafunafuna
njira ya m’mene angazitengere ndalama za munthu wa Mulunguyo. Chomwe iye adachikonza
ndikukhala mtumiki wake ndikuonetsa kukhulupirika kwake konse ndi cholinga choti tsiku lina
adzamusungitse ndalamazo akadzayamba kumukhulupirira.
Tsiku lina atakonza chinyengo chakecho, adafika kwa munthu wa Mulunguyo ndi kufotokoza nkhawa
zake zonse ndi kuti iye akufuna kutumikira Mulungu za dziko lapansi alibe nazo kanthu, pakuti adati
iye afuna kudzakhala m’modzi mwa anthu oyera mtima okalowa nawo mu ufumu wa Mulungu.
Munthu wa Mulungu adati ndi odala iyeyo chifukwa siambiri achinyamata amathamangira ntchito ya
Mulungu. Mnyamata Juni adauza kapolo wa Mulungu kuti amulandire ndikumudzoza pa ntchito
yotumikira Yehova. Mkuluyo adamudzozadi mnyamatayo ndi kutsimikiza zogwira naye ntchito
komanso munthu wopempherayo adauza mnyamatayo kuti azigona nyumba imodzi kuti usiku
ikakwana nthawi yopemphera azipempherera limodzi. Juni adachita chilichonse chomukondweretsa
munthu wa Mulungu. Koma ngakhale zinali choncho, munthu wopempherayo anali kusunga yekha
ndalama zakezo. Tsiku lina kudabwera uthenga woitana munthu wa Mulungu ku phwando lomwe
adakonza kumudzi wina wake. Mkuluyo ndi mnyamata wake Juni adapitadi ku phwandoko. Koma ali
pa ulendo asadafike pa njira adapeza mtsinje. Munthuyo ataona madziwo mtima wopemphera pa
madziwo udamubwerera ndiye adatenga ndalama zakezo mkukulunga mu chikuto cha pepala cha
pulasitiki kuti ndalama zisanyowe koma kenaka adaganiza zomusungitsa Juni. Juni adalandira, ndipo
kapolo wa Mulunguyo adalowa m’madzimo. Atamaliza kupemphera ndikuvuukamo m’madzimo
adaona kuti mnyamata uja wapita nazo ndalama zija.
Mkuluyo adayesetsa kumuunguza osamuona kuyesa kuitana popanda wovomera ndipo anadandaula
kuti basi ndalama zake zapita. Munthu wa Mulungu adadzazindikira kuti mnyamata uja adali wa
Page 6 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
chinyengo mtima mwake udali ku ndalama. Munthuyo sadapitenso ku phwando kuja adabwerera uku
akulira.
Mafunso
a. Fotokozani m’mene munthu wa Mulunguyu amapatira chuma chake.
______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________ (Malikisi 1)
b. Kodi ndi chifukwa chiyani amasunga yekha ndalama zake?
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
c. Perekani kuopsa kosunga wekha ndalama.
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________ (Malikisi 1)
d. Tchulani ma banki atatu amene akupezeka kuno kwathu ku Malawi.
(i) _______________________________________________________________ (Malikisi 1)
(ii) _______________________________________________________________ (Malikisi 1)
(iii) _______________________________________________________________ (Malikisi 1)
e. Chifukwa chiyani kuli koyenera kusunga ndalama ku banki?
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
f. Fotokozani pa mpondachimera pa nkhaniyi.
______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________ (Malikisi 2)
g. Perekani phunziro lomwe mwapeza mu nkhaniyi.
______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
_____________________________________________________________________ (Malikisi 1)
Page 7 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
3. Werengani ndakatulo ili m’munsiyi ndipo muyankhe mafunso otsatirawo pa mizere ili pansi pa funso
lililonse.
NSANAMIRAKANDE (MACKENZIE T. NDEBELE)
Mnzako akalumala usamamseke,
Mawa udzaseka iwe.
Wanga mlomo si dama nchilema.
Pa lansolo gabi mdanyinda.
Mwa njobvu sapita kawiri.
Khwangwala wamantha,
Adafa ndi ukalamba.
Pamadzi sindisenderapo,
M’chitsime ndiopa ndingadzagwere.
Kumadzi toto, koma kulikande.
Pachulu sindingakadamirepo,
Ndiona ana a mbuzi ku8:00-9:45 amkwerakwera.
Kumwamba sindingagadamireko,
Khosi toto ngadzakhobole.
Kusamala moyo suchitsiru.
Anthu opanda nzeru andisinjirira
Nanditcha, ‘sakwerapachulu.’
Achipongwe ana anditcha,
‘Sayang’ana kumwamba zyolizyoli.’
Uwutu ananu ndi mtudzu!
Panyerenyetsa kanda sutchisi,
Adatero akulu.
Dzanja ndili nalo,
Page 8 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
Koma Chauta ngwanjiru
Adandipatsa kachidutswa.
Nsanamira kande nkulipira matope.
MAFUNSO
1. Kodi akuyankhula m’ndakatuloyi ndani?
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
2. Nanga akuyankhula kwa yani?
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
3. Tsimikizani kuti oyankhulayo akusonyeza mtafu.
______________________________________________________________________________
______________________________________________________________________________
____________________________________________________________________(Malilkisi 2)
4. Pezani zipangizo ziwiri zomwe mlembi wagwiritsa ntchito m’ndakatuloyi ndipo pachipangizo
chilichonse mupereke chitsanzo chimodzi.
a. Chipangizo: ________________________________________________________(Malikisi 1)
Chitsanzo: _________________________________________________________(Malikisi 1)
b. Chipangizo: ________________________________________________________(Malikisi 1)
Chitsanzo: _________________________________________________________(Malikisi 1)
5. Lembani kamvekedwe ka ndakatuloyi.
_____________________________________________________________________ (Malikisi 1)
6. Perekani dzina lina la mawu awa: ‘Nsanamirakande.’
_____________________________________________________________________(Malikisi 1)
GAWO C (MALIKISI 10)
4. Masulirani kandime kankhani kali m’munsika m’Chichewa chomveka bwino.
Heavy rains which have been falling in some parts of Malawi for the past three weeks have caused loss
of life and damage of property in Dowa and Dedza districts.
_________________________________________________________________________________

Page 9 of 9
DZINA_________________________________________________________________________________
_________________________________________________________________________________
_________________________________________________________________________________
_________________________________________________________________________________
_________________________________________________________________________________
_________________________________________________________________________________
_______________________________________________________________________(Malikisi 5)
5. Fupikitsani kankhani kali m’munsika kuti kakhale ndi mawu osachepera 27 ndipo asapitirire 30.
Kulemba ana aang’ono ntchito ili yonse, kaya ya m’nyumba, kaya yogulitsa malonda, kaya yolima
m’munda ngakhale m’maesiteti ndi nkhanza yayikulu kwambiri kwa anawo. Nthawi yomwe anawo
amakhala akukangalika ndi kugwira ntchito yomwe tawapatsayo anzawo anthanga yawo amakhala
akuphunzira. Choncho, ufulu wawo wophunzira umakhala ukuphwanyidwa. Tikuyenera tonse
mogwirizana kuwonetsetsa kuti ufulu wa mwana aliyense ukutetezedwa posawalemba ntchito anawo
akadali aang’ono.

________________________________________________________________________(Malikisi 5)
MAFUNSO ATHERA PANO