NORTHERN EDUCATION DIVISION
2024 MALAWI SCHOOL CERTIFICATE OF EDUCATION MOCK EXAMINATION
CHICHEWA
Subject number: M032/II
Tuesday, 26 March Time allowed: 2hrs
1:00 – 3:00 pm
PAPER II
(Malikisi 90)
Malangizo:
1. Onetsetsani kuti pepala ili lili ndi
Funso Chongani Muno
masamba khumi ndi atatu.
funso ngati musalembemo
mwayankha.
2. Pepalali lili ndi magawo anayi: A, B, C ndi D.
1
3. Lembani dzina lanu pamwamba pamwamba pa
2
tsamba lililonse la pepalali.
3
4. Muchitebulo chili pambalichi, onetsani funso
4
lililonse lomwe mwayankha pochonga mubokosi
lomwe lili kutsogolo kwake. 5
6
5. Perekani pepalali kwa oyang’anira mayeso
nthawi ikakwana. 7
Total
Page 1 of 13
Gawo A (Malikisi 40)
MALAMULO ACHIYANKHULO
Langizo: Yankhani mafunso onse m’gawo ili pa mizere ili pansi pa funso
lililonse.
1. a. Perekani zazimuna za mayina ali m’munsimu
(i) msoti
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) mkota
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) chumba
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iv) nkhosa
______________________________________________________
(Malikisi 1)
b. Fotokozani momwe aonjezi ali ndi mnzere kunsi kwawo m’ziganizo
zotsatirazi adapandidwira:
(i) Iye anamwa mowa mwachabe.
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
Page 2 of 13
(ii) Abambo aja anagwa chagada.
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
(iii) Ndalama ija abisa pansalu.
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
2. a. Lembani ntchito za akapandamneni otsatirawa:
(i) Mnzanga watenga buku la aphunzitsi.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Iwo amagula chimanga chachiwisi.
_____________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Wakhala akujomba kwa miyezi iwiri.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iv) Adagula nyumba yokongola kwambiri.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
b. Pangani ziganizo zitatu ndi ‘li’ kusonyeza ntchito zotsatirazi:
(i) kukhala mgwirizanitsi wamchitidwantchito
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
(ii) kukhala tsinde la mneni
Page 3 of 13
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
(iii) kukhala mphatikiramtsogolo woloza
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
3. a. Perekani mitundu ya masinde omwe atsekedwa mzere kunsi kwawo
m’ziganizo zotsatirazi:
(i) Mwana uyo akuphunzira kuyenda.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Mutu wanga ukuwawa.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Abwana ako amakukonda.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iv) Mupita liti kumunda?
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(v) Mnyamata wamtali wasochera.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
b. Kodi mawu awa anachokera ku ziyankhulo ziti?
(i) sawatcha
______________________________________________________
(Malikisi 1)
Page 4 of 13
(ii) muti
______________________________________________________
(Malikisi 1)
c. Tchulani mitundu ya agwirizanitsi omwe ali ndi mzere kunsi kwawo
m’ziganizo zotsatirazi:
(i) Munthu yemwe wadya phala langa ali kuti?
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Mwana wanu wakalipiridwa.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Anthuwa awupeza mtendere.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
4. a. Kodi aneni ali ndi mizere kunsi kwawo ali mkanenedwe kanji?
(i) Amayi aphika ndiwo zokoma zedi
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Gona, upumule
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Ndilembe bwanji zinthu izi?
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iv) Ndipita akabwera.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(v) Kazipitani kwanu.
______________________________________________________
Page 5 of 13
(Malikisi 1)
b. Lembani ntchito za mayina omwe ali ndi mzere kunsi kwawo
(i) Amayi amupatsa malaya Jefuta
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Chisomo ndi mwana wabwino
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Wapita ku chipatala ndi mnzake
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iv) Alinafe wapita ku Blantyre.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(v) Ona mikango, mwanawe.
______________________________________________________
(Malikisi 1)
Gawo B (Malikisi 20 )
Kumvetsa Nkhani Ndi Kusanthula Chiyankhulo
5. Werengani nkhani ili m’munsiyi mosamala ndipo muyankhe mafunso
otsatirawa pa mizere ili pansi pa funso lililonse.
‘Ayi ndithu makono kwaipadi, munthu akuopa munthu mnzake osati chilombo
chakuthengo’. Uku kudali kudandaula kwa bambo Kachigwada akulonjerana
Page 6 of 13
ndi a Chimwendo. Aliyense wa anthu awiriwa adali atalawirira kupita ku dimba
kukakupa kukonzekeratu kuti nthawi ikakwana adzabzalemo nyemba. Nthawiyi
n’kuti a Chimwendo atawafototokozera a Kachigwada za maliro omwe adali
atachitika pamudzi wina wake wapafupi ndi wawowo. Iwo adati munthuyo
adachita kuphedwa atapita kukanena za matenda.
‘Kodi mukuti chenicheni chidatsitsa dzaye kuti njovu ithyoke mnyanga
n’chiyani? Ndiye kuti munthuyo adaputana nawo a chifwambawo?’ Adafunsa
modabwa a Kachigwada uku akutulutsa gwati la fodya m’thumba la jasi.
‘Ayi tere, n’zomwe mwanena kale kuti masiku ano kwaipa, zinthu sizili bwino
m’pang’ono pomwe. Munthuyo adali atatumidwa ku Phokera kukapereka
uthenga wa matenda a mtengwa wina wam’mudzimo ndiye kudam’dera panjira.
Ngakhale kudali kutada iye adapitirira ndi ulendo wake, poti mphuno salota,
osadziwa kuti kulinji. Ali pafupi kufika, ndi pamene adakumana ndi tsokali.
Achifwamba adamlanda njinga, ndalama, zovala ndi kumupha. Amene
adampeza ndi anthu opita ku msika dzana, ali mbambamba panjira ndiponso ali
buno bwamuswe. Manong’onong’o a anthu akuti adachita zimenezo ndi
anyamata a m’mudzi momwe amapita munthuyo.’
Kodi cholinga chawo chidali chiyani?
‘Kodi mwaiwala kuti m’mudzi mmene muja muli malova ambirimbiri. Iwo
safuna konse kulima kapena kuchita geni ngati mmene achitira anzawo m’midzi
ina koma kukhazira anthu basi.’
‘A! A! A! Nanunso a chimwendo musatero, Moti munthu kuleka kugona
n’kumakafa n’chisanu chifukwa chofuna kulanda katundu wa ena panjira?’
‘Ndi zimemenezotu anthuni, ulova ngosavuta ndiye poti kalowa m’malaya
sasankha amagwira aliyense ndiye malovawa njira yachidule yopezera zosowa
zawo ndikulanda za eni basi.’
Page 7 of 13
‘Gwero lalikulu lomwe limachepetsa chitetezo ndi ulova chifukwa kukadakhala
kuti anthuwa ali ndi zochita, bwenzi zoterezi kulibe.’
‘Malova nthawi zambiri akakumana amataya nthawi yawo kukambirana za
zomwe angachite usiku m’malo mokambirana zinthu zaphindu.’
‘Kodi mwatero a Chimwendo? Ine ndikuona kuti ndi nkhanza basi osati china
ayi.’
‘Nanunso a Kachigwada musamanena ngati nthumbidwa. Tsono mumati
akapanda kutero azikadyanji? Pakhomo palibe nkhokwe koma ali ndi banja
ndiye atani? Iye akasowa pogwira, njira yachidule ndi umbanda kuti apeze
zosowa zake.’
‘Ndiye tsono zikatere nanga tiziyenda bwanji? Adadandaula a Kachigwada. Iwo
adafotokoza kuti adamvanso kuti m’tawuni ndiye mudanyanya chifukwa muli
malova ambiri moti anthu amawaliritsa dzuwa likuswa mtengo. Ambiri amene
amapita m’tawuni kukagula zinthu amabwerako manja ali m’khosi
atawakwangwanula ndalama zonse anthu amene amakhala akuyendayenda
kusowa chochita. Pothirira ndemanga a Chimwendo adati ndi zomvetsa chisoni
kuti malova amachepetsadi chitetezo. Anthu ena amavutika kugwira ntchito
mwina yolima koma akakolola zinthu zija zimabedwa nthawi imodzi kumusiya
mwini wakeyo paumphawi.
A Kachigwada adati, ‘Ayi bwanawe takambapo, zamalirozo ndamva koma
ndiyambe ndakupapo pang’ono. Tikumana msana buno kumaliroko.’ Aliyense
adapita kudimba lake.
Tsopano yankhani mafunso otsatirawa m’ziganizo zomveka bwino.
a. (i) Kodi a Chimwendo amalonjerana ndi ndani?
Page 8 of 13
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) Ndi chifukwa ninji anthu awiriwa adalawirira?
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
(iii) Kodi wotumidwa amakatani ku Phokera?
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) Tchulani zinthu ziwiri zomwe zidalandidwa kwa munthu
wotumidwa ku Phokera?
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
(iv) Tsimikizani kuti anyamata ochokera m’mudzi mwa munthu yemwe
adaphedwa anali achifwamba.
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
(v) Tchulani zinthu ziwiri kuchokera m’nkhaniyi zomwe anyamata
akanamachita kuti atukule miyoyo yawo
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
Page 9 of 13
(vi) Kodi ndi chifukwa chiyani anyamata a mmudzi wa Phokera
amachita za uchifwamba?
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
(vii) Perekani tanthauzo la mkuluwiko woti “umanena chatsitsa dzaye
kuti njovu ithyoke mnyanga”.
______________________________________________________
______________________________________________________
(Malikisi 2)
b. Pezani mawu m’nkhaniyi omwe akutsutsana m’matanthauzo ndi awa:
(i) kale
______________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) mkamwini
______________________________________________
(Malikisi 1)
(iii) ndi kutentha
______________________________________________
(Malikisi 1)
c. Pezani zining’a m’nkhaniyi zomwe matanthauzo ake ndi awa:
(i) masana
______________________________________________________
(Malikisi 1)
(ii) kusadziwa
______________________________________________________
(Malikisi 1)
Page 10 of 13
(iii) akudandaula
______________________________________________________
(Malikisi 1)
Gawo C (Malaikisi 15)
Chifupikitso
6. Werengani nkhani yotsatirayi mosamala. Ili ndi mawu 171 ndipo
muyifupikitse kuti ikhale ndi mawu osachepera 50 koma asapitirire 60
Masiku ano nkhani ya ufulu wa achinyamata ili mkamwamkamwa. Amabungwe
ndiwo nkhaniyi ali nayo chire. Akulimbikitsa maufulu monga a kavalidwe,
akuyankhula zakukhosi ndi maphunziro.Achinyamata ali ndi ufulu
wakavalidwe. Ngakhale ufuluwo ulipo koma mwina mwambo wa mtundu wa
anthu wina umaletsa kavalidwe kena.
Chifukwa cha chimenechi, achinyamata ena akuonjeza kwambiri masiku ano
ndipo zambiri akumazitenga mu kanema. Atsikana akuvala zovala zazing’ono
kwambiri zomwe zikuonetsa ziwalo zobisika monga tchafu. Ena akuvala ma
thalauza ogwira thupi ong’ambikang’ambika komanso onyosoka mu mawondo
kuonetsa thupi. Atsikana otere akafika pofuna banja nthawi zambiri
samalipeza.M’sukulu aphunzitsi ali pa ntchito yaikulu kuonetsetsa kuti mwana
aliyense wavala zovala zovomerezeka. Komabe pamapezeka kuti ophunzira ena
avala yunifolomu yothina pena yayifupi kwambiri. Ndipo ena amabwera ali mu
ndekesha zosaloledwa konse pasukulu.
Ena amafuna kuti azicheza momwe akufunira ati ali ndi ufulu woyankhula ndi
wocheza. Ndipo samadziwa poyenera kukhala chete. Ena amayankhulanabe
ngakhale aphunzitsi ali m’kalasi ndipo ena akapalamula nachotsedwa sukulu,
Page 11 of 13
amanena kuti sangachoke pasukulupo chifukwa ali ndi ufulu wophunzira.
Amayiwala kuti ufuluwo ulipodi koma umayenda limodzi ndi udindo wosunga
malamulo.
________________________________________________________________

Gawo D (Malikisi 15)
Chimasuliro
7. Masulirani nkhani yotsatirayi m’chichewa chomveka bwino.
HYGIENE
Many people become ill because they have eaten food which has gone
bad or has been infected by germs. There are various ways in which we
can prevent food poisoning, and make sure that food is safe to eat.
Page 12 of 13
The first rules we should remember concern people’s personal habits. It is
very important that when we eat our hands are clean. It is even more
important that people who are preparing food for others to eat have clean
hands. Secondly, people should make sure that they do not sneeze or
cough over food. Sneezing and coughing spread germs, and if these land
on food, they will be passed on to the person eating the food.

MAFUNSO ATHERA PANO
NB: Pepala ili lili ndi masamba osindikizidwa khumi ndi atatu.
Page 13 of 13